Kalata Yoyamba ya Petulo 1:1-25

  • Moni (1, 2)

  • Kubadwanso mwatsopano nʼkukhala ndi chiyembekezo chodalirika (3-12)

  • Mukhale oyera monga ana omvera (13-25)

1  Ine Petulo mtumwi+ wa Yesu Khristu, ndikulembera inu osankhidwa ndi Mulungu, amene muli alendo mʼdzikoli, omwe mwamwazikana ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya,+ Asia ndi Bituniya.  Ndikulembera inu amene Mulungu Atate+ anadziwiratu za inu. Iye anakupatsani mzimu wake kuti mukhale oyera.+ Anachita zimenezi kuti mukhale omvera komanso kuti akuyeretseni ndi magazi a Yesu Khristu.+ Ndikupempha Mulungu kuti akusonyezeni chifundo chake chachikulu komanso kuti mukhale ndi mtendere.  Atamandike Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, yemwenso ndi Atate wake. Mulungu anatisonyeza chifundo chachikulu pamene anachititsa kuti tibadwenso mwatsopano+ nʼkukhala ndi chiyembekezo chodalirika.+ Zimenezi zinatheka chifukwa cha kuukitsidwa kwa Yesu Khristu.+  Anachititsa kuti tibadwenso mwatsopano kuti tikhale ndi cholowa chosawonongeka, chosadetsedwa ndiponso chosasuluka.+ Cholowa chimenechi anakusungirani kumwamba.+  Anasungira inuyo amene Mulungu akukutetezani ndi mphamvu yake chifukwa muli ndi chikhulupiriro. Mulungu akukutetezani kuti mudzalandire chipulumutso, ndipo chipulumutso chimenechi chidzaonekera munthawi yamapeto.  Pa chifukwa chimenechi, mukusangalala kwambiri ngakhale kuti panopa nʼkoyenera kuti muvutike kwa kanthawi chifukwa cha mayesero osiyanasiyana+ amene mukukumana nawo.  Zimenezi zikukuchitikirani kuti chikhulupiriro chanu chidzachititse kuti mutamandidwe ndiponso kulandira ulemerero ndi ulemu, Yesu Khristu akadzaonekera.*+ Chikhulupiriro chanucho chayesedwa+ ndipo ndi chamtengo wapatali kuposa golide amene amawonongekabe ngakhale kuti anadutsa pamoto.  Ngakhale kuti Khristuyo simunamuonepo, mumamukonda. Ngakhale simukumuona panopa, mumamukhulupirira ndipo mukusangalala kwambiri ndi chimwemwe chodzaza tsaya,  popeza ndinu otsimikiza kuti chikhulupiriro chanu chidzachititsa kuti mupulumuke.+ 10  Aneneri amene analosera za kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu anakusonyezani, anafufuza za chipulumutso chimenechi mwakhama ndiponso mosamala kwambiri.+ 11  Mzimu woyera unali utaneneratu kuti Khristu+ adzavutika ndipo kenako adzalandira ulemerero. Aneneri ankafufuza zizindikiro zimene mzimu woyera* unawasonyeza zokhudza nthawi yeniyeni komanso nyengo imene zimenezi zidzachitike.+ 12  Mulungu anauza aneneriwo kuti sankadzitumikira okha, koma ankatumikira inuyo. Tsopano zinthu zimenezi zaululidwa ndi anthu omwe akulengeza uthenga wabwino kwa inu mothandizidwa ndi mzimu woyera wochokera kumwamba.+ Angelo amafunitsitsa atamvetsa zinthu zimenezi. 13  Choncho konzekeretsani maganizo anu kuti mugwire ntchito mwamphamvu.+ Mukhalebe oganiza bwino+ ndipo muziyembekezera ndi mtima wonse kukoma mtima kwakukulu kumene adzakusonyezeni, Yesu Khristu akadzaonekera.* 14  Monga ana omvera, siyani kuchita zinthu motsatira zimene munkalakalaka musanadziwe Mulungu. 15  Koma mofanana ndi Woyera amene anakuitanani, inunso khalani oyera mʼmakhalidwe anu onse,+ 16  chifukwa Malemba amati: “Mukhale oyera, chifukwa ine ndine woyera.”+ 17  Ndiponso ngati mukupempha zinthu kwa Atate, amene amaweruza mopanda tsankho+ mogwirizana ndi zimene aliyense amachita, muzichita zinthu zosonyeza kuti mumaopa Mulungu+ pamene mukukhala mʼdzikoli monga alendo. 18  Mukudziwa inu kuti zinthu zimene zinakumasulani*+ ku moyo wanu wopanda phindu umene munatengera kuchokera kwa makolo anu, sizinali zinthu zotha kuwonongeka monga siliva kapena golide. 19  Koma munamasulidwa ndi magazi amtengo wapatali+ a Khristu,+ omwe ndi ofanana ndi magazi a nkhosa yopanda chilema komanso yopanda mawanga.+ 20  Zoonadi, Mulungu anasankhiratu Khristu anthu asanayambe kuberekana padziko lapansi,+ koma anaonekera pa nthawi yamapeto chifukwa cha inuyo.+ 21  Kudzera mwa iye, mukukhulupirira Mulungu+ amene anamuukitsa kwa akufa+ ndi kumupatsa ulemerero,+ nʼcholinga choti chikhulupiriro ndiponso chiyembekezo chanu zikhale mwa Mulungu. 22  Popeza mwadziyeretsa pokhala omvera choonadi cha mʼMawu a Mulungu ndipo tsopano mumakonda abale mopanda chinyengo,+ muzikondana kwambiri kuchokera mumtima.+ 23  Inuyo mwabadwanso mwatsopano+ kudzera mʼmawu a Mulungu+ wamoyo ndi wamuyaya. Simunabadwe kuchokera mumbewu yoti ikhoza kuwonongeka, koma mumbewu yomwe singawonongeke.+ 24  Pakuti “anthu onse ali ngati udzu, ndipo ulemerero wawo wonse uli ngati duwa lakutchire. Udzu umafota ndipo duwa limathothoka, 25  koma mawu a Yehova* adzakhalapo mpaka kalekale.”+ “Mawu” amenewa ndi uthenga wabwino umene unalengezedwa kwa inu.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “akadzaululika.”
Kapena kuti, “mzimu woyera umene unali mwa iwo.”
Onani mawu amʼmunsi pavesi 7.
Mʼchilankhulo choyambirira, “zinakuwombolani.”