2 Mafumu 16:1-20

  • Ahazi, mfumu ya Yuda (1-6)

  • Ahazi anapereka ziphuphu kwa Asuri (7-9)

  • Ahazi anatengera mapulani a guwa la mulungu wonama (10-18)

  • Imfa ya Ahazi (19, 20)

16  Ahazi+ mwana wa Yotamu mfumu ya Yuda anakhala mfumu mʼchaka cha 17 cha Peka mwana wa Remaliya.  Ahazi anayamba kulamulira ali ndi zaka 20 ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 16. Iye sanachite zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wake ngati mmene anachitira Davide kholo lake.+  Anayenda mʼnjira ya mafumu a Isiraeli+ ndipo anafika mpaka potentha* pamoto mwana wake wamwamuna,+ potsatira zinthu zonyansa zimene anthu a mitundu ina ankachita+ amene Yehova anawathamangitsa pamaso pa Aisiraeli.  Ahazi ankapereka nsembe zautsi komanso nsembe zina pamalo okwezeka,+ pamapiri ndiponso pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba obiriwira.+  Pa nthawiyi mʼpamene Rezini mfumu ya Siriya ndi Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Isiraeli, anapita kukamenyana ndi anthu amumzinda wa Yerusalemu.+ Anazungulira mzindawu, womwe Ahazi ankakhala, koma sanathe kuulanda.  Pa nthawiyo, Rezini mfumu ya Siriya analanda mzinda wa Elati+ nʼkuubwezera kwa Aedomu. Kenako anathamangitsa Ayuda mumzinda wa Elati ndipo Aedomu anayamba kukhala mumzindawu moti adakali momwemo mpaka lero.  Choncho Ahazi anatumiza uthenga kwa Tigilati-pilesere+ mfumu ya Asuri wakuti: “Ndine mtumiki wanu ndiponso mwana wanu. Bwerani mudzandipulumutse mʼmanja mwa mfumu ya Siriya ndi mʼmanja mwa mfumu ya Isiraeli, amene akundiukira.”  Kenako Ahazi anatenga siliva ndi golide wapanyumba ya Yehova ndiponso wochokera mʼnyumba ya mfumu nʼkutumiza kwa mfumu ya Asuri ngati chiphuphu.+  Mfumu ya Asuri inamvera pempho lake ndipo inapita ku Damasiko nʼkukalanda mzindawo. Anthu amumzindawo inawagwira nʼkupita nawo ku Kiri+ ndipo Rezini inamupha.+ 10  Kenako Mfumu Ahazi anapita kukakumana ndi Tigilati-pilesere mfumu ya Asuri ku Damasiko. Kumeneko anaonako guwa lansembe, choncho Mfumu Ahazi anatumizira wansembe Uliya pulani ya guwalo.+ 11  Wansembe Uliya+ anamanga guwalo+ mogwirizana ndi malangizo onse amene Mfumu Ahazi anamutumizira ali ku Damasiko. Wansembe Uliya anamaliza kumanga guwalo Mfumu Ahazi asanabwere kuchokera ku Damasiko. 12  Mfumuyo itabwerako ku Damasiko, nʼkuona guwa lansembelo, inapita kukaperekapo nsembe.+ 13  Paguwapo, mfumuyo inapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zambewu. Inathiraponso nsembe zachakumwa ndiponso kuwazapo magazi a nsembe zake zamgwirizano. 14  Kenako Ahazi anachotsa guwa lansembe lakopa*+ limene linali pamaso pa Yehova, kutsogolo kwa nyumbayo. Analichotsa pakati pa guwa lake lansembe ndi nyumba ya Yehova nʼkuliika kumpoto kwa guwa lakelo. 15  Ndiyeno Mfumu Ahazi analamula wansembe Uliya+ kuti: “Paguwa lansembe lalikululi uziwotchapo nsembe yopsereza yamʼmawa,+ nsembe yambewu yamadzulo,+ nsembe yopsereza ya mfumu ndi nsembe yake yambewu. Uziwotchaponso nsembe zopsereza za anthu onse amʼdzikoli, nsembe zawo zambewu ndiponso nsembe zawo zachakumwa. Komanso uziwaza paguwali magazi onse a nsembe yopsereza ndi magazi onse a nsembe zina. Koma guwa lansembe lakopalo, ndiona chochita nalo.” 16  Wansembe Uliya anachita zonse zimene Mfumu Ahazi analamula.+ 17  Kuwonjezera apo, Mfumu Ahazi anaduladula malata a mʼmbali mwa zotengera zokhala ndi mawilo+ nʼkuchotsa mabeseni pamwamba pa zotengerazo.+ Thanki yosungira madzi anaichotsa pamwamba pa ngʼombe zamphongo zakopa+ nʼkuiika pansi pomanga ndi miyala.+ 18  Mfumuyo inachotsa chinthu chokhala ndi denga chogwiritsa ntchito pa Sabata chimene anachimanga mʼnyumba ya Yehova ndipo inatsekanso khomo lakunja limene mfumu inkalowera mʼnyumbayo. Inachita zimenezi chifukwa cha mfumu ya Asuri. 19  Nkhani zina zokhudza Ahazi ndiponso zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda.+ 20  Kenako Ahazi, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda a makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndiyeno mwana wake Hezekiya* anakhala mfumu mʼmalo mwake.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Anamudutsitsa pamoto.”
Kapena kuti, “lamkuwa.”
Kutanthauza, “Yehova Amapatsa Mphamvu.”