Kalata yachiwiri yopita kwa Timoteyo 3:1-17

  • Masiku otsiriza adzakhala nthawi yovuta (1-7)

  • Kutsatira chitsanzo cha Paulo (8-13)

  • “Pitiriza kutsatira zimene unaphunzira” (14-17)

    • Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu (16)

3  Koma dziwa kuti masiku otsiriza+ adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta.  Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika,  osakonda achibale awo, osafuna kugwirizana ndi ena, onenera ena zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino,  ochitira anzawo zoipa, osamva za ena, odzitukumula chifukwa cha kunyada, okonda zosangalatsa mʼmalo mokonda Mulungu,  ndiponso ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma amakana kuti mphamvu ya kudziperekako iwasinthe.+ Anthu amenewa uziwapewa.  Ena mwa anthuwa amalowerera mozemba mʼmabanja nʼkumachititsa amayi ena kuti akhale akapolo awo. Amayiwa amakhala ofooka chifukwa cha machimo awo ndiponso otengeka ndi zilakolako zosiyanasiyana.  Nthawi zonse amaphunzira, koma satha kudziwa choonadi molondola.  Mofanana ndi Yane ndi Yambure, amene anatsutsa Mose, anthu amenewanso akupitiriza kutsutsa choonadi. Iwo ali ndi maganizo opotoka kwambiri, ndipo sakuyenerera chikhulupirirochi.  Koma sangapite patali, chifukwa kupusa kwawo kuonekera bwino kwa anthu onse, ngati mmene zinakhalira ndi anthu awiri aja.+ 10  Koma iwe wayesetsa kutsatira zimene ndimaphunzitsa, moyo wanga,+ cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa ndi kupirira kwanga. 11  Ukudziwanso mmene ndinazunzikira komanso masautso amene ndinakumana nawo ku Antiokeya,+ ku Ikoniyo+ ndi ku Lusitara.+ Komabe ndinapirira ndipo Ambuye anandipulumutsa ku zonsezi.+ 12  Pajatu onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mogwirizana ndi Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.+ 13  Koma anthu oipa ndi achinyengo adzaipiraipirabe. Iwo azidzasocheretsa ena ndiponso azidzasocheretsedwa.+ 14  Koma iwe, pitiriza kutsatira zimene unaphunzira ndi zimene unakhulupirira pambuyo pokhutira nazo,+ chifukwa ukudziwa amene anakuphunzitsa. 15  Kuyambira pamene unali wakhanda,+ wadziwa malemba oyera+ amene angakupatse nzeru zokuthandiza kuti udzapulumuke chifukwa chokhulupirira Khristu Yesu.+ 16  Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu,+ ndipo ndi othandiza pophunzitsa,+ kudzudzula, kukonza zinthu ndi kulangiza mwachilungamo,+ 17  kuti munthu wa Mulungu akhale woyenerera kwambiri ndi wokonzeka mokwanira kugwira ntchito iliyonse yabwino.

Mawu a M'munsi