Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira 19:1-21

  • Tamandani Ya chifukwa cha ziweruzo zake (1-10)

    • Ukwati wa Mwanawankhosa (7-9)

  • Amene anakwera pahatchi yoyera (11-16)

  • Phwando lalikulu la Mulungu la chakudya chamadzulo (17, 18)

  • Chilombo chinagonjetsedwa (19-21)

19  Zimenezi zitatha, ndinamva mawu kumwamba amene ankamveka ngati mawu ofuula a khamu lalikulu akuti: “Tamandani Ya!*+ Mulungu wathu amapulumutsa anthu ndipo ali ndi mphamvu zazikulu komanso ulemerero,  chifukwa ziweruzo zake ndi zoona ndi zolungama.+ Iye waweruza hule lalikulu limene linaipitsa dziko lapansi ndi chiwerewere* chake, ndipo walibwezera chifukwa cha magazi a akapolo ake, amene hulelo linapha.”*+  Nthawi yomweyo, ananenanso kachiwiri kuti: “Tamandani Ya!*+ Utsi umene ukufuka chifukwa cha kuwotchedwa kwake udzafuka mpaka kalekale.”+  Ndiye akulu 24+ ndi angelo 4 aja,+ anagwada pansi nʼkuwerama ndipo analambira Mulungu amene wakhala pampando wachifumu, nʼkunena kuti: “Ame! Tamandani Ya!”*+  Komanso kumpando wachifumu kunamveka mawu akuti: “Muzitamanda Mulungu wathu, inu nonse akapolo ake,+ amene mumamuopa, olemekezeka ndi onyozeka omwe.”+  Kenako ndinamva mawu amene ankamveka ngati mawu a khamu lalikulu, ngati mkokomo wa madzi ambiri komanso ngati mabingu amphamvu. Mawuwo anali akuti: “Tamandani Ya!*+ chifukwa Yehova* Mulungu wathu, Wamphamvuyonse,+ wayamba kulamulira monga mfumu!+  Tiyeni tisangalale ndipo tikhale ndi chimwemwe chodzaza tsaya komanso timupatse ulemerero, chifukwa ukwati wa Mwanawankhosa wafika ndipo mkazi wake wadzikongoletsa.  Iye waloledwa kuti avale zovala zapamwamba, zonyezimira ndi zoyera bwino, chifukwa zovala zapamwambazo zikuimira ntchito zolungama za oyera.”+  Mngeloyo anandiuza kuti, “Lemba kuti: Osangalala ndi amene aitanidwa kuchakudya chamadzulo cha phwando la ukwati wa Mwanawankhosa.”+ Anandiuzanso kuti: “Amenewa ndi mawu oona a Mulungu.” 10  Zitatero ndinagwada pansi nʼkuwerama patsogolo pa mapazi ake kuti ndimulambire. Koma iye anandiuza kuti: “Samala! Usachite zimenezo!+ Inetu ndangokhala kapolo mnzako ndi wa abale ako amene ali ndi ntchito yochitira umboni za Yesu.+ Lambira Mulungu,+ chifukwa cholinga cha maulosi ndi kuchitira umboni zokhudza Yesu.”+ 11  Ndinaona kumwamba kutatseguka, kenako ndinaona hatchi yoyera.+ Amene anakwera pahatchiyo dzina lake linali lakuti Wokhulupirika+ ndi Woona.+ Iye amaweruza molungama ndipo akumenya nkhondo mwachilungamo.+ 12  Maso ake anali ngati lawi la moto+ ndipo pamutu pake panali zisoti zachifumu zambiri. Iye analembedwa dzina limene palibe wina aliyense amene akulidziwa koma iye yekha. 13  Iye anavala malaya akunja amene anadonthera* magazi, ndipo amadziwika ndi dzina lakuti Mawu+ a Mulungu. 14  Komanso magulu ankhondo akumwamba ankamutsatira atakwera mahatchi oyera, atavala zovala zapamwamba, zoyera bwino, za mbee! 15  Mʼkamwa mwake munkatuluka lupanga lalitali+ lakuthwa, loti aphere mitundu ya anthu ndipo adzawakusa ndi ndodo yachitsulo.+ Komanso iye ankapondaponda muchopondera mphesa cha mkwiyo waukulu wa Mulungu Wamphamvuyonse.+ 16  Pamalaya ake akunja komanso pantchafu yake, panalembedwa dzina lakuti, Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye.+ 17  Ndinaonanso mngelo ataimirira padzuwa. Iye anafuula ndi mawu okweza kwa mbalame zonse zouluka chapafupi mumlengalenga kuti: “Bwerani kuno, dzasonkhaneni kuphwando lalikulu la Mulungu la chakudya chamadzulo,+ 18  kuti mudzadye minofu ya mafumu, ya akuluakulu a asilikali, ya amuna amphamvu,+ ya mahatchi ndi ya amene akwera pamahatchiwo,+ minofu ya onse, ya mfulu ndi ya akapolo, ya olemekezeka ndi ya onyozeka.” 19  Ndiyeno ndinaona chilombo, mafumu a dziko lapansi ndi asilikali awo atasonkhana pamodzi kuti amenyane ndi amene anakwera pahatchi uja ndi gulu lake lankhondo.+ 20  Koma chilombocho chinagwidwa limodzi ndi mneneri wabodza+ uja, amene anachita zizindikiro pamaso pa chilombocho. Zizindikiro zimenezi anasocheretsa nazo amene analandira chizindikiro cha chilombo+ komanso amene ankalambira chifaniziro chake.+ Onse awiri adakali amoyo, anaponyedwa mʼnyanja ya moto yoyaka ndi sulufule.+ 21  Koma ena onse anaphedwa ndi lupanga lalitali limene linkatuluka mʼkamwa mwa amene anakwera pahatchi+ uja. Ndipo mbalame zonse zinakhuta minofu yawo.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Aleluya!” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene ali mʼmanja mwake.”
Kapena kuti, “Aleluya!” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
Kapena kuti, “Aleluya!” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
Kapena kuti, “Aleluya!” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
Mabaibulo ena amati, “anawazidwa.”