Machitidwe a Atumwi 10:1-48

  • Masomphenya a Koneliyo (1-8)

  • Masomphenya a Petulo a nyama zoyeretsedwa (9-16)

  • Petulo anapita kunyumba kwa Koneliyo (17-33)

  • Petulo analalikira uthenga wabwino kwa anthu a mitundu ina (34-43)

    • “Mulungu alibe tsankho” (34, 35)

  • Anthu a mitundu ina analandira mzimu woyera nʼkubatizidwa (44-48)

10  Ku Kaisareya kunali munthu wina dzina lake Koneliyo, mtsogoleri wa asilikali* a mʼgulu la asilikali a ku Italy.*  Iyeyu ankakonda zopemphera ndipo ankaopa Mulungu pamodzi ndi banja lake lonse. Komanso ankapatsa anthu mphatso zachifundo zambiri ndipo ankapemphera mochonderera kwa Mulungu nthawi zonse.  Tsiku lina cha mʼma 3 koloko+ masana,* anaona masomphenya. Mngelo wa Mulungu anabwera kwa iye nʼkunena kuti: “Koneliyo!”  Zitatero, Koneliyo anayangʼanitsitsa mngeloyo mwamantha nʼkunena kuti: “Lankhulani Mbuyanga.” Mngeloyo anamuuza kuti: “Mulungu wamva mapemphero ako ndiponso waona mphatso zako zachifundo.+  Choncho tumiza anthu ku Yopa kuti akaitane munthu wina dzina lake Simoni, wotchedwanso Petulo.  Munthu ameneyu ndi mlendo kunyumba kwa Simoni wina wofufuta zikopa, amene nyumba yake ili mʼmbali mwa nyanja.”  Mngelo amene ankalankhula nayeyo atangochoka, Koneliyo anaitana atumiki ake awiri ndiponso msilikali wake wina amene ankakonda zopemphera.  Iye anawafotokozera zonse nʼkuwatuma ku Yopa.  Tsiku lotsatira, ulendo wawo uli mkati komanso akuyandikira mzindawo, Petulo anakwera padenga kukapemphera cha mʼma 12 koloko masana.* 10  Koma anamva njala kwambiri ndipo ankafuna kudya. Pamene chakudya chinkakonzedwa, anayamba kuona masomphenya.+ 11  Mʼmasomphenyawo anaona kumwamba kutatseguka, chinthu chinachake chooneka ngati chinsalu chachikulu chikutsika. Chinthucho anachigwira mʼmakona onse 4 nʼkumachitsitsira padziko lapansi. 12  Pachinthucho panali mitundu yonse ya nyama za miyendo 4, nyama zokwawa zapadziko lapansi ndiponso mbalame zamumlengalenga. 13  Kenako anamva mawu akuti: “Petulo, nyamuka ndipo uphe zinthu zimenezi nʼkudya.” 14  Koma Petulo anati: “Ayi Ambuye, ine sindinadyepo chinthu chodetsedwa ndiponso chonyansa chilichonse.”+ 15  Koma anamvanso mawu aja kachiwiri kuti: “Zinthu zimene Mulungu waziyeretsa, usiyiretu kunena kuti nʼzodetsedwa.” 16  Anamvanso mawu amenewa kachitatu, ndipo nthawi yomweyo chinthu chooneka ngati chinsalu chija chinatengedwa kupita kumwamba. 17  Petulo atathedwa nzeru chifukwa chosamvetsa tanthauzo la masomphenyawo, anthu amene Koneliyo anawatuma aja anafunsa kuti nyumba ya Simoni ili kuti ndipo anali ataima pageti.+ 18  Iwo anafunsa mofuula ngati kumeneko anali ndi mlendo dzina lake Simoni wotchedwanso Petulo. 19  Petulo akuganizirabe za masomphenyawo, mzimu wa Mulungu+ unamuuza kuti: “Petulo! Pali anthu atatu amene akukufuna. 20  Ndiye konzeka, tsika upite nawo limodzi. Usakayikire, chifukwa ndawatuma ndine.” 21  Choncho Petulo anatsika nʼkukakumana ndi anthuwo ndipo anati: “Amene mukumufunayo ndine. Tikuthandizeni?” 22  Iwo anati: “Tachokera kwa Koneliyo,+ mtsogoleri wa asilikali. Iye ndi munthu wolungama komanso woopa Mulungu ndipo mtundu wonse wa Ayuda umamuyamikira. Mngelo woyera anamupatsa malangizo ochokera kwa Mulungu kuti atume anthu kudzakutengani kuti mupite kunyumba kwake, akamve zimene inu mukanene.” 23  Ndiyeno anawalowetsa mʼnyumba nʼkuwasamalira monga alendo ake. Kutacha, ananyamuka nʼkupita nawo ndipo abale ena a ku Yopa anapita naye limodzi. 24  Tsiku lotsatira anafika ku Kaisareya ndipo Koneliyo ankawayembekezeradi. Iye anali atasonkhanitsa achibale ake ndi anzake apamtima. 25  Petulo akulowa, Koneliyo anakumana naye ndipo anagwada posonyeza kumulambira. 26  Koma Petulo anamudzutsa nʼkunena kuti: “Imirira, inenso ndine munthu ngati iwe wemwe.”+ 27  Kenako analowa mkati uku akukambirana ndipo anapeza anthu ambiri atasonkhana. 28  Ndiyeno Petulo anawauza kuti: “Inunso mukudziwa bwino kuti si zololeka kuti Myuda azicheza ndi munthu wa mtundu wina kapena kumuyandikira.+ Koma Mulungu wandionetsa kuti ndisatchule munthu aliyense kuti wodetsedwa kapena wonyansa.+ 29  Nʼchifukwa chake ndabwera mosanyinyirika mutatumiza anthu kuti adzandiitane. Choncho ndiuzeni chimene mwandiitanira.” 30  Ndiyeno Koneliyo anati: “Masiku 4 apitawo, ine ndikupemphera mʼnyumba mwanga muno cha mʼma 3 koloko masana,* ndinangoona munthu wovala zowala ataima kutsogolo kwanga. 31  Munthuyo anandiuza kuti, ‘Koneliyo, Mulungu wamva pemphero lako ndiponso waona mphatso zako zachifundo. 32  Choncho tumiza anthu ku Yopa kuti akaitane Simoni wotchedwanso Petulo. Munthu ameneyo ndi mlendo mʼnyumba ya Simoni wofufuta zikopa, amene amakhala mʼmbali mwa nyanja.’+ 33  Nthawi yomweyo ndinatuma anthu kuti akakuitaneni ndipo mwatikomera mtima nʼkubwera. Choncho tonse tili pano pamaso pa Mulungu, kuti timve zonse zimene Yehova* wakulamulani kuti mutiuze.” 34  Petulo atamva zimenezi, anayamba kulankhula kuti: “Ndazindikira ndithu kuti Mulungu alibe tsankho.+ 35  Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.+ 36  Mulungu anatumiza mawu kwa Aisiraeli nʼkulengeza kwa iwo uthenga wabwino wa mtendere+ kudzera mwa Yesu Khristu. Ameneyu ndi Ambuye wa onse.+ 37  Inu mukudziwa nkhani imene inali mʼkamwamʼkamwa kuyambira ku Galileya+ mpaka ku Yudeya konse, pambuyo pa ubatizo umene Yohane ankalalikira. 38  Nkhani yake inali yonena za Yesu wa ku Nazareti, amene Mulungu anamudzoza ndi mzimu woyera+ ndi mphamvu. Popeza Mulungu anali naye,+ anayenda mʼdziko lonse nʼkumachita zabwino ndiponso kuchiritsa anthu onse amene Mdyerekezi+ ankawazunza. 39  Ndipo ife ndife mboni za zinthu zonse zimene anachita mʼdziko la Ayuda ndi ku Yerusalemu komwe. Koma Aisiraeliwo anamupha pomupachika pamtengo. 40  Ameneyu Mulungu anamuukitsa pa tsiku lachitatu+ nʼkulola kuti anthu amuone, 41  osati anthu onse, koma mboni zimene Mulungu anasankhiratu, zomwe ndi ifeyo, amene tinadya ndiponso kumwa naye limodzi ataukitsidwa.+ 42  Ndiponso, anatilamula kuti tilalikire kwa anthu ndi kupereka umboni wokwanira+ woti iyeyu ndi amene Mulungu anamupatsa udindo woweruza anthu amoyo ndi akufa.+ 43  Aneneri onse amachitira umboni za iyeyu,+ kuti aliyense womukhulupirira, machimo ake amakhululukidwa mʼdzina lake.”+ 44  Pamene Petulo ankalankhula zimenezi, anthu onse amene ankamvetsera mawuwo analandira mzimu woyera.+ 45  Ndipo okhulupirira amene anabwera ndi Petulo aja, amenenso anali odulidwa, anadabwa kwambiri. Iwo anadabwa chifukwa mphatso yaulere ya mzimu woyera inaperekedwanso kwa anthu a mitundu ina. 46  Chifukwanso anawamva akulankhula zilankhulo zina* ndiponso kulemekeza Mulungu.+ Ndiyeno Petulo anati: 47  “Anthu awa alandira mzimu woyera ngati mmenenso ife tinalandirira. Ndani amene angaletse kuti asabatizidwe mʼmadzi?”+ 48  Atatero anawalamula kuti abatizidwe mʼdzina la Yesu Khristu.+ Ndiyeno iwo anamupempha kuti akhalebe nawo kwa masiku angapo.

Mawu a M'munsi

Ankayangʼanira asilikali 100.
Gulu la asilikali a Chiroma omwe ankakhalapo 600.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 9,” kuwerenga kuchokera 6 koloko mʼmawa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 6,” kuwerenga kuchokera 6 koloko mʼmawa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 9,” kuwerenga kuchokera 6 koloko mʼmawa.
Kapena kuti, “malilime.”