Miyambo 21:1-31

  • Yehova amatsogolera mtima wa mfumu (1)

  • Kuchita zinthu zachilungamo nʼkwabwino kuposa kupereka nsembe (3)

  • Khama limapindulitsa (5)

  • Amene samvetsera munthu wonyozeka nayenso sadzamvetseredwa (13)

  • Palibe nzeru zotsutsana ndi Yehova (30)

21  Mtima wa mfumu uli ngati mitsinje yamadzi mʼdzanja la Yehova.+ Amaupititsa kulikonse kumene iye akufuna.+   Njira zonse za munthu zimaoneka zabwino kwa iye,+Koma Yehova amafufuza mitima.*+   Kuchita zinthu zoyenera komanso zachilungamoKumasangalatsa kwambiri Yehova kuposa nsembe.+   Maso odzikweza komanso mtima wonyadaZili ngati nyale imene imatsogolera anthu oipa, koma zimenezi ndi tchimo.+   Mapulani a munthu wakhama amamuthandiza kuti zinthu zimuyendere bwino,*+Koma onse amene amachita zinthu mopupuluma amasauka.+   Kupeza chuma pogwiritsa ntchito lilime lonamaKuli ngati nkhungu imene imachoka mofulumira komanso msampha wakupha.*+   Zinthu zachiwawa zimene anthu oipa amachita nʼzimene zidzawawononge,+Chifukwa amakana kuchita zinthu mwachilungamo.   Njira ya munthu wochimwa imakhala yokhotakhota,Koma zochita za munthu wolungama ndi zowongoka.+   Ndi bwino kukhala pakona ya denga la nyumbaKusiyana ndi kukhala mʼnyumba limodzi ndi mkazi wolongolola.*+ 10  Munthu woipa amalakalaka zoipa,+Ndipo mnzake samukomera mtima.+ 11  Munthu wonyoza akapatsidwa chilango, wosadziwa zinthu amakhala wanzeru,Ndipo munthu wanzeru akaphunzira zinthu zambiri, amadziwa zinthu.*+ 12  Mulungu amene ndi wolungama amayangʼana nyumba ya munthu woipa.Amagwetsa anthu oipa kuti akumane ndi tsoka.+ 13  Aliyense amene amatseka khutu lake kuti asamve kudandaula kwa munthu wonyozeka,Nayenso adzaitana koma sadzayankhidwa.+ 14  Mphatso yoperekedwa mwachinsinsi imathetsa mkwiyo,+Ndipo chiphuphu choperekedwa mwamseri* chimathetsa ukali waukulu. 15  Wolungama amasangalala akamachita chilungamo,+Koma anthu ochita zoipa amadana ndi chilungamo. 16  Munthu amene wasochera nʼkusiya kuchita zinthu mozindikiraAdzapumula mʼgulu la anthu akufa.+ 17  Munthu amene amakonda zosangalatsa adzasauka.+Amene amakonda vinyo ndi mafuta sadzalemera. 18  Munthu woipa ndi dipo la munthu wolungama,Ndipo munthu wochita zachinyengo adzatengedwa mʼmalo mwa anthu owongoka mtima.+ 19  Ndi bwino kukhala mʼchipululuKusiyana ndi kukhala ndi mkazi wolongolola* komanso wosachedwa kukwiya.+ 20  Chuma chamtengo wapatali komanso mafuta zimapezeka mʼnyumba ya munthu wanzeru,+Koma munthu wopusa amasakaza* zinthu zimene ali nazo.+ 21  Amene akufunafuna chilungamo ndiponso chikondi chokhulupirikaAdzapeza moyo, chilungamo ndi ulemerero.+ 22  Munthu wanzeru amagonjetsa* mzinda wa anthu amphamvu,Ndipo amawononga mpanda wolimba umene amadalira.+ 23  Amene amateteza pakamwa pake komanso lilime lakeAmapewa mavuto.+ 24  Munthu wochita zinthu modzikuza amene saganizira zotsatira zake ndi amene mumamutiNdi munthu wonyada komanso amene amakonda kudzionetsera ndiponso kudzitamandira.+ 25  Zinthu zimene munthu waulesi amalakalaka zidzamupha,Chifukwa manja ake amakana kugwira ntchito.+ 26  Tsiku lonse amalakalaka chinachake mwadyera,Koma munthu wolungama amapereka, saumira chilichonse.+ 27  Nsembe ya munthu woipa ndi yonyansa.+ Ndiye kuli bwanji akaipereka ndi zolinga zoipa!* 28  Mboni yonena mabodza idzawonongedwa,+Koma munthu amene amamvetsera adzapereka umboni wa zinthu zimene anamva ndipo zidzamuyendera bwino.* 29  Munthu woipa amadzionetsa ngati wolimba mtima,+Koma wolungama amasankha njira yoyenera kuyenda.+ 30  Palibe nzeru kapena kuzindikira, kapena malangizo amene angalepheretse zimene Yehova amafuna.+ 31  Hatchi amaiphunzitsa pokonzekera tsiku la nkhondo,+Koma Yehova ndi amene amapulumutsa.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “zolinga.”
Kapena kuti, “zinthu zimupindulire.”
Mabaibulo ena amati, “mofulumira kwa amene akufunafuna imfa.”
Kapena kuti, “wokonda kudandaula.”
Kapena kuti, “amadziwa zoyenera kuchita.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chiphuphu chobisidwa pachovala.”
Kapena kuti, “wokonda kudandaula.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amameza.”
Kapena kuti, “amakwera mpanda wa.”
Kapena kuti, “limodzi ndi khalidwe lochititsa manyazi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzalankhula kwamuyaya.”