Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mawu Omaliza

Mawu Omaliza

Kodi mukukumbukira nthawi yomwe munkasangalala ndi Akhristu anzanu? Mwina mukukumbukira misonkhano ikuluikulu kapena ya mpingo imene inakulimbikitsani kwambiri. Mwinanso munasangalala mutalalikira munthu winawake kapena pamene munacheza ndi m’bale kapena mlongo wina. Ngati zili choncho ndiye kuti simunaiwale Yehova ndipo iyenso sanakuiwaleni. Iye amakumbukira zabwino zimene munkachita pomutumikira ndipo akufunitsitsa kukuthandizani kuti mubwerere.

Paja Yehova anati: ‘Inetu ndidzafunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalira. Ndidzasamalira nkhosa zanga ngati mmene amachitira munthu amene amadyetsa gulu la nkhosa zake pamene ali pakati pa nkhosa zimene zinabalalika. Ndidzapulumutsa nkhosazo kuchokera m’malo onse kumene zinabalalikira.’—Ezekieli 34:11, 12.