Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mwana Wanu Amagwiritsa Ntchito Intaneti?

Kodi Mwana Wanu Amagwiritsa Ntchito Intaneti?

Kodi Mwana Wanu Amagwiritsa Ntchito Intaneti?

PANTHAWI iliyonse ndiponso kulikonse, kaya kunyumba, kusukulu, kwa anzawo, pafoni ya m’manja ndi pa zipangizo zina, ana ambirimbiri amagwiritsa ntchito Intaneti. Ngati ndinu kholo, mwinanso mwana wanu akuchita zimenezi, ndipo n’kutheka kuti amadziwa zambiri kuposa inuyo. Mwinanso amadziwa kubisa zimene iye amachita pa Intaneti.

Zimenezi n’zodetsa nkhawa, koma sikuti palibe chimene tingachite ndi vutoli. N’zoona, zingaoneke kuti mwana wanu amaidziwa bwino Intaneti kuposa inuyo. Komabe inunso mungathe kudziwa zina ndi zina zokhudza Intaneti. Ndipo sikuti mukufunikira kukhala katswiri wa chilichonse chokhudza Intaneti kuti muteteze mwana wanu.

Nkhaniyi ili ndi mfundo zimene zingakuthandizeni. Choyamba, tiyeni tione ena mwa mavuto amene mwana wanu angakumane nawo pa Intaneti.

[Mawu Otsindika patsamba 3]

Ku Canada pafupifupi theka la achinyamata amene ali ndi foni za m’manja, amagwiritsa ntchito Intaneti pafonizo