Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Okhulupirira Kuti Kulibe Mulungu Ali pa Kampeni

Anthu Okhulupirira Kuti Kulibe Mulungu Ali pa Kampeni

Anthu Okhulupirira Kuti Kulibe Mulungu Ali pa Kampeni

MASIKU ano kwabwera gulu lina la anthu omwe sakhulupirira zoti kuli Mulungu. Mosiyana ndi magulu ena a m’mbuyomu, anthu a m’gululi ali pa kampeni yokopa anthu ena kuti atengere maganizo awo. Munthu wina wolemba nkhani m’nyuzipepala, dzina lake Richard Bernstein, ananena kuti iwo akuchita zimenezi “mwakhama, mokwiya, komanso modzipereka kwambiri n’cholinga choti anyengerere anthu opembedza kuti asiye kukhulupirira kuti kuli Mulungu.” Iwo akunyengereranso ngakhale anthu amene amanena kuti n’zosatheka kudziwa ngati Mulungu alipo kapena ayi, chifukwa kwa iwo imeneyi si nkhani yokayikiranso ayi. Mulungu kulibe basi.

Munthu wina yemwe analandirapo mphoto ya Nobel, dzina lake Steven Weinberg, anati: “Anthu padzikoli ayenera kusiya kukhulupirira zinthu zopanda pake zimene zipembedzo zakhala zikuphunzitsa kwa nthawi yaitali. Asayansife tiyenera kuchita chilichonse chimene tingathe kuti zipembedzo zisakhalenso ndi mphamvu ndipo ngati zimenezi zitatheka, dziko lingadzatikumbukire kuti tinachita zazikulu.” Njira imodzi imene akugwiritsa ntchito kuti akwanitse zimenezi ndi kulemba mabuku. Ndipo zikuoneka kuti anthu akukonda kwambiri mabuku awowo chifukwa ena mwa mabukuwa akuyenda malonda kwambiri.

Zipembedzo n’zimene zathandizira kuti gulu latsopanoli liyambe, chifukwa anthu atopa ndi zinthu zankhanza, zauchigawenga, ndi nkhondo zimene zimachitika m’dzina la chipembedzo. Munthu wina wotchuka yemwe sakhulupirira zoti kuli Mulungu, anati: “Chipembedzo chimawononga zinthu kwambiri. Chili ngati poizoni.” Poizoni ameneyu akuphatikizapo zikhulupiriro zawo komanso zinthu zankhanza zimene amachita. Anthu a m’gulu latsopanoli amanenanso kuti anthu ayenera kuthandizidwa kuzindikira kuti ziphunzitso zikuluzikulu za zipembedzo n’zonama ndipo ayenera kusiya kuzikhulupirira n’kuyamba kukhulupirira zinthu zomveka ndiponso zanzeru. Munthu wina wokhulupirira kuti kulibe Mulungu, dzina lake Sam Harris, ananena kuti anthu sayenera kuopa kudzudzula “zinthu zabodza ndiponso zosokoneza zimene zimapezeka m’Baibulo ndi m’Korani. Ino ndi nthawi yoti tizinena chilungamo, . . . osati kulankhula monyengerera poopa kukhumudwitsa anthu.”

Ngakhale kuti anthu okhulupirira kuti kulibe Mulungu amenewa amanyoza chipembedzo, iwo amatamanda sayansi ndipo ena mwa iwo amanena kuti sayansi imasonyeza kuti kulibe Mulungu. Koma kodi n’zoona kuti sayansi imasonyeza kuti kulibe Mulungu? Ndipo kodi sayansi ingakwanitse n’komwe kuchita zimenezi? Harris ananena kuti: “M’kupita kwa nthawi, zidzadziwika bwinobwino kuti gulu ili linkanena zoona ndipo gulu ili linkanena zabodza.”

Kodi mukuganiza kuti m’kupita kwa nthawi ndi gulu liti limene lidzapezeke kuti limanena zoona? Pamene mukuganizira nkhaniyi, dzifunseni kuti: ‘Kodi kukhulupirira zoti kuli Mlengi pakokha n’koipa? Kodi zinthu zingayambe kuyenda bwino padzikoli ngati tonsefe titayamba kukhulupirira kuti kulibe Mulungu?’ Tiyeni tione zimene ena mwa akatswiri otchuka asayansi ndiponso anthu ena anzeru anena pa nkhani yokhudza chipembedzo, sayansi, ndiponso chikhulupiriro chakuti kulibe Mulungu.