Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Musaganize Kuti Ndamwalira”

“Musaganize Kuti Ndamwalira”

“Musaganize Kuti Ndamwalira”

“Musaime Pamanda Anga N’kumalira,

Ineyo Sindili M’mandamo

Musaganize Kuti Ndamwalira.”

● Kodi ndakatulo imeneyi mumaidziwa? Ndakatuloyi ndi yotchuka kwambiri ndipo yakhala ikutonthoza anthu oferedwa padziko lonse lapansi kwa zaka zambiri. Anthu sadziwa bwinobwino munthu amene analemba ndakatuloyi. Ena amanena kuti ndakatuloyi ndi pemphero limene anthu enaake a ku North America a mtundu wa Navajo ankalinena poika maliro.

Ndakatulo imeneyi inatchuka kwambiri ku Japan zaka zingapo zapitazo chifukwa chakuti anthu ankakonda kuiimba. Koma mawu ena a m’ndakatuloyi asokoneza kwambiri anthu chifukwa chakuti ku Japan, anthu ambiri amakonda kupita kumanda kukapereka ulemu kwa achibale awo amene anafa. Iwo amaganiza kuti achibale awowo adakali ndi moyo m’mandamo. Choncho, ndakatuloyi yachititsa anthu ambiri kumafunsa kuti: “Ngati wakufa sakhala m’mandamo, ndiyeno kodi amapita kuti?”

Anthu a chipembedzo cha Chibuda ku Japan akhala akuchita miyambo yosiyanasiyana ya maliro kwa zaka zambiri, koma amalephera kudziwa yankho la funso lakuti, Kodi munthu akamwalira amapita kuti? Kapena mafunso ena monga akuti: Kodi anthu a zipembedzo zosiyanasiyana komanso a m’mayiko osiyanasiyana akamwalira amapita kumalo ofanana? N’chifukwa chiyani anthu amene anamwalira satiyankha tikamalankhula nawo?

Anthu ambiri amaganiza kuti palibe angakwanitse kuyankha mafunso amenewa, ndiponso kuti kufufuza mayankho ake n’kungotaya nthawi. Komabe mwina mungafune kudziwa chimene chimachitika munthu akamwalira. Baibulo limayankha funso limeneli. Limanena kuti Mulungu analenga anthu awiri oyambirira, Adamu ndi Hava, ali angwiro ndipo anawapatsa malo okhala okongola kwambiri. Akanapitiriza kumvera Mulungu, iwo akanakhala m’Paradaiso mpaka kalekale. Koma chifukwa cha kusamvera, zimenezi sizinachitike.

Mulungu anathamangitsa banjalo kuchoka m’Paradaiso ndipo pamapeto pake iwo anafa. Mulungu anafotokoza chilango chawo motere: “Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.” Munthu anapangidwa kuchokera ku fumbi ndipo akafa thupi lake limasanduka fumbi.—Genesis 2:7; 3:19.

Munthu wina yemwe amagwira ntchito yosamalira manda ku Kofu m’dziko la Japan, ananena kuti: “Timaika mafupa ndi phulusa la munthu wakufa m’manda koma pakapita zaka 10, timapeza kuti phulusa ndi mafupa aja sizikuonekanso.” Zoonadi, matupi athu anapangidwa ndi zinthu zochokera m’nthaka ndipo tikafa, m’kupita kwa nthawi matupiwo amaola n’kusandukanso nthaka. Ndiyeno kodi munthu akafa, wafa basi?

Munthu akafa sadziwa chilichonse, koma Mlengi wathu wachikondi, yemwe amadziwa ngakhale mbalame ikafa, amatikumbukira. (Mateyu 10:29-31) Ndipo mogwirizana ndi zimene iye analonjeza, adzatiukitsa. Iye adzatiitana ku tulo ta imfa.—Yobu 14:13-15; Yohane 11:21-23, 38-44.

Ngati mukufuna kudziwa zambiri zokhudza zimene zimachitika munthu akamwalira, lemberani kalata amene amafalitsa magazini ino ndipo iwo adzakuthandizani kudziwa zambiri. Kapena mungapite pa malo athu a pa Intaneti pa adiresi iyi: www.dan124.com.