Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Munthu Yemwe Ankakonda Kufunsa Mafunso

Munthu Yemwe Ankakonda Kufunsa Mafunso

Munthu Yemwe Ankakonda Kufunsa Mafunso

● Kodi inuyo mumafuna kuti anthu adzakukumbukireni ndi chiyani mukadzafa? Kodi anthu azidzakumbukira chiyani akangoganiza za inuyo? Anthu ambiri amachita zinthu zazikulu pa nkhani ya sayansi, ndale, masewera, ndi zinthu zina zaluso n’cholinga choti anthu asadzawaiwale. Koma bwanji pa nkhani yofunsa mafunso? Kodi mukuganiza kuti anthu angamakumbukire munthu chifukwa chakuti ankakonda kufunsa mafunso?

Zaka 500 zapitazo, munthu wina wa ku Central America ankakonda kufunsa mafunso ochititsa chidwi kwambiri ndipo mpaka pano anthu amamukumbukira chifukwa cha zimenezi. Munthuyu anali mfumu Nicarao. Dzina la dziko la Nicaragua linachokera ku dzina limeneli. Kenako anthu anayamba kugwiritsa ntchito dzinali ponena za mtundu wake wonse, dera limene ankakhala, komanso nyanja yawo yaikulu.

Anthu a mtundu wa Nicarao ankakhala m’dera linalake lapakati pa nyanja yam’chere ya Pacific ndi nyanja ya Nicaragua. Pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Columbus anatulukira dziko la America, anthu ena a ku Spain anakafika m’dera limenelo. Anthuwa motsogoleredwa ndi Gil González Dávila anayenda ulendo wa panyanja kulowera kumpoto n’kukafika ku Costa Rica ndipo kenako mu 1523, anakafika ku Nicaragua.

Mwina anthuwo anali ndi mantha kwambiri pamene amayenda m’dera lachilendo limeneli. Koma n’kutheka kuti anasangalala kwambiri atakumana ndi mfumu Nicarao. Gululi linalandiridwa bwino kwambiri ndi anthu a ku Nicaragua. Anapatsidwa mphatso zosiyanasiyana kuphatikizapo golide wambirimbiri, ndipo mpaka pano anthu a ku Nicaragua amadziwika kuti ndi odziwa kulandira alendo.

Nicarao anali ndi mafunso ambirimbiri amene ankafuna kudziwa mayankho ake. Mabuku a mbiri yakale amasonyeza kuti mfumuyi inafunsa González mafunso otsatirawa:

Kodi munamvapo za chigumula chimene chinapha anthu onse padziko ndi nyama zomwe? Kodi Mulungu adzawononganso dziko lapansi ndi chigumula? Kodi munthu akafa chimachitika n’chiyani? Kodi dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zimayenda bwanji? Kodi zimatheka bwanji kuti zinthu zimenezi zizikhala m’mlengalenga osagwa? Kodi zili kutali bwanji ndi dziko lapansi? Kodi dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zidzaleka liti kuwala? Kodi mphepo imachokera kuti? Kodi kutentha ndi kuzizira ndiponso kuwala ndi mdima zimakhalapo bwanji? N’chifukwa chiyani nthawi zina usiku umatalika kuposa masiku ena?

Mungaone kuti Nicarao ankafunitsitsa kudziwa zinthu zambiri zokhudza chilengedwe. Mafunso ake amasonyeza zimene ankakhulupirira. Amasonyezanso kuti anali ndi chidwi ndi zinthu zofanana ndi zimene anthu amachita nazo chidwi masiku ano. Mafunso ake okhudza chigumula amasonyeza kuti iye ndi anthu ake ankadziwako nkhani yokhudza chigumula chimene Baibulo limafotokoza.—Genesis 7:17-19.

Ngakhale kuti anthu a ku Nicaragua ankachita zinthu zamizimu komanso kupha anthu popereka nsembe, mfumuyi inkafuna kuti anthu ake azikhala ndi moyo wabwino komanso akhale ndi makhalidwe abwino. Mafunso amene mfumuyi inkafunsa ndi umboni wakuti munthu ali ndi chikumbumtima chimene mwachibadwa chimamuuza zinthu zoyenera ndi zosayenera kuchita. Mogwirizana ndi zimenezi, mtumwi Paulo analemba kuti: “Chikumbumtima chawo chimachitira umboni pamodzi ndi iwowo, ndipo maganizo awo amawatsutsa ngakhalenso kuwavomereza.”—Aroma 2:14, 15.

Ngakhale masiku ano anthu amaikumbukirabe mfumuyi chifukwa cha moyo wake wokonda kufunsa mafunso, zomwe zinkamuchititsa kuti aziganizira mozama zinthu zosiyanasiyana zokhudza moyo ndi chilengedwe. (Aroma 1:20) Ndipo pamalo amene mfumuyi inakumana ndi asilikali a ku Spain ku Nicaragua, pali chithunzi cha mfumuyi chomwe anthu anachisema n’cholinga choti aziikumbukira.

[Mapu patsamba 21]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Nicaragua

SOUTH AMERICA

ATLANTIC OCEAN