Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Mukhalenso pa Mtendere ndi Anthu Ena?

Kodi Mungatani Kuti Mukhalenso pa Mtendere ndi Anthu Ena?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Mungatani Kuti Mukhalenso pa Mtendere ndi Anthu Ena?

BAIBULO limati: “[Anthu] onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Anthu onse padziko lapansi, omwe alipo oposa 7 biliyoni, ndi opanda ungwiro. Chifukwa cha zimenezi, kusemphana maganizo n’kosapeweka. Ndiye ngati mwasemphana maganizo ndi wina wake kodi mungatani kuti mukhalenso pa mtendere?

Baibulo limapereka malangizo othandiza. Mwachitsanzo, limanena kuti Mlengi wathu, yemwe dzina lake ndi Yehova, ndi “Mulungu wamtendere.” (Salimo 83:18; Aheberi 13:20) Mulungu amafuna kuti anthufe tizikhala mwamtendere ndi anzathu ndipo iye ndi chitsanzo chabwino pa nkhani imeneyi. Adamu ndi Hava atachimwira Mulungu ubwenzi wawo ndi iye unasokonekera. Koma Mulungu mwamsanga anapeza njira yokhazikitsira mtendere kuti anthu agwirizanenso ndi iye. (2 Akorinto 5:19) Ganizirani mfundo zitatu zotsatirazi zimene zingakuthandizeni kuti mukhalenso pa mtendere ndi anthu ena.

Muzikhululuka ndi Mtima Wonse

Zimene Baibulo limanena “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni.”—Akolose 3:13.

N’chifukwa chiyani zimakhala zovuta? N’kutheka kuti muli ndi chifukwa chomveka ‘chodandaulira mnzanu’ ndipo mukuona kuti si kulakwa kusiya kucheza naye. Mungamaonenso kuti munthu winayo ayenera kukupepesani kaye kuti pakhalenso mtendere. Koma ngati munthu winayo sakudziwa kuti analakwa kapena akukhulupirira kuti sanalakwe, nkhaniyo singathe.

Zimene mungachite Tsatirani malangizo a m’Baibulo okhudza kukhululukirana ndi mtima wonse, makamaka ngati nkhaniyo ndi yaing’ono. Musaiwale kuti ngati Mulungu akanati azingoona zonse zimene timalakwitsa, sitikanaima pamaso pake. (Salimo 130:3) Baibulo limati: “Yehova ndi wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha. Pakuti iye akudziwa bwino mmene anatiumbira, amakumbukira kuti ndife fumbi.”—Salimo 103:8, 14.

Taganiziraninso zimene Baibulo limanena m’buku la Miyambo. Limati: “Kuzindikira kumachititsa munthu kubweza mkwiyo wake, ndipo kunyalanyaza cholakwa kumam’chititsa kukhala wokongola.” (Miyambo 19:11) Kuzindikira kumatithandiza kuti tizitha kudziwa chifukwa chenicheni chimene chachititsa munthu kuchita kapena kulankhula zinthu zinazake. Muyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi munthu ameneyu walankhula zimenezi chifukwa chotopa, kudwala kapena chifukwa cha mavuto enaake amene wakumana nawo?’ Kudziwa mmene ena akumvera, zimene akukumana nazo pa moyo wawo komanso chifukwa chenicheni chimene achitira zinazake kungatithandize kuti tisamafulumire kukwiya komanso kuti tiziwakhululukira.

Muzikambirana

Zimene Baibulo limanena “Ngati m’bale wako wachimwa, upite kukam’fotokozera cholakwacho panokha iwe ndi iyeyo. Ngati wakumvera, ndiye kuti wabweza m’bale wakoyo.”—Mateyu 18:15.

N’chifukwa chiyani zimakhala zovuta? Zinthu monga mantha, mkwiyo komanso manyazi zingakulepheretseni kukambirana ndi munthu winayo kuti mukhalenso pa mtendere. Komanso kuuza anthu ena kuti akuthandizeni kungachititse kuti nkhaniyo ikule.

Zimene mungachite Ngati mukuona kuti nkhaniyo ndi yaikulu moti simungathe kungoisiya, yesetsani kukambirana ndi munthu amene wakulakwiraniyo. Pochita zimenezi, yesani kutsatira mfundo izi:

(1) Muzikambirana mwamsanga: Musachedwe kukambirana chifukwa mukachedwa, vutolo likhoza kumangopitirira kapena kumangokula. Yesani kutsatira zimene Yesu ananena kuti: “Ngati wabweretsa mphatso yako paguwa lansembe, ndipo uli pomwepo wakumbukira kuti m’bale wako ali nawe chifukwa, siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako choyamba, ndipo ukabwerako, pereka mphatso yako.”—Mateyu 5:23, 24.

(2) Muzikambirana mwachinsinsi: Muzipewa kuuza anthu ena za nkhaniyo. Baibulo limati: “Kambirana mlandu wako ndi mnzako, ndipo usaulule chinsinsi cha munthu wina.”—Miyambo 25:9.

(3) Muzikambirana mwamtendere: Yesetsani kuti pokambirana musamalozane chala. Cholinga chanu ndi kukhazikitsa mtendere, osati kudziwa kuti wolakwa ndi ndani. Mungachite bwino kumagwiritsa ntchito mawu akuti “Ineyo” m’malo mwa mawu akuti “Inuyo.” Mwachitsanzo, m’malo monena kuti “Zimene munachita zija zandikhumudwitsa,” mungachite bwino kunena kuti “Ndakhumudwa chifukwa cha . . . ” Pa mfundo imeneyi Baibulo limati: “Tiyeni titsatire zinthu zobweretsa mtendere ndiponso zolimbikitsana.”—Aroma 14:19.

Khalani Oleza Mtima

Zimene Baibulo limanena “Musabwezere choipa pa choipa. . . . Koma ‘ngati mdani wako ali ndi njala, um’patse chakudya. Ngati ali ndi ludzu, um’patse chakumwa. Pakuti mwa kutero udzamuunjikira makala a moto pamutu pake.’”—Aroma 12:17, 20.

N’chifukwa chiyani zimakhala zovuta? Mungaganize zongosiya chifukwa choona kuti mwayesetsa kambirimbiri kukhazikitsa mtendere koma mnzanu sakufuna.

Zimene mungachite Muzikhala oleza mtima. Anthu amachita zinthu mosiyana malinga ndi kuchuluka kwa zimene akudziwa zokhudza Baibulo. Ena amatenga nthawi yaitali kuti mkwiyo wawo uthe komanso ena akuphunzira kumene kukhala ndi makhalidwe abwino. Choncho pitirizani kuwachitira zinthu mwachifundo komanso mwachikondi. Baibulo limati: “Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.”—Aroma 12:21.

Kuti tikhale pa mtendere ndi ena tiyenera kusonyeza khalidwe lodzichepetsa, kuleza mtima, kuchita zinthu mozindikira komanso mwachikondi. Dziwani kuti kukhala mwamtendere ndi anthu ena kumabweretsa madalitso ambiri.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● N’chiyani chingakuthandizeni kuti mukhululukire ndi mtima wonse munthu amene wakulakwirani?—Akolose 3:13.

● N’chiyani chingakuthandizeni kuti mukambirane ndi munthu amene mwasemphana naye maganizo?—Mateyu 5:23, 24.

● Kodi mungatani ngati mwayesetsa kukhazikitsa mtendere koma munthuyo sakufuna?—Aroma 12:17-21.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

“Kuzindikira kumachititsa munthu kubweza mkwiyo wake, ndipo kunyalanyaza cholakwa kumam’chititsa kukhala wokongola.”—MIYAMBO 19:11.