Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mapiko a Kachikumbu

Mapiko a Kachikumbu

Kodi Zinangochitika Zokha?

Mapiko a Kachikumbu

● Pafupifupi anthu 900 miliyoni padziko lonse alibe mwayi wopeza madzi akumwa abwino. M’madera ena, azimayi ndi ana amayenda ulendo wautali kukatunga madzi. Shreerang Chhatre, yemwe amagwira ntchito pa sukulu ya Massachusetts Institute of Technology, anati: “N’zomvetsa chisoni kuti anthu osauka amayenda mtunda wautali pa tsiku kuti akangopeza madzi okha basi.” Pofuna kuthana ndi vuto la kusowa kwa madzi, katswiriyu ndi anzake ena, akufufuza njira yopezera madzi kuchokera ku nkhungu. Njira imeneyi ndi imene chikumbu cha mtundu winawake chimapezera madzi. Zikumbu za mtunduwu zimapezeka kuchipululu cha Namib, m’dziko la Namibia.

Taganizirani izi: M’mawa uliwonse, kuchipululu cha Namib, kumakhala nkhungu. Choncho, kachikumbuko kakafuna kupeza madzi kamayang’ana kumene kukuchokera mphepo. * Mapiko a kachikumbuka ali ndi tiziphuphu tomwe timakhala ndi tizinthu tina tomwe timasonkhanitsa timadontho ta madzi. Timadonthoto tikachuluka timayamba kuyenderera m’timizere ta mapiko a kachikumbuko. Timizereto timakhala toti madzi sangalowe mkati, zomwe zimachititsa kuti madziwo atsetsereke mpaka kukagwera m’kamwa.

Pofuna kuthandiza anthu kuti azipeza madzi akumwa, Chhatre ndi anzake akufufuza njira zopezera madzi potengera zimene kachilomboka kamachita. Komabe, kuti anthu akhale ndi moyo amafunika madzi ambiri kuposa amene kachikumbu kamamwa. Ndipo kupeza ndalama zogwirira ntchitoyi si nkhani yamasewera. Choncho, Chhatre anafotokoza kuti tiyembekezere zoti papita nthawi yaitali kuti anthu adzayambe kupeza madzi akumwa ochokera ku nkhungu.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti kachikumbu ka kuchipululu cha Namib kakhale ndi mapiko oterewa, kapena umenewu ndi umboni wakuti pali wina amene anakalenga?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Palinso mitundu ina ya zikumbu imene imapeza madzi pogwiritsa ntchito njira imeneyi.

[Chithunzi patsamba 22]

Timadontho ta madzi timatsetserekera m’kamwa mwa kachikumbuka

[Mawu a Chithunzi patsamba 22]

Photo: Chris Mattison Photography/photographersdirect.com