Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kanyama ka M’nyanja Kosambira Modabwitsa

Kanyama ka M’nyanja Kosambira Modabwitsa

Kodi Zinangochitika Zokha?

Kanyama ka M’nyanja Kosambira Modabwitsa

● Pali kanyama kena ka m’nyanja kooneka ngati bowa. Mbali yaikulu ya thupi lake ndi madzi okhaokha ndipo kamatha kukula masentimita atatu mpaka mamita awiri. Kuti kanyamaka kathe kusambira, thupi lake limatambasuka kenako n’kutsekeka ngati mmene timachitira potsegula ndi kutseka ambulela.

Taganizirani izi: Asayansi ena atulukira kuti tinyama tina ta mtunduwu timasambira modabwitsa kwambiri ngakhale kuti sitisambira mofulumira. Akuti kanyamaka kakamasambira, thupi lake limatambasuka n’kupanga kadzenje kumimba kwake. Kenako limatsekeka zomwe zimachititsa kuti kathe kusuntha. Kutambasuka komanso kutsekeka mobwerezabwerezako kumathandiza kuti kanyamaka kapeze mphamvu zosambira ulendo wautali. Magazini ina inanena kuti: “Ena angaone ngati palibe chodabwitsa chilichonse ndi mmene kanyamaka kamasambirira, koma asayansi amalephera kudziwa mmene kanyamaka kamachitira zimenezi.”

Akatswiri ena akufufuza mmene kanyamaka kamayendera n’cholinga choti apange sitima imene ingamayende pansi pamadzi mosawononga mphamvu zambiri. Katswiri wina wapanga kale sitima yoyenda pansi pamadzi yotalika mamita 1.2. Akuti sitimayi imayenda ngati mmene kanyamaka kamayendera ndipo siwononga mphamvu zambiri poyerekezera ndi sitima zina zoyenda pansi pamadzi. Akatswiriwa akufunanso kupanga chipangizo choyezera mtima. Popeza kuti magazi akamapita kumtima amayenda mofanana ndi mmene kanyamaka kamayendera, iwo akuganiza kuti akhoza kupanga chipangizo chimene chingamawathandize kudziwa mofulumira ngati munthu wayamba kudwala nthenda ya mtima.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti kanyama ka m’madzi kameneka kazitha kusambira mosavuta, kapena alipo wina amene anakalenga?

[Chithunzi patsamba 13]

Thupi lakanyamaka likatambasuka limapanga kadzenje kumimba kwake, kenako umatsekeka zomwe zimachititsa kuti kasunthe

[Mawu a Chithunzi patsamba 13]

Photo: © JUNIORS BILDARCHIV/age fotostock; graphic: Courtesy of Sean Colin