Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

“Kumayambiriro kwa chaka cha 2011, anthu omwe anali ndi mafoni a m’manja padziko lonse anali 5.4 biliyoni.”—UN CHRONICLE, U.S.A.

Pa zaka 10 zapitazi, “anthu oposa 780 000 anafa chifukwa cha masoka achilengedwe ndipo pafupifupi 60 peresenti ya anthu amenewa anafa chifukwa cha zivomezi.”—THE LANCET, BRITAIN.

“Pa zaka zoposa 20 zapitazi, anthu pafupifupi 800,000 ku Russia anadzipha.ROSSIISKAYA GAZETA, RUSSIA.

Ku Philippines, komwe malamulo a dzikolo salola anthu kuthetsa banja, chiwerengero cha akazi a zaka 15 mpaka 49, omwe “akungokhala m’banja ndi mwamuna koma osakwatirana mwalamulo . . . , chinawonjezereka kwambiri kuyambira mu 1993 mpaka mu 2008.”—THE PHILIPPINE STAR, PHILIPPINES.

Pafupifupi “anthu 80 pa 100 alionse m’dziko la Georgia,  . . .amapuma utsi wa fodya amene anthu ena akusuta.” Mumzinda wa Tbilisi, womwe ndi likulu la dzikoli, ana pafupifupi 88 pa 100 alionse amapumanso utsi wa fodya umenewu.”—TABULA, GEORGIA.

Ulendo Wofunafuna Chithandizo Chamankhwala ku Asia

Odwala ambiri padziko lonse akumapita ku Asia kukafunafuna chithandizo chamankhwala. Iwo akumachita zimenezi chifukwa akuona kuti ku Asia kukumapezeka chithandizo chamankhwala chodalirika komanso chotsika mtengo kwambiri poyerekeza ndi zipatala zakwawo. Magazini ya Business World, inanena kuti pofika mu 2015, ku Philippines kuzipita anthu 1 miliyoni chaka chilichonse okafunafuna chithandizo. Akuyembekezeranso kuti pofika mu 2020 anthu ochuluka chonchi, azipita ku South Korea chaka chilichonse. Anthu akumakondanso kupita kumayiko ngati India, Malaysia, Singapore ndi Thailand. Anthu a kumayiko a azungu ndi amene akumakonda kupita ku Asia kukafunafuna chithandizo cha matenda monga a mtima komanso a mafupa. Magazini ija inanenanso kuti anthu ena olemera a ku China, akumapita kwa madokotala a ku Asia komweko kuti akawapange opaleshoni yokongoletsa nkhope n’cholinga choti azifanana ndi “anthu enaake otchuka omwe amawasirira.”

Anthu ogwira ntchito zambiri nthawi imodzi sagwira zolongosoka

Masiku ano, anthu ambiri akutha kugwira ntchito zambirimbiri pa nthawi imodzi chifukwa cha kupita patsogolo kwa zipangizo zamakono. Komabe, mkulu wa pa yunivesite ya Stanford ku United States, dzina lake Clifford Nass, ananena kuti: “Nthawi zambiri anthu amene amagwira ntchito zambirimbiri nthawi imodzi sagwira zolongosoka.” Zikuoneka kuti anthu amene amagwira ntchito zambiri nthawi imodzi, amakhala ndi nkhawa, sachedwa kusokonezeka, amachita zinthu asanaganize bwino zimene zimachititsa kuti aziiwala zinthu zofunika. Choncho Clifford Nass analangiza kuti: “Mukayamba kugwira ntchito inayake, muzionetsetsa kuti mukugwira ntchito yokhayo, mwina kwa mphindi 20. Zimenezi zimathandiza kuti maganizo anu azikhala pa chinthu chimodzi komanso kuti muziganiza bwino.”