Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Zolaula

Zolaula

Kodi Baibulo Limaletsa Kuonera Zolaula?

“Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.”—Mateyu 5:28.

ZOTI MUDZIWE

Masiku ano zolaula zikupezeka paliponse moti anthu ambiri akukonda kuonera zolaula kuposa kale. Ngati mukufuna kusangalatsa Mulungu komanso kukhala moyo wosangalala, muyenera kudziwa mmene Mulungu amaonera nkhani imeneyi.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

M’Baibulo mulibe mawu akuti zolaula. Komabe, muli mfundo zosiyanasiyana zosonyeza kuti kuonera zolaula n’kosayenera.

Mwachitsanzo, Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti ngati mwamuna wokwatira ‘akuyang’anitsitsa mkazi’ yemwe si wake, mpaka kulakalaka atagona naye, ndiye kuti akhoza kuchita chigololo. Mfundo imeneyi imagwira ntchito kwa aliyense, kaya ndi wapabanja kapena ayi. Ngati munthu ali ndi chizolowezi ‘choyang’anitsitsa’ zolaula n’cholinga choti apange zachiwerewere, ndiye kuti akuchita zosayenera ndipo Mulungu amanyansidwa kwambiri ndi anthu ochita zimenezi.

 Kodi kuonera zolaula n’kolakwikabe ngakhale kuti munthuyo alibe cholinga chochita zachiwerewere?

“Chititsani ziwalo za thupi lanu . . . kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, chilakolako cha kugonana, chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje.”—Akolose 3:5.

ZIMENE ANTHU AMANENA

Akatswiri ena ofufuza amanena kuti kuonera zolaula sikungachititse munthu kupanga zachiwerewere. Koma kodi kungoonera zolaula kokhako kulibe vuto lililonse?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo limati kunena “nthabwala zotukwana” n’kosayenera. (Aefeso 5:3, 4) Ndiye kuli bwanji kuonera zolaula? Masiku ano, mafilimu komanso zithunzi zolaula zimasonyeza anthu akuchitadi zachiwerewere, kugonana amuna kapena akazi okhaokha komanso zinthu zina zoipa. Choncho ngati Mulungu amanyansidwa ndi munthu wolankhula nthabwala zotukwana, ndiye kuti amanyansidwanso kwambiri ndi munthu amene ali ndi chizolowezi choonera zolaula.

Akatswiri amanena zosiyanasiyana pa nkhani ya kuonera zolaula. Koma Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti kuonera zolaula kokhako, kumasokoneza ubwenzi wa munthu ndi Mulungu ndipo Mulungu amanyansidwa ndi munthu wochita zimenezi. Baibulo limatilangiza kuti: “Chititsani ziwalo za thupi . . . kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa [ndi] chilakolako cha kugonana.” (Akolose 3:5) Munthu amene amakonda kuonera zolaula amachita zosemphana ndi zimenezi. M’malo mothetsa zilakolako zimenezi, munthu wotereyu amazikolezera.

Kodi mungapewe bwanji kuonera zolaula?

“Yesetsani kuchita zabwino osati zoipa . . . Danani ndi choipa ndipo muzikonda chabwino.”—Amosi 5:14, 15.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo limanena za anthu ena amene ankachita zachiwerewere, kuledzera ndi kuba, koma anasiya makhalidwe oipawa. (1 Akorinto 6:9-11) N’chiyani chinawathandiza kuti asinthe? Chifukwa chotsatira mfundo za m’Mawu a Mulungu, anaphunzira kudana ndi zoipa.

Munthu akhoza kuphunzira kudana ndi khalidwe loonera zolaula ngati atamaganizira mavuto amene angakumane nawo. Kafukufuku wina yemwe anachitika pa yunivesite ya Utah State anasonyeza kuti anthu ena amene ankaonera zolaula “amavutika maganizo, safuna kucheza ndi anthu, sagwirizana ndi anthu a m’banja lawo” komanso amakumana ndi mavuto ena ambiri. Koma choopsa kwambiri n’chakuti, popeza Mulungu amanyansidwa ndi munthu woonera zolaula, zimakhala zovuta kuti akhale pa ubwenzi ndi Mulungu, yemwe ndi Mlengi wathu.

Baibulo likhoza kukuthandizani kuyamba kukonda zabwino. Mukamaliwerenga mungayambe kukonda kwambiri Mulungu komanso kutsatira zimene Baibulo limanena pa nkhani ya makhalidwe abwino. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muzipewa kuonera zolaula komanso mungamve mmene wamasalimo anamvera. Iye analemba kuti: “Sindidzaika maso anga pa chinthu chilichonse chopanda pake.”—Salimo 101:3.