Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Mapiko a Gulugufe Ndi Odabwitsa Zedi

Mapiko a Gulugufe Ndi Odabwitsa Zedi

POFUNA kuthandiza anthu kuti asamangodalira mafuta, asayansi akufuna kupeza njira zina zoti azipanga mphamvu za magetsi kuchokera kudzuwa. Wasayansi wina ananena kuti: “Pali njira yosavuta imene ingatithandize kuchita zimenezi. Tingathe kutengera zimene mapiko a agulugufe amachita.”

Timamba tomwe timakhala pamapiko a gulugufe tili ndi timabowo tooneka ngati timabowo ta chisa cha njuchi

Taganizirani izi: Pa nthawi yozizira agulugufe amatambasula mapiko awo n’kudziyanika padzuwa. Amachita zimenezi pofuna kuti azimva kutentha. Pali agulugufe a mtundu winawake amene mapiko awo amakoka komanso kusunga mphamvu yambiri ya dzuwa. Chimene chimathandiza kwambiri agulugufewa n’choti mapiko awo ali ndi mbali ina yakuda komanso m’mapikomo mumakhala timamba tosanjikizana. Timambati tili ndi tinthu tooneka ngati timabowo ta zisa za njuchi. Pakati pa tinthuti pamakhala timizire tooneka ngati V ndipo n’timene timachititsa kuti kutentha kwa dzuwa kudzilowa m’timabowoto. Zimenezi zimapangitsa kuti mapikowa azikhalabe akuda komanso kuti gulugufe azimva kutentha.

Magazini ina inanena kuti: “Ngakhale kuti mapiko a gulugufe ndi osalimba, asayansi ambiri akuganiza kuti kuona zimene mapikowa amachita kungawathandize kutulukira njira zina zopangira mphamvu za magetsi zambiri kuchokera ku madzi komanso dzuwa.” (Science Daily) Potengera mapiko a gulugufe, asayansi akuonanso kuti akhoza kupanga zipangizo zothandizira kuona komanso zopangira mphamvu za magetsi kuchokera ku dzuwa.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti agulugufewa akhale ndi mapiko otere, kapena pali winawake amene anawapanga?