Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUMATANI MUKAKUMANA NDI MAVUTO?

Vuto Limene Limakhalapo: Kupanikizika

Vuto Limene Limakhalapo: Kupanikizika

MWINA simunkayembekezera kuti moyo wanu udzakhala mmene ulili panopa. N’kutheka kuti mumapanikizika chifukwa chosamalira banja, kugwira ntchito ndiponso kusamalira makolo amene akudwala. Koma mukuonanso kuti si bwino kuchita zonse zimene anthu ena angafune ndipo mwina simungakwanitse. Ndiyeno kodi mungatani?

CHITSANZO CHA M’BAIBULO: MOSE

Poyamba Mose ankaweruza yekha Aisiraeli ndipo mwina ankaona kuti ndi udindo wake. Koma apongozi ake anamuuza kuti: ‘Imene ukutsatirayi si njira yabwino. Ndithu utopa nazo zimenezi.’ Apongozi akewo anamuuza kuti apeze amuna oyenerera amene angathandize kuti nkhani zovuta kwambiri zokha zizibwera kwa Mose. Ndiyeno anamutsimikizira kuti: “Udzaikwanitsa ntchitoyi komanso anthuwa adzabwerera kumahema awo mu mtendere.”—Ekisodo 18:17-23.

ZIMENE DELINA AMACHITA

Monga tanenera m’nkhani yoyamba ija, Delina amadwaladwala komanso amasamalira azichimwene ake atatu olumala. Iye anati: “Sindidera nkhawa za mawa ndipo sindizengereza kuchita zinthu. Izi zimandithandiza kuti ndisamapanikizike. Ndimauzanso anthu momasuka zimene ndikuvutika nazo. Choncho mwamuna wanga komanso anthu ena amandithandiza. Tsiku lililonse ndimapezanso nthawi yochepa yosamalira maluwa chifukwa zimandisangalatsa.”

“Chilichonse chili ndi nthawi yake.”—Mlaliki 3:1

ZIMENE MUNGACHITE

Ngati mumapanikizika kwambiri, yesani izi:

  • Mungapemphe ena kuti azikuthandizani. Mwachitsanzo, mungapemphe ana anu, achibale kapena anzanu amene amakhala pafupi.

  • Muziuza anthu ena mavuto anu. Mwachitsanzo, mungakambirane ndi abwana anu ngati akukupanikizani. Mwina mukawafotokozera mavuto anu, akhoza kukuchepetserani ntchito.

  • Lembani zinthu zonse zimene muyenera kuchita mlungu uliwonse. Kodi pali zinthu zina zimene anthu ena angakuchitireni?

  • Mukaitanidwa kocheza ganizani bwino musanavomere. Ngati mulibe nthawi yokwanira kapena mwatopa, mungokana mwaulemu.

Mfundo Yofunika: Mukamayesa kuchita zonse nokha mukhoza kulephera kuchita chilichonse.