Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nyanja ya Nicaragua imadziwika kwambiri chifukwa cha chilumba chokongola cha Ometepe chomwe chili ndi mapiri awiri omwe amaphulika

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Nicaragua

Dziko la Nicaragua

NICARAGUA ndi dziko lomwe lili ndi nyanja zambiri komanso kumakonda kuphulika mapiri. Dziko la Nicaragua ndi limene lili ndi nyanja yaikulu kwambiri ku Central America konse. Anthu a m’dzikoli amatchula nyanjayo kuti Cocibolca kutanthauza nyanja ya madzi okoma. M’nyanja ya Nicaragua muli zilumba zambiri ndipo ndi nyanja yokhayo imene ndi yopanda mchere yomwe mumapezeka nsomba za m’nyanja zikuluzikulu monga shaki.

Maluwa a ku Nicaragua omwe amawatchula kuti sacuanjoche

Ku Nicaragua kuli dera linalake lakutali kwambiri lomwe amalitchula kuti Mosquito Coast. Derali lili m’mbali mwa nyanja komanso ndi lalikulu makilomita 65 ndipo limakafika ku Honduras, dziko lomwe linachita malire ndi Nicaragua. Ku Mosquito Coast kumakhala anthu amtundu wa Miskito ndipo anthu amenewa anabwera kale kwambiri m’dzikoli moti pamene anthu amitundu ina ankafika m’dzikoli cha m’ma 1500, anachita kuwapeza.

Amiskito ndi anthu ogwirizana kwambiri komanso ali ndi chikhalidwe chosiyana kwambiri ndi ena. M’chinenero cha Chimesikito mulibe mawu ena omwe anthu amatchula pofuna kulemekeza munthu. Mwachitsanzo m’madera a kumidzi, ana amatchula munthu wamwamuna kuti “Ankolo” ndipo wamkazi amangoti “Anti,” kaya anthuwo atakhala achibale awo kapena ayi. Kuyambira kale, azimayi a mtundu wa Miskito amapatsana moni pogunditsana masaya. Akangogunditsana masayawo, mzimayi amene anayamba kupereka moniyo amapuma mokoka mpweya.

Anthu a ku Nicaragua

Mabuku a Mboni za Yehova ofotokoza nkhani za m’Baibulo olembedwa m’chinenero cha Chimayanya ndi Chimesikito