Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

GALAMUKANI! Na. 1 2017 | N’chifukwa Chiyani Achinyamata Ambiri Akudwala Matenda Ovutika Maganizo?

Zikuoneka kuti chiwerengero cha achinyamata ovutika maganizo chikukwera kwambiri.

Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chingathandize kuchepetsa vutoli?

Galamukani! iyi ikufotokoza mfundo zina zimene zingathandize achinyamata amene akudwala matendawa ndiponso mmene makolo awo angawathandizire.

 

NKHANI YAPACHIKUTO

N’chifukwa Chiyani Achinyamata Ambiri Akudwala Matenda Ovutika Maganizo?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zizindikiro zake ndiponso zimene zimayambitsa matendawa. Onani zimene makolo komanso anthu ena angachite kuti athandize achinyamatawa.

Kumwetulira Ndi Mphatso Yofunika Kugawana

Kumwetulira n’kopatsirana moti anzathu kapena anthu amene sitikuwadziwa akatimwetulira, timamva bwino ndipo nafenso timawamwetulira

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kuchotsa Mimba

Chaka chilichonse anthu mamiliyoni ambiri amachotsa mimba. Kodi kuchotsa mimba ndi nkhani yoti munthu akhoza kungosankha yekha zochita?

“Chikondi Chimene Anatisonyeza Chinatikhudza Kwambiri”

Loweruka pa 25 April, 2015, ku Nepal kunachitika chivomerezi champhamvu kwambiri. Zimene a Mboni za Yehova anachita pambuyo pa chivomerezichi zinasonyeza kuti Akhristu enieni amakondana kwambiri.

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Kodi Mungasonyeze Bwanji kuti Mumayamikira Zimene Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Amachita?

Mwamuna ndi mkazi akamayesetsa kuona zabwino zimene mnzawo amachita, nthawi zambiri chikondi chawo chimakula. N’chiyani chingakuthandizeni kuti muziyamikira mwamuna kapena mkazi wanu?

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Nyerere Yokhala ndi Zinthu Zoiteteza ku Dzuwa

Nyerereyi ndi imodzi mwa nyama zimene zimatha kukhala m’malo otentha kwambiri omwe nyama zina sizingakhale. Kodi n’chiyani chimaithandiza kukhala m’malo oterewa?

Zina zimene zili pawebusaiti

N’chiyani Chingandithandize Ndikakhala Ndi Nkhawa?

Zinthu 5 zimene zingakuthandizeni kuti muzida nkhawa pa zinthu zoyenera m’malo mwa zinthu zimene zingakubweretserani mavuto.

Kodi a Mboni za Yehova Amagwira Nawo Ntchito Yothandiza Ena Pakagwa Tsoka?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene timachita pothandiza a Mboni anzathu amene akhudzidwa ndi tsoka komanso anthu ena omwe si a Mboni.