Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Zimene Mungachite Mwana Akatsala Pang’ono Kutha Msinkhu

Zimene Mungachite Mwana Akatsala Pang’ono Kutha Msinkhu

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Makolo ambiri amaona kuti ana amakula mofulumira. Kwa iwowo zimangokhala ngati wabadwa dzulodzuloli, lero n’kupezeka kuti watha msinkhu.

Ana ambiri amavutika akafika pa msinkhu umenewu. Ndiye kodi makolo angawathandize bwanji?

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

Ana amatha msinkhu pa nthawi zosiyanasiyana. Ana ena akhoza kutha msinkhu ali ndi zaka 8 zokha pomwe ena angafike zaka 15 asanathe msinkhu. Buku lina limati: “Ana ena amatha msinkhu ali ndi zaka zochepa pomwe ena amachedwerapo.”—Letting Go With Love and Confidence.

Pa nthawiyi, mwana angamadzikayikire. Achinyamata amaganizira kwambiri mmene anthu ena amawaonera. Mnyamata wina dzina lake Chikondi * anati: “Ndinayamba kuganizira kwambiri za maonekedwe anga ndiponso zochita zanga. Ndinkaopa kuti anthu ena angamaganize kuti si ine munthu wabwinobwino.” Achinyamata angamadzikayikire kwambiri akayamba kutuluka ziphuphu. Mtsikana wina wazaka 17 dzina lake Madalitso anati: “Ndinkaona kuti ziphuphu zikuipitsa nkhope yanga moti tsiku lina ndinayamba kulira n’kumanena kuti ndine wonyansa.”

Ana amene atha msinkhu mofulumira amakumana ndi mavuto ena. Nthawi zina, thupi la mtsikana likayamba kusintha n’kumamera mabere, anthu ena amayamba kumuseka. Komanso buku lina limati: “Anyamata akuluakulu amayamba kukopeka ndi atsikanawo n’kumafuna kuti azigona nawo.”—A Parent’s Guide to the Teen Years.

Mwana akatha msinkhu, sikuti amaganiza ngati munthu wamkulu. Lemba la Miyambo 22:15 limati: “Uchitsiru umakhazikika mumtima mwa mwana.” Ngakhale wachinyamata atatha msinkhu amachitabe zinthu zachibwana. Buku lina limanenanso kuti wachinyamata angamaoneke ngati munthu wamkulu, koma “sizikutanthauza kuti angakhale wodziletsa, angamasankhe zinthu mwanzeru kapena kuchita zinthu ngati munthu wachikulire.”—You and Your Adolescent.

ZIMENE MUNGACHITE

Muzikambirana nkhaniyi ndi mwana wanu nthawiyo isanafike. Muzithandiza mwana wanu kudziwa zimene zidzamuchitikire. Ngati ndi mtsikana, muyenera kumuuza kuti adzayamba kusamba ndipo ngati ndi mnyamata, mungamuuze kuti adzayamba kutulutsa umuna akamalota usiku. Zinthuzi zimayamba mwadzidzidzi ndipo zingapangitse mwana kusokonezeka maganizo kapena kuchita mantha. Mukamakambirana ndi mwana wanu muzimuthandiza kuona kuti zinthuzi zikayamba kumuchitikira sikuti ali ndi vuto, koma ndi chizindikiro choti akukula.—Lemba lothandiza: Salimo 139:14.

Muzifotokoza momveka bwino. Mnyamata wina dzina lake John anati: “Pamene makolo anga ankandifotokozera zimenezi ankangolankhula mokuluwika. Ndikanasangalala akanandiuza mosabisa mawu.” Mtsikana wina wazaka 17 dzina lake Elena anati: “Mayi anga anandifotokozera mmene thupi langa linkasinthira koma ndikanasangalala akanandithandizanso kuti ndisadzavutike nazo maganizo.” Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zimene achinyamatawa ananena? Makolo ayenera kuuza ana awo zonse zimene zingawachitikire akatha msinkhu, ngakhale kuti nkhanizi zingawachititse manyazi.—Lemba lothandiza: Machitidwe 20:20.

Muzifunsa mafunso othandiza mwana wanu kumasuka. Kuti mwana wanu ayambe kumasuka, mwina mungakambirane naye zimene zinachitikira anthu ena. Mwachitsanzo, mungafunse mwana wanu wamkazi kuti, “Kodi pali anzako ena kusukulu amene anakuuza kuti ayamba kusamba?” kapena kuti, “Kodi ana ena kusukulu amaseka atsikana amene ayamba kumera mabere?” Mukhozanso kufunsa mwana wanu wamwamuna kuti, “Kodi ana ena kusukulu amaseka anyamata amene sakuoneka amphamvu?” Achinyamata akayamba kufotokoza zimene zikuchitikira ena, akhoza kuyambanso kumasuka n’kunena zimene zikuwachitikira iwowo komanso mmene akumvera. Ndiyeno akayamba kumasuka, muyenera kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: ‘Mukhale ofulumira kumva, odekha polankhula.’—Yakobo 1:19.

Muzithandiza mwana wanu kukhala ‘wanzeru ndiponso woganiza bwino.’ (Miyambo 3:21) Sikuti mwana akatha msinkhu thupi lake lokha ndi limene limasintha. Pa nthawiyi, mwanayo amayambanso kuganiza mwanzeru kuti akadzakhala wamkulu azidzatha kusankha bwino zochita. Choncho mungachite bwino kumuphunzitsa makhalidwe abwino amene angamuthandize akadzakula.—Lemba lothandiza: Aheberi 5:14.

Musataye mtima. N’zoona kuti achinyamata ambiri samasuka kukambirana ndi makolo awo za nkhaniyi. Komabe buku lina limati: “Wachinyamata angaoneke ngati sakuchita chidwi kapena akunyansidwa ndi zimene mukunena, koma akhoza kukhala kuti akumvetsera.”—You and Your Adolescent.

^ ndime 8 Tasintha mayina m’nkhaniyi.