Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndi Lachikale Kapena Limanena Zinthu Zoti Ena Sanazitulukire?

Kodi Ndi Lachikale Kapena Limanena Zinthu Zoti Ena Sanazitulukire?

SAYANSI

BAIBULO SI BUKU LA SAYANSI KOMA LILI NDI MFUNDO ZOLONDOLA ZOKHUDZA SAYANSI ZOMWE PA NTHAWIYO ASAYANSI ANALI ASANAZITULUKIRE. TIYENI TIONE ZITSANZO ZINGAPO.

Kodi chilengedwechi chili ndi chiyambi?

Poyamba akatswiri asayansi ankanena motsimikiza kuti yankho la funsoli ndi lakuti ayi. Koma masiku ano ambiri amavomereza kuti chilengedwechi chili ndi chiyambi. Baibulo linali litanena kale zimenezi momveka bwino.​—Genesis 1:1.

Kodi dziko lapansili ndi looneka bwanji?

Kale anthu ambiri ankaganiza kuti dziko lapansili ndi lafulati. Zaka za m’ma 400 B.C.E., asayansi a ku Girisi anayamba kunena kuti ndi lozungulira. Koma kale kwambiri asayansi asananene zimenezi, cha m’ma 700 B.C.E., Baibulo linali litanena kale zoti dzikoli ndi “lozungulira.”​—Yesaya 40:22.

Kodi zinthu zakuthambo zimawonongeka?

Wasayansi wina wa zaka za m’ma 300 B.C.E. dzina lake Aristotle ankaphunzitsa kuti zinthu zapadziko lapansi zokha ndi zimene zimawonongeka koma zakumwamba sizisintha kapena kuwonongeka. Kwa zaka zambiri anthu ankakhulupirira zimenezi. Koma m’zaka za m’ma 1800 B.C.E., asayansi anayamba kufotokoza zinthu zina zosonyeza kuti zimenezi si zoona. Iwo anapeza kuti zinthu zonse, kaya zakumwamba kapena zapadzikoli, zimawonongeka. Mmodzi mwa asayansi amene anachititsa kuti anthu ambiri adziwe mfundo imeneyi anali Lord Kelvin. Iye ananena kuti ponena za kumwamba komanso dziko lapansili Baibulo limati: “Zonsezi zidzatha ngati chovala.” (Salimo 102:25, 26) Mofanana ndi zimene Baibulo limanena, Kelvin ankakhulupiriranso kuti Mulungu akhoza kuchititsa kuti zinthu zimene analenga zisawonongeke.​—Mlaliki 1:4.

Kodi mapulaneti anakhazikidwa pachinachake?

Aristotle ankaphunzitsa kuti pulaneti iliyonse ili mkati mwa pulaneti inzake ndipo dziko lapansi ndi limene lili mkati mwenimweni mwa mapulanetiwa. Koma pomafika m’zaka za m’ma 1700 C.E., asayansi anayamba kuvomereza kuti nyenyezi ndi mapulaneti zili m’malere. Koma buku la m’Baibulo la Yobu lomwe linalembedwa m’zaka za m’ma 1400 B.C.E. limati Mulungu “anakoloweka dziko lapansi m’malere.”​—Yobu 26:7.

ZACHIPATALA

NGAKHALE KUTI BAIBULO SI BUKU LA ZACHIPATALA LILI NDI MFUNDO ZOKHUDZA ZAUMOYO ZIMENE PA NTHAWIYO MADOKOTALA ANALI ASANAZITULUKIRE.

Kuika kwaokha anthu odwala matenda opatsirana.

Chilamulo cha Mose chinkati anthu odwala khate azikhala kwaokha. Koma madokotala sankadziwa ubwino wotsatira mfundo imeneyi mpaka pamene kunagwa miliri inayake m’zaka za pakati pa 500 ndi 1500. Mpaka pano madokotala amaonabe kuti njira imeneyi ndi yothandiza.​—Levitiko chaputala 13 ndi 14.

Kusamba m’manja ukagwira munthu wakufa.

Kuyambira kale mpaka chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800, nthawi zambiri madokotala akagwira thupi la munthu wakufa ankagwiranso odwala asanasambe m’manja. Zimenezi zinkachititsa kuti anthu ambiri azifa. Koma m’Chilamulo cha Mose munali lamulo lakuti munthu akagwira thupi la munthu wakufa azikhala wodetsedwa. Ndipotu Chilamulo chinkati munthuyo ankayenera kusamba komanso kuchapa zovala zake kuti akhalenso woyera. Ngakhale kuti Aisiraeli ankachita zimenezi ngati mbali ya chipembedzo chawo, zinkawathandiza kuti asatenge matenda.​—Numeri 19:11, 19.

Kutaya zinthu zoipa.

Chaka chilichonse ana oposa 500,000 amamwalira ndi matenda otsekula m’mimba chifukwa choti anthu ambiri amangochitira chimbudzi paliponse. Koma Chilamulo cha Mose chinkanena kuti chimbudzi cha munthu chiyenera kukwiriridwa pansi kutali ndi kumene anthu amakhala.​—Deuteronomo 23:13.

Nthawi yoyenera kupanga mdulidwe.

Malamulo a Mulungu ankanena kuti mwana wamwamuna ayenera kudulidwa akakwanitsa masiku 8. (Levitiko 12:3) Mwana woti wangobadwa kumene, zimakhala zovuta kuti magazi ake aundane ngati wachekedwa penapake. Zimenezi zimayamba kuchitika bwinobwino pambuyo poti mwanayo wakwanitsa mlungu umodzi. Zimene Chilamulo chinkanenazi, zoti anthu azidikira kuti mwana akwanitse kaye masiku 8, zinkathandiza kuti bala la mwanayo lisachedwe kupola.

Munthu wosangalala amakhala ndi thanzi labwino.

Akatswiri a zaumoyo amanena kuti munthu wosangalala, wamtima woyamikira, wosachedwa kukhululuka ndiponso amene ali ndi chiyembekezo, amakhala ndi thanzi labwino. Baibulo limati: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa, koma mtima wosweka umaumitsa mafupa.”—Miyambo 17:22.