Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ngati Mukuona Kuti Bola Kungofa

Ngati Mukuona Kuti Bola Kungofa

Adriana, yemwe amakhala ku Brazil, anati: “Nthawi zonse ndinkangoganiza kuti sindingathenso kupirira moti ndinayamba kuona kuti bola kungofa.”

KODI inunso nthawi zina mumaona kuti zingakhale bwino mutangofa? Ngati ndi choncho, ndiye kuti mungamvetse mmene Adriana ankamvera. Iye ankada nkhawa kwambiri moti ankangokhala wokhumudwa ndipo ankaona kuti zinthu sizidzakhalanso bwino. Adriana anamupeza ndi matenda ovutika maganizo.

Taganiziraninso za bambo wina wa ku Japan dzina lake Kaoru. Bamboyu ankasamalira makolo ake okalamba omwe ankadwala. Iye anati: “Pa nthawi imeneyi ndinkakumananso ndi mavuto aakulu kuntchito. Zimenezi zinachititsa kuti ndisamafunenso kudya komanso ndizivutika kugona. Ndinkaona kuti zingakhale bwino nditangofa.”

Bambo wina wa ku Nigeria dzina lake Ojebode anati: “Nthawi zambiri ndinkakhala wokhumudwa ndipo pena ndinkalira, moti ndinayamba kuganiza zongodzipha.” Ubwino wake ndi wakuti a Ojebode, a Kaoru komanso Adriana sanadziphe. Koma chaka chilichonse anthu ambirimbiri amadzipha.

KODI N’CHIYANI CHINGAKUTHANDIZENI?

Ambiri mwa anthu amene amadzipha ndi amuna, ndipo ambiri mwa amenewa amakhala kuti ankachita manyazi kupempha thandizo. Komatu Yesu anena kuti anthu odwala amafunika dokotala. (Luka 5:31) Choncho ngati mukuvutika maganizo, musamachite manyazi kupempha thandizo. Anthu ambiri amene ali ndi vutoli aona kuti zinthu zimasintha akalandira thandizo lakuchipatala. A Ojebode, a Kaoru komanso Adriana analandira thandizo ndipo panopa zinthu ziliko bwino.

Madokotala angakupatseni mankhwala kapena malangizo, kapenanso angagwiritse ntchito njira ziwiri zonsezi pokuthandizani. Anthu amene akuvutika maganizo amafunika kuwalezera mtima. Zimakhalanso bwino ngati achibale komanso anzawo akuwathandiza pa vuto lawoli. Bwenzi labwino kwambiri ndi Yehova ndipo kudzera m’Mawu ake, Baibulo, amathandiza anthu amene akuvutika maganizo.

KODI PALI NJIRA YOTHETSERATU VUTOLI?

Nthawi zambiri anthu amene akuvutika maganizo amafunika kulandira thandizo kwa nthawi yaitali komanso kusintha zina ndi zina pa moyo wawo. Ngati mukuvutika maganizo mungakhale ndi chiyembekezo ngati chimene a Ojebode ali nacho, choti m’tsogolomu zinthu zidzakhala bwino. Iwo anati: “Ndimayembekezera nthawi imene lemba la Yesaya 33:24 lidzakwaniritsidwe. Lembali limanena za nthawi yomwe palibe munthu amene adzanene kuti, ‘Ndikudwala.’” Mofanana ndi a Ojebode, inunso muziyembekezera lonjezo la Mulungu la “dziko lapansi latsopano” limene simudzakhala ‘zopweteka.’ (Chivumbulutso 21:1, 4) Pokwaniritsa lonjezoli Mulungu adzathetsanso kuvutika maganizo. Pa nthawiyo simuzidzadanso nkhawa. Zinthu zonse zimene zikukudetsani nkhawa panopa, “sizidzakumbukiridwanso ndipo sizidzabweranso mumtima.”​—Yesaya 65:17.