Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi apolisi apakachisi anali ndani, nanga ntchito yawo inali yotani?

Anthu amtundu wa Levi omwe sanali ansembe ankagwira ntchito zina zofanana ndi zimene apolisi amagwira masiku ano. Iwo ankagwira ntchito zimenezi motsogoleredwa ndi woyang’anira kachisi. Munthu wina wolemba mbiri ya Ayuda dzina lake Philo anafotokoza ntchito zina za apolisi apakachisi. Iye anati: “Ena ankakhala pageti penipeni pa kachisi. Koma ena ankakhala chakutsogolo kuti aziletsa anthu ena kupita kumalo opatulika, kaya mwadala kapena mosazindikira. Ena ankazungulira kunja kwa kachisiyo ndipo ankachita izi mosinthanasinthana masana ndi usiku womwe.”

Khoti Lalikulu la Ayuda linkatha kutuma anthu amenewa kuti awathandize pa zinthu zina. Awa anali ngati asilikali a Chiyuda okhawo amene Aroma ankawalola kuyenda ndi zida.

Katswiri wina dzina lake Joachim Jeremias ananena kuti: “Pamene anthu anapita kukagwira Yesu, iye anawafunsa kuti n’chifukwa chiyani sanamugwire pamene ankaphunzitsa m’kachisi. (Mat. 26.55) Yesu sakanafunsa funso limeneli zikanakhala kuti apolisi apakachisi sanali m’gulu la anthu odzamugwirawo.” Katswiriyu amakhulupiriranso kuti anthu amene anatumidwa kuti akagwire Yesu pa nthawi ina izi zisanachitike analinso apolisi apakachisi. (Yoh. 7:32, 45, 46) Apolisiwa limodzi ndi wowayang’anira ndi amenenso anatumidwa kuti akagwire ophunzira a Yesu n’kupita nawo ku Khoti Lalikulu la Ayuda. Ndipo ayenera kuti ndi amene anagwira Paulo n’kumukokera kunja kwa kachisi.​—Mac. 4:1-3; 5:17-27; 21:27-30.