Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi kachisi wa ku Yerusalemu anamangidwanso pambuyo pa 70 C.E.?

YESU ananena kuti kachisi wa Yehova adzagwetsedwa ndipo sipadzatsala mwala uliwonse pamwamba pa mwala unzake. Ulosi umenewu unakwaniritsidwa mu 70 C.E. M’chakachi asilikali achiroma, otsogoleredwa ndi Tito, anawononga Yerusalemu. (Mat. 24:2) Kenako, mfumu ina ya ku Roma, dzina lake Julian, inakonza zoti imangenso kachisiyu.

Anthu amanena kuti Julian anali mfumu yomaliza ya ku Roma yomwe sinali Mkhristu. Iye anali mwana wa mchimwene wa Constantine Wamkulu ndipo anaphunzitsidwa Chikhristu. Koma atakhala mfumu mu 361 C.E., iye anakana maphunziro achikhristuwo chifukwa cha chinyengo cha anthu amene ankati ndi Akhristu. Akatswiri a mbiri yakale amanena kuti iye anali wampatuko chifukwa chakuti anakana Chikhristu.

Julian ankanyansidwa kwambiri ndi Chikhristu. Chifukwa china n’chakuti ali ndi zaka 6, anaona anthu amene ankati ndi Akhristu akupha bambo ake ndiponso achibale ake. Choncho akatswiri a mbiri yakale amati Julian analimbikitsa Ayuda kumanganso kachisi wawo pofuna kusonyeza kuti Yesu anali mneneri wonyenga. *

N’zoona kuti Julian anakonza zoti amangenso kachisiyu. Koma sitikudziwa ngati anayambadi kumanga. Ndipo ngati anayamba, sitikudziwa chimene chinaimitsa ntchitoyo. Chomwe tikudziwa n’chakuti iye anaphedwa pasanathe zaka ziwiri kuchokera pamene anakhala mfumu ndipo kachisiyo sanamangidwenso.

Apa m’pamene panali kachisi ndipo mwina ankaoneka chonchi nthawi ya Yesu

^ ndime 5 Yesu sananene kuti kachisi sadzamangidwanso. Koma anati adzawonongedwa ndipo izi zinachitikadi mu 70 C.E.