Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

N’chifukwa chiyani munthu wina amene ankakonda kwambiri mankhwala osokoneza bongo, masewera olimbitsa thupi ndiponso kukwera njinga zamoto, anasintha n’kuyamba kutumikira Yehova nthawi zonse? Kodi n’chiyani chinathandiza munthu wina amene ankakonda juga kuti asiye, n’kuyamba kugwira ntchito yovomerezeka kuti azisamalira banja lake? Nanga n’chiyani chinathandiza mtsikana wina amene anabadwira m’banja la Mboni za Yehova kuti ayambirenso kutsatira mfundo za m’Baibulo atasiya kutumikira Yehova kwa kanthawi? Tamvani zimene anthuwa ananena.

ZA MUNTHUYU

DZINA: TERRENCE J. O’BRIEN

ZAKA: 57

DZIKO: AUSTRALIA

POYAMBA: ANKAKONDA MANKHWALA OSOKONEZA BONGO NDI KUKWERA NJINGA

KALE LANGA: Ndinakulira mumzinda wa Brisbane, womwe ndi likulu la dera la Queensland. Makolo anga anali achikatolika koma ndili ndi zaka 8, tinasiya kupita kutchalitchi ndiponso kukambirana za chipembedzo. Ndipo ndili ndi zaka 10, tinasamukira mumzinda wa Gold Coast ku Australia. Tinkakhala pafupi ndi nyanja ndipo kuyambira ndili ndi zaka 13 mpaka 15, ndinkakonda kusambira ndiponso kuchita masewera oyenda pamafunde nditakwera thabwa.

Komabe, zimenezi sizinandithandize kukhala wosangalala. Ndili ndi zaka 8, banja la makolo anga linatha. Kenako mayi anakwatiwanso ndipo pabanja pathu, mowa ndiponso mikangano sizinali zachilendo. Tsiku lina usiku, makolo anga atakangana kwambiri ndinakhala pabedi n’kulumbira kuti ngati ndingadzakwatire sindizidzakangana ndi mkazi wanga. M’banja mwathu tinalipo ana 6 ndipo ngakhale kuti panali mavuto amenewa, tinkakondana kwambiri.

Nditatsala pang’ono kukwanitsa zaka 20, anzanga ambiri anayamba kuchita zinthu zophwanya malamulo. Ankasuta chamba, fodya, kugwiritsa ntchito mankhwala ena osokoneza bongo ndiponso kuledzera. Inenso ndinkachita nawo zimenezi. Komanso ndinkakonda kwambiri kukwera njinga zamoto. Ngakhale kuti ndinachita ngozi zoopsa maulendo angapo, sindinasiye kukwera njinga zamoto ndipo nthawi ina ndinaganiza zoyenda ulendo wapanjinga yamoto kuzungulira dziko la Australia.

Ndipo ngakhale kuti ndinali ndi ufulu wochita zinthu pandekha, nthawi zambiri ndinkakhumudwa ndikaona kuchuluka kwa mavuto padzikoli. Ndinkakhumudwanso kuona kuti anthu ambiri sizikuwakhudza zoti padzikoli pali mavuto. Ndinkalakalaka nditadziwa zoona zenizeni za Mulungu, chipembedzo choona komanso chifukwa chake padzikoli pali mavuto ambiri. Nditafunsa ansembe awiri achikatolika pankhani zimenezi, zomwe anandiyankha zinandikhumudwitsa kwambiri. Ndinafunsanso abusa ambiri amatchalitchi osiyanasiyana koma ndinakhumudwanso ndi zimene anandiyankha. Kenako, mnzanga wina anakonza zoti ndikumane ndi munthu wina wa Mboni za Yehova, dzina lake Eddie. Ndinakambirana ndi Eddie maulendo anayi ndipo nthawi zonsezi iye ankagwiritsa ntchito Baibulo poyankha mafunso anga. Kungoyambira ulendo woyamba kukambirana naye, ndinadziwa kuti ndapeza chinthu chapadera kwambiri. Komabe nthawi imeneyo sindinaone kufunika kosintha khalidwe langa.

MMENE BAIBULO LASINTHIRA MOYO WANGA: Paulendo wanga wozungulira dziko la Australia, ndinakambirana mawu a Mulungu ndi wa Mboni wina amene ndinakumana naye paulendowo. Komabe nditabwerera ku Queensland, sindinakumanenso ndi a Mboni kwa miyezi 6.

Koma tsiku lina ndikuchokera kuntchito, ndinaona azibambo awiri ovala bwino atanyamula zikwama, akuyenda mumsewu ndipo ndinaganiza kuti anali a Mboni za Yehova. Nditawafunsa anandiuza kuti analidi a Mboni za Yehova ndipo ndinawapempha kuti azindiphunzitsa Baibulo. Pasanapite nthawi ndinayamba kupita kumisonkhano ya Mboni za Yehova mpaka ndinapita nawo kumsonkhano waukulu umene unachitikira mumzinda wa Sydney mu 1973. Komabe achibale anga, makamaka mayi anga, atadziwa zimene ndinkachitazi, anakhumudwa kwambiri. Pachifukwa chimenechi ndiponso zifukwa zina, ndinasiya kusonkhana ndi Mboni. Kenako, kwa chaka chimodzi, ndinkangokhalira kusewera mpira womwe ndinkaukonda kwambiri.

Koma m’kupita kwa nthawi, ndinazindikira kuti nthawi imene ndinkaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndi imene ndinkasangalala kwambiri pa moyo wanga. Choncho ndinayambanso kuphunzira Baibulo komanso kupezeka pamisonkhano. Ndiponso ndinasiya kucheza ndi anzanga omwe ankakonda mankhwala osokoneza bongo.

Zimene zinandithandiza kwambiri kusintha khalidwe langa n’zimene ndinaphunzira m’Baibulo, zokhudza Yobu. Munthu wina wachikulire wa Mboni za Yehova, dzina lake Bill, yemwe anali wolimba mtima koma wachifundo, ankabwera nthawi zonse kudzandiphunzitsa Baibulo. Nthawi ina titaphunzira za Yobu, Bill anandifunsa kuti nditchule anthu ena amene Satana amawanena kuti satumikira Yehova ndi mtima wonse. (Yobu 2:3-5) Ndinatchula anthu onse a m’Baibulo amene ndinkawadziwa ndipo mokoma mtima, Bill anandiuza kuti, “ndi zoona zimenezo.” Kenako, anandiyang’anitsitsa n’kundiuza kuti: “Satana akunenanso kuti iweyo sukutumikira Mulungu ndi mtima wonse.” Mawu amenewa anandikhudza kwambiri. Ndisanaphunzire zimenezi, ndinkadziwa kuti mfundo zonse zimene ndinkaphunzira zinali zoona. Koma panthawiyi ndinamvetsa chifukwa chake ndinafunikira kuyamba kuchita zimene ndinkaphunzira. Patangotha miyezi inayi yokha, ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Sindikudziwa kuti moyo wanga ukanakhala wotani zikanakhala kuti sindinaphunzire Baibulo. Ndikukhulupirira kuti bwenzi pano nditafa kalekale. Anthu ambiri amene ndinkacheza nawo anamwalira chifukwa cha khalidwe lawo lokonda mankhwala osokoneza bongo ndiponso mowa. Komanso mabanja awo anali osasangalala. Ndimaona kuti inenso ndikanakhala ngati anzangawa.

Panopa ndinakwatira ndipo tikusangalala kutumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya ku Australia limodzi ndi mkazi wanga, Margaret. Palibe m’bale wanga ngakhale mmodzi amene akulambira Yehova. Koma kwa zaka zambiri ineyo ndi mkazi wanga tasangalala kuphunzira Baibulo ndi mabanja angapo ndiponso anthu ena. Anthuwa asintha moyo wawo ngati mmene ndinasinthira ineyo. Zimenezi zathandiza kuti tipeze anzathu abwino ambiri. Komanso Margaret, yemwe anabadwira m’banja la Mboni, wandithandiza kuti ndikwanitse zimene ndinalumbira zaka pafupifupi 40 zapitazo. Takhala m’banja zaka zoposa 25 ndipo tikusangalala kwambiri. N’zoona kuti sitigwirizana pazinthu zina koma sitinayambe takanganapo. Ine ndi mkazi wanga timaona kuti Baibulo ndi limene latithandiza kwambiri kuti tikwanitse kuchita zimenezi.

ZA MUNTHUYU

DZINA: MASAHIRO OKABAYASHI

ZAKA: 39

DZIKO: JAPAN

POYAMBA: ANKAKONDA JUGA

KALE LANGA: Ndinakulira m’tawuni yaing’ono ya Iwakura, yomwe ili pafupi ndi mzinda wa Nagoya. Ndimakumbukira kuti makolo anga anali achifundo kwambiri. Komabe patapita nthawi ndinazindikira kuti bambo anali m’gulu lina la zigawenga ndipo kwa kanthawi ndithu, ankapeza ndalama zosamalira banja lathu la anthu asanu pochita katangale. Ankaledzeranso tsiku lililonse ndipo ndili ndi zaka 20, iwo anamwalira ndi matenda enaake a m’chiwindi.

Bambo anali a ku Korea ndipo chifukwa cha zimenezi anthu a m’dera lathu ankatisala. Zimenezi ndiponso mavuto ena zinachititsa kuti ndizivutika kwambiri panthawi imene ndinali mnyamata. Ndinayamba sukulu ya sekondale koma ndinkangopita mwa apo ndi apo ndipo patangotha chaka chimodzi ndinasiyiratu. Zinali zovuta kwambiri kuti ndipeze ntchito chifukwa choti ndinamangidwapo komanso bambo anga anali a ku Korea. Koma patapita nthawi, ndinaipeza. Komabe ndinavulala maondo ndipo zimenezi zinachititsa kuti ndizilephera kugwira ntchitoyo.

Kenako, ndinayamba kutchova juga n’cholinga choti ndizipeza ndalama kuti ndizitha kudzisamalira. Nthawi imeneyi ndinkakhala ndi mtsikana wina yemwe anali chibwenzi changa. Iye ankafuna kuti ndipeze ntchito yolongosoka n’cholinga choti tikwatirane. Koma sindinkafuna kusiya juga chifukwa inkandipezetsa ndalama zambiri.

MMENE BAIBULO LASINTHIRA MOYO WANGA: Tsiku lina munthu wina wa Mboni za Yehova anabwera panyumba pathu ndipo anandipatsa buku lakuti Life​—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? Ndinali ndisanaganizirepo za mmene moyo unayambira. Koma nditawerenga bukuli ndinavomera kuti ndiziphunzira Baibulo. Kuyambira kale ndinkafunitsitsa nditadziwa chimene chimachitika munthu akamwalira. Mayankho omveka bwino amene ndinapeza m’Baibulo pankhani imeneyi ndiponso pankhani zina ananditsegula m’maso.

Ndinaona kuti ndinayenera kuyamba kutsatira mfundo za m’Baibulo zimene ndinkaphunzira. Choncho tinakalembetsa ukwati wathu kuboma, ndinasiya kusuta, ndinasiya juga ndiponso ndinameta tsitsi langa limene linali lalitali komanso lopaka mankhwala ofiiritsa. Zimenezi zinachititsa kuti ndizioneka bwino kwambiri.

Koma kusintha makhalidwe amenewa kunali kovuta kwambiri. Mwachitsanzo, pandekha sindikanatha kusiya kusuta fodya. Koma ndinkapemphera mochokera pansi pa mtima kuti Yehova Mulungu andithandize ndipo ndinasiyadi kusuta. Ntchito imene ndinkagwira nditasiya juga inali yovuta kwambiri. Ndinkapeza ndalama zochepa kwambiri poyerekeza ndi ndalama zimene ndinkapeza ndikutchova juga. Lemba limodzi la m’Baibulo limene linandithandiza kuti ndipirire mavuto amenewa ndi Afilipi 4:6, 7. Lembali limati: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, limodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” Ndimaona kuti lonjezo limeneli limakwaniritsidwa pa ineyo.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Nditayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, mkazi wanga sanasangalale nazo. Koma ataona kuti ndikusintha kwambiri khalidwe langa, anayamba kuphunzira nawo komanso kupita nawo kumisonkhano ya Mboni za Yehova. Panopo tonse ndife a Mboni za Yehova. Ndipo tikusangalala kwambiri kutumikira Mulungu limodzi.

Ndisanayambe kuphunzira Baibulo, ndinkaona ngati ndikusangalala. Koma panopa ndi pamene ndikusangalaladi. N’zoona kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo n’kovuta ndithu, koma ndikuona kuti palibe chilichonse chosangalatsa kuposa zimenezi.

ZA MUNTHUYU

DZINA: ELIZABETH JANE SCHOFIELD

ZAKA: 35

DZIKO: UNITED KINGDOM

POYAMBA: ANKAKONDA KUPITA KUMALO AZISANGALALO

KALE LANGA: Ndinakulira m’tawuni ina yaing’ono ya Hardgate, yomwe ili pafupi ndi mzinda wa Glasgow ku Scotland. Ndili ndi zaka 7, mayi anga omwe anali a Mboni za Yehova anayamba kundiphunzitsa Baibulo. Komabe ndili ndi zaka 17 ndinayamba kukonda kwambiri kupita kumalo azisangalalo, kumvera nyimbo zoipa komanso kumwa mowa mwauchidakwa ndi anzanga akusukulu. Ndipo sindinkaganizira n’komwe zinthu zauzimu. Chimene ndinkaona kuti ndi chofunika pamoyo wanga wonse chinali kupita kumalo azisangalalo basi. Komabe, ndili ndi zaka 21, zinthu zinasintha kwambiri.

Ndinapita kukacheza ndi achibale anga ku Northern Ireland ndipo ndili kumeneko ndinaona chionetsero chimene Apulotesitanti anachita. Zimene ndinaona pa chionetserocho zinasonyeza chidani cha Akatolika ndi Apulotesitanti ndipo zinandichititsa mantha kwambiri. Komabe zimenezi zinandithandiza kuti ndiganizire mofatsa moyo wanga. Ndinakumbukira zimene mayi anga anandiphunzitsa kuchokera m’Baibulo ndipo ndinadziwa kuti Mulungu sasangalala ndi anthu amene amanyalanyaza dala mfundo zimene iye anatipatsa chifukwa chotikonda. Ndinazindikiranso kuti nthawi zonse ndinkangochita zofuna zanga, n’kumanyalanyaza zofuna za Mulungu. Choncho ndinaganiza kuti ndikadzabwerera ku Scotland, ndikafufuza mwakhama kuti ndidziwe zimene Baibulo limaphunzitsa.

MMENE BAIBULO LASINTHIRA MOYO WANGA: Nthawi yoyamba imene ndinayambanso kupita kumisonkhano ya Mboni za Yehova ya m’dera la kwathu, ndinali womangika ndipo ndinkachita mantha. Koma aliyense anandilandira bwino kwambiri. Nditayamba kutsatira zimene ndinkaphunzira m’Baibulo, mlongo wina anasonyeza mwapadera kuti amandikonda. Anandithandiza kuti ndisamadzione ngati mlendo ndikapita kumisonkhanoko. Anthu omwe ndinkacheza nawo kale, ankapitirizabe kundiitanira kumalo azisangalalo koma ndinkakana chifukwa ndinali nditayamba kutsatira mfundo za m’Baibulo. Kenako, anangosiya kundiitana.

Poyamba ndinkangoona kuti Baibulo ndi buku la malamulo basi. Koma ndinazindikira kuti anthu otchulidwa m’Baibulo analidi enieni, omwe anali ndi maganizo ndiponso zofooka ngati ineyo. Anthuwa ankachitanso zinthu zina zolakwika, koma atalapa mochokera pansi pamtima, Yehova Mulungu anawakhululukira. Ndinayamba kukhulupirira kuti ngakhale kuti ndili mwana ndinasiya kutumikira Mulungu, iye angandikhululukire ndiponso kuiwala machimo anga ngati nditayesetsa kuchita zinthu zomusangalatsa.

Ndinachitanso chidwi kwambiri ndi khalidwe labwino la mayi anga. Ngakhale kuti ndinasiya kutumikira Mulungu, iwo sanasiye. Kukhulupirika kwawoku kunandithandiza kuti ndizindikire kuti kutumikira Yehova n’kofunika kwambiri. Ndili wamg’ono, sindinkasangalala ndikamalalikira khomo ndi khomo ndi mayi anga. Koma masiku ano ndimatha maola ambiri ndikulalikira ndipo ndaona kuti lonjezo la Yesu lomwe lili pa Mateyo 6:31-33 ndi loona. Iye anati: “Musamade nkhawa n’kumati, ‘Tidya chiyani?’ kapena, ‘Timwa chiyani?’ kapena, ‘Tivala chiyani?’ . . . Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti zinthu zonsezi inu mukuzisowa. Chotero pitirizani kufuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake, ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.” Nditangobatizidwa, n’kukhala wa Mboni za Yehova, ndinasiya ntchito n’kumangogwira maganyu n’cholinga choti ndizitumikira Mulungu nthawi zonse.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Ndili mtsikana ndinkakonda kupita kumalo azisangalalo koma sindinkasangalala ndi moyo. Ndinkaona kuti moyo wanga ndi wopanda cholinga. Popeza kuti tsopano ndikutumikira Yehova ndi mtima wonse, ndikusangalala kwambiri ndipo ndikuona kuti moyo wanga uli ndi cholinga. Panopa ndinakwatiwa ndipo mlungu uliwonse ine ndi mwamuna wanga timayendera mipingo ya Mboni za Yehova kuti tikalimbikitse anthu. Ndimaona kuti kugwira ntchito imeneyi ndi mwayi waukulu kwambiri pamoyo wanga. Ndikuthokoza kwambiri Yehova pondilola kuti ndiyambirenso kumutumikira.

[Mawu Otsindika patsamba 27]

“Kungoyambira ulendo woyamba kukambirana naye, ndinadziwa kuti ndapeza chinthu chapadera kwambiri. Komabe nthawi imeneyo sindinaone kufunika kosintha khalidwe langa”

[Mawu Otsindika patsamba 29]

“Pandekha sindikanatha kusiya kusuta fodya. Koma ndinkapemphera mochokera pansi pa mtima kuti Yehova Mulungu andithandize ndipo ndinasiyadi kusuta”

[Mawu Otsindika patsamba 30]

“Poyamba ndinkangoona kuti Baibulo ndi buku la malamulo basi. Koma ndinazindikira kuti anthu otchulidwa m’Baibulo analidi enieni, omwe anali ndi maganizo ndiponso zofooka ngati ineyo”