Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

“Ndinapeza Ufulu Weniweni”

“Ndinapeza Ufulu Weniweni”
  • CHAKA CHOBADWA: 1981

  • DZIKO: AMERICA

  • POYAMBA: NDINALI MWANA WOLOWERERA

KALE LANGA:

Ndinabadwira m’tauni yotchedwa Moundsville yomwe ili m’mbali mwa mtsinje wa Ohio kumpoto kwa West Virginia ku America. Ndine wachiwiri m’banja mwathu ndipo tilipo ana anayi, anyamata atatu ndi mtsikana. Kunyumba kwathu tinkasangalala kwambiri popeza anyamatafe tinkakonda kucheza komanso kuchita zosangalatsa zosiyanasiyana tikakhala pakhomo. Makolo anga anali anthu olimbikira ntchito, oona mtima komanso ankakonda kwambiri anthu. Sitinali olemera, komabe sikuti tinkakhala moyo wovutika. Popeza makolo anga ndi a Mboni za Yehova, anayesetsa kutiphunzitsa mfundo za m’Baibulo kuyambira tili ana.

Koma mmene ndinkakwanitsa zaka 13, ndinali nditayamba kale kukayikira ngati zimene makolo athu ankatiphunzitsa zinalidi zoona. Ndinkakayikira ngati kutsatira mfundo za m’Baibulo kungathandizedi munthu kukhala ndi moyo wosangalala komanso waphindu. Ndinayamba kuganiza kuti munthu angakhale wosangalala pokhapokha atakhala ndi ufulu wochita chilichonse chimene akufuna. Pasanapite nthawi ndinasiya kupita ku misonkhano ya Mboni za Yehova. Mchimwene wanga ndi mchemwali wanga nawonso anayamba kutsanzira khalidwe langa loipa. Makolo athu anayesetsa kutithandiza, koma tinkakana ndipo tinasiya kuwamvera.

Sindinkazindikira kuti umene ndinkati ufuluwo, uchititsa kuti ndiyambe khalidwe loipa. Tsiku lina ndikuchokera kusukulu mnzanga wina anandipatsa ndudu ya fodya. Kungoyambira tsiku limenelo ndinayamba kuchita zinthu zoipa zambiri komanso zopweteketsa. Pasanapite nthawi ndinayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kumwa mowa mwauchidakwa komanso kuchita zachiwerewere. Kenako ndinayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo oopsa kwambiri ndipo ndinali kapolo wa khalidwe langali. Ndinalowerera kwambiri moyo woterewu moti mpaka ndinayamba kugulitsa mankhwala osokoneza bongo n’cholinga choti ndizipeza ndalama zochitira zimene ndikufuna.

Pa nthawi yonse imene ndinkachita zimenezi chikumbumtima chinkandivutitsa kwambiri chifukwa ndinkadziwa kuti ndikuchita zolakwika. Ndikamayesetsa kuchinyalanyaza m’pamenenso chinkandivutitsa kwambiri. Komabe ndinkadziuza kuti madzi akatayika sawoleka choncho sindingathe kusiya khalidwe langa loipa. Ngakhale kuti ndikapita kumapate komanso kumadansi a oyimba kunkakhala anthu ambirimbiri, nthawi zambiri ndinkasungulumwa komanso sindinkasangalala. Nthawi zina ndikaganiza kuti makolo anga ndi anthu abwino ndipo sangapange zimene ine ndinkapanga,  ndinkadabwa kuti n’chifukwa chiyani ineyo ndinalowerera choncho.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

Ngakhale kuti mwini wakene ndinkaona ngati sindingasinthe khalidwe langali, anthu ena sankaona choncho. M’chaka cha 2000 makolo anga anandipempha kuti ndipite nawo kumsonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova. Ndinapita, koma monyinyirika. Ndinadabwa kwambiri kuti mchimwene wanga ndi mchemwali wanga aja nawonso anapita.

Ndili pamsonkhanowo, ndinakumbukira kuti chaka chimodzi m’mbuyomo ndinalinso pamalo omwewa kudansi ya gulu lina la oyimba. Koma zimene ndinaona pa nthawi ya msonkhanoyo, zinandikhudza kwambiri. Pa nthawi ya dansiyo, anthu ankangotaya zinyalala paliponse ndipo ndudu za fodya zinali mbwee. Anthu ake anali olusa ndipo mawu a nyimbo zomwe zinkaimbidwa anali om’chititsa munthu kukhala wosasangalala. Koma pamsonkhanowo anthu onse anali ansangala ndipo anandilandira bwino ngakhale kuti ndinali nditatha zaka zambiri osapita kumsonkhano. Malowo anali aukhondo ndipo nkhani zimene zinkakambidwa zinali zopatsa chiyembekezo. Nditaona kuti mfundo za m’Baibulo n’zothandiza kwambiri, ndinayamba kudzifunsa kuti n’chifukwa chiyani ndinasiya kuzitsatira.—Yesaya 48:17, 18.

“Baibulo linandithandiza kusiya kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndiponso kugulitsa mankhwalawa. Linandithandizanso kusintha n’kukhala munthu wabwino”

Pasanapite nthawi yaitali, ndinaganiza zoyambiranso kusonkhana ndi Mboni za Yehova. Mchimwene wanga ndi mchemwali wanga aja nawonso anakhudzidwa ndi zimene anamva ndi kuona pamsonkhanowu, ndipo iwonso anaganiza zosiya makhalidwe awo oipa. Tonse tinavomera kuti munthu wa Mboni azitiphunzitsa Baibulo.

Lemba la Yakobo 4:8 ndi limene linandikhudza kwambiri. Lembali limati: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” Ndinazindikira kuti ngati ndikufuna kuyandikira Mulungu, ndiyenera kusiya makhalidwe oipa monga kusuta fodya, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kumwa mowa mwauchidakwa komanso makhalidwe ena onse oipa.—2 Akorinto 7:1.

Ndinasiya kucheza ndi anzanga amakhalidwe oipa ndipo ndinayamba kucheza ndi a Mboni za Yehova. Wa Mboni amene ankaphunzira nane Baibulo, yemwenso anali mkulu, ndi amenenso anandithandiza kwambiri. Nthawi zonse ankandiimbira foni komanso kubwera kunyumba kwathu kudzandiona. Mpaka pano ndimamuonabe kuti ndi mnzanga wapamtima.

M’chaka cha 2001 ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni posonyeza kudzipereka kwa Mulungu. Mchimwene wanga ndi mchemwali wanga aja nawonso anabatizidwa chaka chomwechi. Makolo athu komanso mchimwene wathu, yemwe sanalowerere uja, anasangalala kwambiri ataona kuti tsopano tonse m’banja mwathu tikulambira Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

Poyamba ndinkaona ngati mfundo za m’Baibulo n’zopanikiza koma tsopano ndazindikira kuti zimanditeteza. Baibulo linandithandiza kusiya kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndiponso kugulitsa mankhwalawa. Linandithandizanso kusintha n’kukhala munthu wabwino.

Ndikusangalala chifukwa tsopano ndili m’gulu la anthu olambira Yehova omwe amapezeka padziko lonse. Anthu amenewa amakondanadi ndipo ndi ogwirizana potumikira Mulungu. (Yohane 13:34, 35) M’gulu limeneli ndapezanso mkazi amene ndimam’konda kwambiri dzina lake Adrianne, ndipo ndimaona kuti iye ndi madalitso ochokera kwa Mulungu. Timasangalala kwambiri kutumikira limodzi Mlengi wathu.

Panopa sindikhalanso moyo wongoganizira zofuna zanga zokha koma ndimathera nthawi yambiri kuphunzitsa anthu kuti nawonso apindule ndi zimene Mawu a Mulungu amaphunzitsa. Ntchito imeneyi yandithandiza kukhala wosangalala kwambiri. Ndinganene ndi mtima wonse kuti Baibulo limasinthadi anthu ndipo ndikuona kuti panopa ndinapeza ufulu weniweni.