Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

N’chifukwa Chiyani Ena Amati Mulungu Ndi Wankhanza?

N’chifukwa Chiyani Ena Amati Mulungu Ndi Wankhanza?

ANTHU ena amaona kuti n’zosayenera kufunsa funso lomwe lili pachikuto cha magazini ino chifukwa n’zosatheka kuti Mulungu akhale wankhanza. Koma anthu ambiri amaona kuti Mulungu ndi wankhanza. N’chifukwa chiyani amaganiza choncho?

Anthu ena amene apulumuka pakachitika masoka achilengedwe amadzifunsa kuti: “N’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti zinthu ngati zimenezi zizichitika? Ndiye kuti Mulungu ndi wankhanza?”

Koma ena amakhala ndi maganizo amenewa akamawerenga Baibulo. Mwachitsanzo, akamawerenga nkhani yokhudza Chigumula chomwe chinachitika m’nthawi ya Nowa amadzifunsa kuti: “N’chifukwa chiyani Mulungu, yemwe ndi wachikondi, anapha anthu ambiri chonchi? Ndiye kuti Mulungu ndi wankhanza eti?”

Kodi inuyo munayamba mwadzifunsapo mafunso amenewa? Kapena nthawi zina mumasowa choyankha munthu akakufunsani funso limeneli? Choyamba taganizirani kaye funso ili.

N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHUFE TIMADANA NDI NKHANZA?

Anthufe timadana ndi nkhanza chifukwa Mulungu anatilenga kuti tizitha kudziwa ngati zinthu zili zabwino kapena zoipa. Mlengi wathu anatilenga “m’chifaniziro chake.” N’chifukwa chake timasiyana ndi nyama. (Genesis 1:27) Anatilenga kuti tizitha kusonyeza makhalidwe omwe iye ali nawo. Ndiyeno taganizirani izi: Chifukwa chakuti tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu timadana ndi nkhanza. Ndiye ngati timadana ndi nkhanza, kuli bwanji Mulungu amene anatilengayo?

Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amadana ndi nkhanza chifukwa anachita kunena yekha kuti: “Njira zanga n’zapamwamba kuposa njira zanu, ndiponso maganizo anga ndi apamwamba kuposa maganizo anu.” (Yesaya 55:9) Ndiye ngati titanena kuti Mulungu ndi wankhanza, kodi pamenepa sitingakhale tikunena kuti njira zathu n’zapamwamba kuposa njira za Mulungu? Ngati titamaganiza choncho ndiye kuti tikutsutsana ndi zimene Baibulo limanena. Choncho ndi nzeru kufufuza kaye tisanaweruze kuti Mulungu ndi wankhanza. Mwina m’malo momadzifunsa ngati Mulungu ali wankhanza, ndi bwino kumadzifunsa kuti n’chifukwa chiyani nthawi zina Mulungu amachita zinthu zooneka ngati zankhanza? Kuti timvetse, tiyeni tikambirane tanthauzo la mawu akuti “nkhanza.”

Tikamanena kuti munthu uyu ndi wankhanza ndiye kuti munthuyo amafunira anzake zoipa. Munthu wankhanza amasangalala kuona anthu ena akuvutika ndipo sawamvera chisoni. Mwachitsanzo, bambo amene amalanga mwana wake n’kumasangalala mwanayo akuvutika ndiye kuti bamboyo ndi wankhanza. Koma bambo amene amalanga mwana wake n’cholinga chomuphunzitsa makhalidwe abwino si wankhanza. N’zosavuta kuweruza ena chifukwa anthufe nthawi zambiri sitidziwa chifukwa chimene anthu ena achitira zinazake. Mungamvetse bwino mfundo imeneyi ngati mwina nthawi inayake munthu wina anakuganizirani molakwa kuti muli ndi zolinga zoipa.

Tiyeni tikambirane zifukwa ziwiri zimene zimachititsa anthu ena kuganiza kuti Mulungu ndi wankhanza. Zifukwa zake ndi masoka achilengedwe amene amachitika masiku ano komanso zilango zofotokozedwa m’Baibulo zimene Mulungu anapereka. Tiona ngati zifukwa zimenezi zimasonyezadi kuti Mulungu ndi wankhanza.