Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KUCHEZA NDI MUNTHU WINA

Kodi Mulungu Amamva Chisoni Tikamavutika?

Kodi Mulungu Amamva Chisoni Tikamavutika?

Nkhani ili m’munsiyi ikusonyeza mmene a Mboni za Yehova amachitira akamakambirana ndi anthu nkhani za m’Baibulo.Tiyerekeze kuti mtsikana wina wa Mboni dzina lake Alinafe wafika pakhomo pa mayi Phiri.

N’CHIFUKWA CHIYANI MULUNGU WALOLA KUTI TIZIKUMANA NDI MAVUTO?

Alinafe: Lero ndikugawira anthu a m’dera lino kapepala aka. Mutu wake ndiwakuti, Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? Eni.

Mayi Phiri: Ndinu a chipembedzo chanji?

Alinafe: Ndine wa Mboni za Yehova. Taonani mafunso 6 omwe ali patsamba loyamba la kapepalaka. Kodi mungakonde kuti tikambirane funso—

Mayi Phiri: N’takudulani mawu. Mungotaya nthawi yanu kundilalikira.

Alinafe: N’chifukwa chiyani mukutero?

Mayi Phiri: Ndikuuzeni zoona, ine sindimakhulupirira kuti kuli Mulungu.

Alinafe: Owo, ndithokoze kuti mwandiuza maganizo anu. Komabe n’takufunsani, Munayamba liti kukhala ndi maganizo amenewo?

Mayi Phiri: Kale ndithu, kungoti poyamba ndinkapita kutchalitchi koma kenako ndinasiya.

Alinafe: Owo. Komatu tangoyamba kucheza tisanadziwane. Ine dzina langa ndi Alinafe. Kaya inu ndi ndani?

Mayi Phiri: Ndine mayi Phiri.

Alinafe: Ndasangalala kukudziwani mayi Phiri.

Mayi Phiri: Zikomo kwambiri.

Alinafe: Sindinabwere kuti ndidzakukakamizeni kukhulupirira zimene ndimakhulupirira. Komabe ndifunse kuti, n’chiyani chinakupangitsani kukayikira zoti kuli Mulungu?

Mayi Phiri: Ngozi imene inawachitikira mayi anga. Inachitika zaka 17 zapitazo.

Alinafe: Iiii, pepani kwambiri. Anavulala kwambiri?

Mayi Phiri: Eee, moti panopa analumala.

Alinafe: Pepani kwambiri. Zimenezi ziyenera kuti zinakukhumudwitsani kwambiri.

Mayi Phiri: Eee kwambiri, mpaka pano. Moti ndimadzifunsa kuti, Ngati Mulungu aliko, n’chifukwa chiyani analola kuti zimenezi zichitike? N’chifukwa chiyani amalola kuti tizivutika chonchi?

KODI N’KULAKWA KUFUNSA CHIFUKWA CHAKE MULUNGU AMALOLA KUTI TIZIVUTIKA?

Alinafe: Ndikukumvetsani mmene mukumvera ndipo simukulakwitsa kufunsa mafunso amenewa. Tonsefe tikamakumana ndi mavuto timafuna titadziwa chifukwa chake mavutowo akuchitika. Ndiponsotu Baibulo limanena za atumiki ena okhulupirika a Mulungu amene anafunsapo mafunso ngati amenewa.

Mayi Phiri: Zoona?

Alinafe: Eya. Taimani ndikuonetseni chitsanzo chimodzi cha munthu amene anafunsa mafunso ngati amenewa.

Mayi Phiri: Owo chabwino.

Alinafe: Tiyeni tiwerenge Habakuku 1:2, 3, kuti tione zimene mneneri wokhulupirikayu anafunsa Mulungu. Lembali likuti: “Inu Yehova, kodi ndidzalirira thandizo koma inu osandimva kufikira liti? Kodi ndidzapempha thandizo kuti mundipulumutse ku chiwawa koma inu osandimva kufikira liti? N’chifukwa chiyani mukundichititsa kuona zinthu zopweteka?” Kodi mafunso amenewa akufanana ndi amene inuyo munadzifunsapo?

Mayi Phiri: Eya akufanana.

Alinafe: Mulungu sanakalipire Habakuku chifukwa chofunsa mafunso amenewa ndiponso sanamuone ngati wopanda chikhulupiriro.

Mayi Phiri: N’zodabwitsa bwanji.

YEHOVA AMADANA NDI ZOTI ANTHU AZIVUTIKA

Alinafe: Baibulo limanena kuti Mulungu amaona tikamavutika ndipo amatimvera chisoni.

Mayi Phiri: Mukutanthauza chiyani?

Alinafe: Imani ndikusonyezeni chitsanzo chimene chili pa Ekisodo 3:7. Tawerengani.

 Mayi Phiri: Chabwino. Lembali likuti: “Yehova anawonjezeranso kuti: ‘Ndaona nsautso ya anthu anga amene ali ku Iguputo, ndipo ndamva kulira kwawo chifukwa cha amene akuwagwiritsa ntchito mwankhanza. Zoonadi, ndikudziwa bwino zowawa zawo.’”

Alinafe: Mwawerenga bwino. Mogwirizana ndi zimene taona palembali, kodi Mulungu amaona mavuto amene tikukumana nawo?

Mayi Phiri: Eya, zikuoneka kuti amaona.

Alinafe: Mwaona zimene lembali lanena makamaka chakumapetoku? Mulungu ananena kuti: “Ndikudziwa bwino zowawa zawo.” Kodi mawu amenewa akusonyeza kuti Mulungu ndi wopanda chifundo kapena wouma mtima?

Mayi Phiri: Ayi.

Alinafe: Komatu, kungoona kuti munthu wina akuvutika n’kosiyana ndi kumumvera chisoni.

Mayi Phiri: Zoona zimenezo.

Alinafe: Kuti timvetse mfundo imeneyi, tiyeni tiwerenge zimene zinachitika nthawi ina pamene anthu a Mulungu ankavutika. Tiwerenge lemba la Yesaya 63:9. Mbali yoyamba ya vesili imati: “Pamene iwo anali kuvutika m’masautso awo onse, iyenso anali kuvutika.” Kodi mwaona kuti Mulungu ankamva chisoni pamene anthu ake ankavutika?

Mayi Phiri: Eya, zikuoneka choncho.

Alinafe: Pamenepatu mfundo ndi yakuti, Mulungu amatikonda kwambiri ndipo amadana ndi zoti tizivutika. Ife tikamavutika iye zimamupweteka kwambiri mumtima.

N’CHIFUKWA CHIYANI SAKUTHETSA MAVUTOWA?

Alinafe: Koma ndisanapite, ndimati ndikuonetseninso lemba lina.

Mayi Phiri: Chabwino.

Alinafe: Tiwerenge lemba la Yeremiya 10:12, lomwe limatiuza za mphamvu za Mulungu. Tawerengani.

Mayi Phiri: Chabwino. Akuti: “Mulungu woona ndi amene anapanga dziko lapansi ndi mphamvu zake, amene mwanzeru zake anakhazikitsa dziko limene anthu amakhalamo. Iye ndi amenenso anayala kumwamba mwa kuzindikira kwake.”

Alinafe: Mwawerenga bwino. Taganizirani mfundo imene ili palembali. Kodi Mulungu anafunika mphamvu zambiri bwanji kuti alenge zinthu zonse za kumwamba ndi za padziko lapansi?

Mayi Phiri: Iii, anafunikadi mphamvu zambiri.

Alinafe: Ndiye ngati Mulungu ali ndi mphamvu zolenga zinthu zonse zomwe timazionazi, kodi tingakayikire zoti ali ndi mphamvu zothetsera mavuto amene timakumana nawo?

Mayi Phiri: Ayi sitingakayikire.

Alinafe: Ndiye taganizirani za mayi anu. N’chifukwa chiyani mumamva chisoni mukamawaona akuvutika?

Mayi Phiri: Ndimawakonda chifukwa ndi mayi anga.

Alinafe: Kodi mukanatani mukanakhala ndi mphamvu zowachiritsa?

Mayi Phiri: Ndikanawachiritsa kalekale.

Alinafe: Chabwino. Baibulo limanena kuti Mulungu amaona tikamavutika, amatimvera chisoni komanso ali ndi mphamvu zopanda malire. Ndiye mukhoza kuona kuti Mulungu ndi wodziletsa kwambiri chifukwa ngakhale ali ndi mphamvu zopanda malire, sanazigwiritse ntchito mopupuluma kuti athetse mavutowa.

Mayi Phiri: Komadi eti?

Alinafe: Kodi mukuganiza kuti pali chifukwa chimene chimapangitsa Mulungu kuti asathetse mavutowa? *

Mayi Phiri: Ayenera kuti alidi ndi chifukwa chomveka.

Alinafe: Ndaona kuti mumafuna muziyamba kuchapa ndiye bwanji ndidzabwerenso tsiku lina kuti tidzapitirize kukambirana nkhani imeneyi.

Mayi Phiri: Zikomo kwambiri. Mudzandipeza. *

Kodi pali nkhani inayake ya m’Baibulo imene simumaimvetsa? Kapena mumafuna mutadziwa zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira? Ngati ndi choncho, funsani a Mboni za Yehova ndipo adzasangalala kwambiri kukambirana nanu.

^ ndime 61 Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 11, m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 64 Nkhani yotsatira idzafotokoza chifukwa chimene Mulungu walolera kuti anthu azivutika.