Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MBIRI YA MOYO WANGA

Mavuto Anga Andithandiza Kulimbitsa Ubwenzi Wanga Ndi Yehova

Mavuto Anga Andithandiza Kulimbitsa Ubwenzi Wanga Ndi Yehova

Munthu akandiona nditakhala pa njinga ya olumala, amaona kuti ndine woofoka kwambiri chifukwa kathupi kanga n’kakang’ono ndipo ndimangolemera makilogalamu 29 okha. Koma ngakhale zili choncho, ndili pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndipo zimenezi zandithandiza kuti ndizipirira mavuto anga. Mwina ndikufotokozereni bwinobwino mmene mavuto amene ndakumana nawo pa moyo wanga andithandizira kukhala wolimba.

Ndili ndi zaka 4

Ine ndi makolo anga tinkakhala kum’mwera kwa dziko la France. Ndimakumbukira kuti ndili mwana zinthu zinkayenda bwinobwino m’banja lathu. Bambo anga anandipangira katungwe komanso ndinkakonda kusewera m’minda ya maluwa. Mu 1966, a Mboni za Yehova anafika pakhomo pathu ndipo anakambirana kwa nthawi yaitali ndi bambo anga. Patangotha miyezi 7, bambo anakhala a Mboni. Pasanapite nthawi, nawonso mayi anga anakhala a Mboni ndipo banja lathu linali losangalala komanso lachikondi.

Kenako tinabwerera ku Spain kumene makolo anga anachokera ndipo pasanapite nthawi, ndinayamba kudwala. Ndinayamba kumva kupweteka koopsa m’manja komanso mapazi. Patatha zaka ziwiri tikuyenda m’zipatala zosiyanasiyana, dokotala wina wa matenda a nyamakazi anatiuza kuti: “Matendawatu mwachedwa nawo.” Amayi atamva zimenezi anayamba kulira. Dokotala ananena kuti ndili ndi nyamakazi  * ndipo anafotokozera mayi zambiri za matendawa. Pa nthawiyi n’kuti ndili ndi zaka 10 zokha ndipo sindinkamvetsa bwinobwino zimene zinkakambidwazo. Komabe ndinazindikira kuti dokotalayo akunena kuti ndili ndi matenda aakulu.

Dokotala ananena kuti ndi bwino ndikalandire thandizo pachipatala chinachake cha ana. Nditafika kuchipatalachi sindinasangalale ngakhale pang’ono ndi mmene malowa ankaonekera. Ana onse pachipatalachi ankauzidwa kuti azisunga mwambo. Masisitere anandimeta tsitsi n’kundiveka yunifomu yosaoneka bwino. Zonsezi zinandikhumudwitsa kwambiri ndipo ndinkachita kuoneratu kuti moyo wa pamalopa ukhala wosasangalatsa.

YEHOVA ANANDITHANDIZA KWAMBIRI

Popeza makolo anga anandiphunzitsa kuti ndizitumikira Yehova, ndinkakana kuchita nawo miyambo yachikatolika imene inkachitika pachipatalachi. Masisitere ankadabwa kuti n’chifukwa chiyani ndinkakana kuchita nawo miyamboyi. Ndinapempha Yehova kuti asanditaye ndipo ndinkaona kuti akundikonda komanso kunditeteza ngati mmene bambo wachikondi amachitira.

Makolo anga ankaloledwa kudzandiona kwa nthawi yochepa Loweruka lililonse. Ankandibweretsera  mabuku othandiza kuphunzira Baibulo amene ankandithandiza kukhalabe ndi chikhulupiriro cholimba. Ana sankaloledwa kukhala ndi mabuku awoawo, koma masisitere ankandilola kuti ndiziwerenga mabukuwa ndipo ndinkawasunga pamodzi ndi Baibulo langa, lomwenso ndinkaliwerenga tsiku lililonse. Ndinkauzanso atsikana anzanga za chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi, pomwe sikudzakhalanso matenda. (Chivumbulutso 21:3, 4) Ngakhale kuti nthawi zina ndinkakhala wokhumudwa komanso ndinkawasowa makolo anga, ndinkasangalala kuona kuti chikhulupiriro changa pa Yehova chikukula.

Patatha miyezi 6, madokotala ananditumiza kunyumba. Sikuti ndinali nditachira, komabe ndinasangalala kubwerera kunyumba kuti ndizikakhala ndi makolo anga. Vuto langa lija linkangokulirakulirabe ndipo ululu unawonjezekanso kwambiri. Mmene ndinkakwanitsa zaka 13 n’kuti ndili wofooka kwambiri. Komabe ndili ndi zaka 14 ndinabatizidwa ndipo ndinkafunitsitsa kutumikira Yehova, Atate wakumwamba. Ndikaganizira mavuto anga, nthawi zina ndinkakhumudwa ndipo ndinkamufunsa Yehova kuti: “N’chifukwa chiyani mwalola kuti zimenezi zindichitikire? Taonani mmene ndikuvutikiramu. Chonde Mulungu ndichiritseni.”

Mavuto angawa anachititsa kuti ndisasangalale ndi moyo ngati mmene wachinyamata amachitira. Ndinafunika kungovomereza kuti ndi mmene zinthu zilili pa moyo wanga. Ndikaona achinyamata anzanga akusangalala komanso ali ndi thanzi labwino, ndinkadziona kuti ndine wachabechabe. Zimenezi zinapangitsa kuti ndizipewa kucheza ndi anthu. Komabe, abale anga komanso anzanga ankandithandiza. Ndimakumbukirabe mnzanga wina, dzina lake Alicia yemwe anali wa zaka 20 kuposa ineyo. Iyeyu anali mnzanga wapamtima ndipo anandithandiza kwambiri kuti ndisamangoganizira za matenda anga koma ndiziganiziranso mmene ndingathandizire ena.

ZIMENE ZINANDITHANDIZA KUTI NDIZIKHALABE WOSANGALALA

Ndili ndi zaka 18, matenda anga anakula, moti ngakhale kukasonkhana ndi a Mboni anzanga kunkapangitsa kuti ndikhale wotopa kwambiri. Komabe ndinkagwiritsa ntchito nthawi imene ndinkakhala pakhomo kuwerenga Baibulo. Zimene ndinawerenga m’buku la Yobu ndi la Masalimo, zinandithandiza kudziwa kuti panopa Yehova amatithandiza kwambiri mwauzimu osati mwakuthupi. Kupemphera pafupipafupi kunandithandiza kukhala ndi “mphamvu yoposa yachibadwa” komanso “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.”—2 Akorinto 4:7; Afilipi 4:6, 7.

Ndili ndi zaka 22, ndinayamba kuyendera njinga ya anthu olumala. Ndinkaona kuti anthu akandiona saziganiziranso za ineyo, azingoganizira za mtsikana wodwaladwala woyenda pa njinga ya olumala. Komabe zimene ndinkaganizazi si zimene zinachitika. M’malomwake njingayi inandithandiza kuti ndizitha kuchita zinthu zina ndekha. Mnzanga wina, dzina lake Isabel, anandiuza kuti mwezi wina ndilalikire naye kwa maola 60.

Poyamba sindinagwirizane ndi maganizo amenewa chifukwa ndinkaona kuti sindingakwanitse. Koma ndinapempha Yehova kuti andithandize ndipo abale anga ndi anzanga anandithandizanso kwambiri moti ndinakwanitsa. Mwezi umenewo sunachedwe kutha ndipo ndinaona kuti zimene ndinachitazi zinandithandiza kuti ndisamadziderere. Zimenezi zinandisangalatsa kwambiri moti mu 1996 ndinakhala mpainiya, dzina limene limapatsidwa kwa wa Mboni amene amathera nthawi yambiri mwezi uliwonse akulalikira. Ndimaona kuti ndinasankha bwino kwambiri chifukwa izi zinandithandiza kuti ndilimbitse ubwenzi wanga ndi Yehova komanso kuti ndizikhalako wamphamvu. Utumiki umenewu unandithandiza kuti ndiziuza anthu zimene ndimakhulupirira komanso kuti ndithandize ena kukhala mabwenzi a Mulungu.

YEHOVA SANANDITAYE

Mu 2001, ndinachita ngozi yoopsa yapamsewu ndipo miyendo yanga yonse inathyoka. Ndili m’chipatala, ndikumva ululu woopsa, ndinapemphera chamumtima kuti: “Yehova chonde musanditaye.” Nditangomaliza, mzimayi amene anali pafupi ndi bedi langa anandifunsa kuti, “Kodi anti, ndinu a Mboni?” Ndinalibiretu mphamvu zoti ndiyankhe, moti ndinangogwedeza mutu. Ndiyeno mayiyu anati, “Ndinadziwa. A Mboni za Yehova ndimakudziwani komanso ndimakonda kuwerenga magazini anu.” Mawu amenewo anandilimbikitsa kwambiri. Ndinaona kuti ndi chinthu chamtengo wapatali kuti ngakhale ndinali mu ululu woopsa, ndinakwanitsa kuchitira umboni za Yehova.

Nditayamba kupezako bwino, ndinaganiza zoyamba kuuza anthu muwodimo, uthenga wa m’Baibulo. Mayi anga ankandiyendetsa m’mabedi a anthu odwala, miyendo yanga ili m’chikhakha. Tsiku lililonse ndinkalalikira kwa anthu angapo. Ndinkawafunsa mmene alili,  kenako n’kuwapatsa mabuku othandiza kuphunzira Baibulo. Kuchita zimenezi kunali kotopetsa kwambiri komabe Yehova ankandipatsa mphamvu.

Ndili ndi makolo anga, mu 2003

Panopa vuto langa lawonjezereka komanso kumwalira kwa bambo anga kunandiwonjezera nkhawa. Komabe ndimayesetsa kuti ndisamangoganizira za mavuto angawa. Ndikaona kuti ndingakwanitse, ndimacheza ndi abale anga komanso anzanga n’cholinga choti ndiziiwalako mavuto anga. Ndikakhala ndekha, ndimawerenga Baibulo komanso kuuza anthu ena uthenga wa m’Baibulo pafoni.

Nthawi zambiri ndimatsinzina n’kumayerekezera kuti ndili m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza

Ndimakondanso kusangalala ndi zinthu zachilengedwe monga, kamphepo kayaziyazi komanso fungo losangalatsa la maluwa. Zimenezi zimandithandiza kuti ndiziyamikira Yehova. Ndimakondanso kuchita nthabwala ndipo izi zimandithandizanso kuti ndizisangalala. Mwachitsanzo tsiku lina ndikulalikira, mnzanga amene ankandiyendetsa anasiya kaye njinga yanga kuti alembe zinazake. Koma njinga yanga inayamba kutsetsereka mpaka ndinakagunda galimoto ina imene inaimikidwa pamalo ena. Zimenezi zinatichititsa mantha kwambiri koma titaona kuti sindinavulale, tonse tinayamba kuseka kwambiri.

Pali zinthu zambiri zimene sindingathe kuchita. Koma ndimadziuza kuti m’tsogolo ndidzakwanitsa kuchita zimenezi. Nthawi zambiri ndimatsinzina n’kumayerekezera kuti ndili m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza. (2 Petulo 3:13) Ndimaganiza mmene ndidzasangalalire ndikadzakhala ndi thanzi labwino, kumayenda komanso kumatha kuchita chilichonse bwinobwino. Ndimaganizira kwambiri mawu a Mfumu Davide akuti: “Yembekezera Yehova. Limba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu.” (Salimo 27:14) Ngakhale kuti panopa thupi langa ndi lofooka kwambiri, Yehova amandipangitsa kuti ndikhale wamphamvu. Ndimaona kuti mavuto anga andithandiza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.

^ ndime 6 Nyamakaziyi nthawi zambiri imagwira ana. Zimene zimachitika ndi zoti, chitetezo cha m’thupi chimaukira mtundu winawake wa maselo ndipo izi zimachititsa kuti munthu azimva kupweteka m’malo olumikizirana mafupa komanso kuti malowa azitupa.