Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGATANI KUTI MUZISANGALALA NDI NTCHITO YANU?

Kodi Kugwira Ntchito Mwakhama Ndi Kwachikale?

Kodi Kugwira Ntchito Mwakhama Ndi Kwachikale?

Alex amagwira ntchito pakampani inayake yonyamula katundu. Tsiku lina atatopa kwambiri ndi ntchito yake, anapumira m’mwamba n’kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimadzivutitsiranji kugwira ntchito yopanda tsogolo ngati imeneyi? Mwinanso ndikanakhala kuti sindikugwira ntchitoyi, bwenzi ndikusangalala kuposa panopa.’

Mofanana ndi Alex, anthu ambiri sasangalala ndi ntchito yawo. Pa mfundo imeneyi, munthu wina yemwe amagwira ntchito yokonza magalimoto, dzina lake Aaron anati: “Anthu ambiri safuna kugwira ntchito monga yokonza magalimoto chifukwa amaiona ngati yonyozeka. Akamagwira ntchito zoterezi amakhala ndi maganizo akuti, ‘Ndikungogwira poti ndi yomwe yapezeka, ndikadzapeza yabwino ndidzaisiya.’”

N’chifukwa chiyani anthu ambiri safuna kugwira ntchito zooneka ngati zonyozeka? Mwina n’chifukwa choti amayendera maganizo amene otsatsa malonda amalimbikitsa akuti, munthu amene zikumuyendera bwino ndi amene sagwira ntchito yokhetsa thukuta, koma n’kumapeza ndalama zambiri. Matthew, yemwe amagwira ntchito yosamalira nyumba, anati: “Anthu ambiri amaganiza kuti, ngati ukuchita kukhetsa thukuta kuti upeze ya mchere, ndiye kuti sizikukuyendera.” Munthu winanso, dzina lake Shane, anati: “Anthu ambiri sagwira ntchito molimbika komanso mokhulupirika. Koma mwezi ukatha amayembekezera kulandira malipiro onse.”

Komabe pali anthu ena amene amagwira ntchito mwakhama ndipo zinthu zikuwayendera bwino. Mwachitsanzo Daniel, yemwe ali ndi zaka 25 ndipo amagwira ntchito ya zomangamanga, anati: “Ukagwira ntchito mwakhama umasangalala, makamaka ngati wachita zimenezo ndi zolinga zabwino.” Nayenso Andre yemwe ali ndi zaka 23 anati: “Kugwira ntchito kumathandiza munthu kuti azisangalala. Anthu amaganiza kuti ngati atamagwira ntchito kwa nthawi yochepa kwinaku n’kumangokhala, akhoza kumasangalala. Koma zimenezi si zoona chifukwa ukakhala nthawi yaitali wosagwira ntchito, umayamba kunyong’onyeka.”

Kodi n’chiyani chimathandiza anthu ngati Daniel komanso Andre kuti azisangalala ndi ntchito yawo? N’chifukwa choti amayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wawo. Baibulo limatilimbikitsa kuti tiziona kuti kugwira ntchito n’kofunika komanso tiziigwira mwakhama. Limatiuzanso zimene tingachite kuti tizisangalala ndi ntchito yathu.

Kodi ndi mfundo ziti za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni kuti muzisangalala ndi ntchito yanu? Nkhani yotsatira ikufotokoza zina mwa mfundo zimenezi.