Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGAKONDE KUPHUNZIRA BAIBULO?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuphunzira Baibulo?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuphunzira Baibulo?
  • Kodi Mulungu anatilengeranji?

  • N’chifukwa chiyani timavutika komanso kufa?

  • Kodi m’tsogolomu mudzachitika zotani?

  • Kodi Mulungu amadera nkhawa za ine?

Kodi inunso nthawi zina mumakhala ndi mafunso amenewa? Ngati ndi choncho, dziwani kuti si inu nokha. Anthu ambiri amafuna atadziwa mayankho a mafunso amenewa ndi enanso ambiri. Koma kodi n’zotheka kupeza mayankho a mafunsowa?

Anthu ambiri angayankhe kuti inde n’zotheka, chifukwa anthuwa anapeza mayankho a m’Baibulo a mafunsowa. Ngati nanunso mukufuna kudziwa mayankho a mafunso amenewa, tikukulimbikitsani kuti muyambe kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova kwaulere. *

Komabe ambiri amaona kuti sangapeze nthawi yophunzira Baibulo. Enanso amaona kuti kuphunzira Baibulo n’kovuta kwambiri. Pomwe ena amaopa kupangana ndi wa Mboni kuti aziwaphunzitsa Baibulo chifukwa amaona kuti zimenezi ziziwapanikiza. Koma ena salola kuti zimenezi ziwalepheretse kuphunzira Baibulo. Taonani zitsanzo zotsatirazi:

  • Mayi ena a ku England, dzina lawo a Gill, anati: “Ndili ku yunivesite ndinkaphunzira zokhudza Mulungu. Komanso ndinapempherapo m’chipembedzo chachisiki, chachibuda komanso m’matchalitchi osiyanasiyana. Koma sindinapeze mayankho a mafunso anga. Ndiyeno tsiku lina, wa Mboni za Yehova wina anabwera kunyumba kwathu. Wamboniyo anayankha mafunso anga onse pogwiritsa ntchito Baibulo. Chifukwa cha zimenezi ndinavomera kuti azindiphunzitsa Baibulo.”

  • Bambo ena a ku Benin, dzina lawo a Koffi, anati: “Ndinali ndi mafunso ambirimbiri, koma zimene abusa a kutchalitchi kwathu ankandiyankha, sizinkandigwira mtima. Koma wa Mboni wina anayankha mafunso anga onse pogwiritsa ntchito Baibulo. Atandifunsa ngati ndingakonde kuphunzira Baibulo kuti ndidziwe zambiri, ndinavomera.”

  • A José, a ku Brazil, anati: “Ndinkafuna nditadziwa zimene zimachitika munthu akamwalira. Ndinkakhulupirira kuti akufa angathe kuchitira anthu amoyo zinthu zoipa, komabe ndinkafuna nditadziwa zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi. Choncho, ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi mnzanga wina yemwe anali wa Mboni.”

  • Mayi ena a ku Mexico, dzina lawo a Dennize, anati: “Ndinkawerenga Baibulo koma sindinkalimvetsa. Kenako a Mboni za Yehova anabwera kwathu ndipo anandifotokozera momveka bwino maulosi angapo a m’Baibulo. Ndinkafuna kudziwa zambiri, choncho ndinavomera kuti azindiphunzitsa Baibulo.”

  • A Anju, a ku Nepal, anati: “Ndinkafuna kudziwa ngati Mulungu amandiganizira kapena ayi. Choncho, ndinaganiza zopemphera kwa Mulungu yemwe amatchulidwa m’Baibulo. Tsiku lotsatira, kunyumba kwathu kunabwera a Mboni ndipo atandipempha kuti ndiziphunzira nawo Baibulo, ndinavomera.”

Zimene anthuwa ananenazi zikutikumbutsa mawu a Yesu akuti: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.” (Mateyu 5:3) Mwachibadwa, anthufe timafuna kudziwa Mulungu ndipo Mulungu watipatsa Mawu ake, Baibulo. Choncho tiyenera kuphunzira Baibulo kuti timudziwe bwino Mulungu.

Koma kodi phunziro la Baibulo limachitika bwanji? Nanga kuphunzira Baibulo kungakuthandizeni bwanji? Mafunso amenewa ayankhidwa m’nkhani yotsatira.

^ ndime 8 Baibulo limati dzina la Mulungu ndi Yehova.