Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tiziyembekezera Kuti Zinthu Zidzakhala Bwino M’tsogolo

Tiziyembekezera Kuti Zinthu Zidzakhala Bwino M’tsogolo

 Kodi mukuganiza kuti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolomu? Anthu ambiri amayesetsa kuganiza choncho ngakhale kuti panopa tikukumana ndi mavuto ambiri. Koma kodi m’pomvekadi kuyembekezera kuti zinthu zidzasintha n’kukhala bwino m’tsogolo? Inde. Baibulo limalonjeza kuti zinthu zidzakhaladi bwino m’tsogolo.

 Kodi Baibulo limalonjeza zotani?

 Baibulo limavomereza kuti anthufe timakumana ndi mavuto ambiri. Koma limalonjeza kuti mavutowa adzatha. Mavuto ena amene adzathe ndi awa:

  •   Vuto: Kusowa nyumba

     Zimene Baibulo limanena: “Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo.”​—Yesaya 65:21.

     Zimene tingayembekezere m’tsogolo: Anthu onse adzakhala ndi nyumba yawoyawo.

  •   Vuto: Kusowa ntchito komanso umphawi

     Zimene Baibulo limanena: “Anthu anga osankhidwa mwapadera adzapindula mokwanira ndi ntchito ya manja awo.”​—Yesaya 65:22.

     Zimene tingayembekezere m’tsogolo: Anthu onse adzakhala ndi ntchito yabwino komanso yosangalatsa.

  •   Vuto: Zinthu zopanda chilungamo

     Zimene Baibulo limanena: “Mfumu idzalamulira mwachilungamo.”​—Yesaya 32:1.

     Zimene tingayembekezere m’tsogolo: Palibe amene adzachitiridwe zinthu zopanda chilungamo chifukwa choti alibe ndalama, ndi wosaphunzira kapena chifukwa cha mtundu wake. Onse adzachitiridwa mwachilungamo.

  •   Vuto: Matenda osowa zakudya m’thupi komanso njala

     Zimene Baibulo limanena: “Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.”​—Salimo 72:16.

     Zimene tingayembekezere m’tsogolo: Anthu onse adzakhala ndi chakudya chopatsa thanzi chokwanira. Palibe amene adzagone ndi njala kapena kudwala matenda osowa zakudya m’thupi.

  •   Vuto: Uchigawenga ndi zachiwawa

     Zimene Baibulo limanena: “Aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu ndipo sipadzakhala wowaopsa.”​—Mika 4:4.

     Zimene tingayembekezere m’tsogolo: Aliyense adzakhala wotetezeka chifukwa anthu oipa adzakhala kulibe ndipo ‘olungama ndi amene adzakhale padziko lapansi.’​—Salimo 37:10, 29.

  •   Vuto: Nkhondo

     Zimene Baibulo limanena: “Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.”​—Yesaya 2:4.

     Zimene tingayembekezere m’tsogolo: Padziko lonse padzakhala mtendere. (Salimo 72:7) Palibe amene adzalire chifukwa cha munthu yemwe waphedwa pankhondo kapena amene adzathawe kwawo chifukwa cha nkhondo.

  •   Vuto: Matenda ndi miliri

     Zimene Baibulo limanena: “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”​—Yesaya 33:24.

     Zimene tingayembekezere m’tsogolo: Anthu sadzakhalanso olumala kapena kudwala. (Yesaya 35:5, 6) Baibulo limalonjezanso kuti ngakhale “imfa sidzakhalaponso.”​—Chivumbulutso 21:4.

  •   Vuto: Kuwononga chilengedwe

     Zimene Baibulo limanena: “Chipululu ndi malo opanda madzi zidzasangalala. Dera lachipululu lidzakondwa ndipo lidzachita maluwa n’kukhala lokongola ngati duwa la safironi.”​—Yesaya 35:1.

     Zimene tingayembekezere m’tsogolo: Dziko lonse lidzakhala lokongola kwambiri ngati mmene Mulungu ankafunira poyamba.​—Genesis 2:15; Yesaya 45:18.

 Kodi malonjezo a m’Baibulo adzakwaniritsidwadi?

 Mwina zingakuvuteni kukhulupirira kuti malonjezowa angakwaniritsidwe. Koma tikukulimbikitsani kuti muziphunzira bwinobwino zimene Baibulo limanena zokhudza m’tsogolo. N’chifukwa chiyani tikutero? Malonjezo a m’Baibulo ndi osiyana ndi malonjezo kapena maganizo a anthu. Malonjezo a m’Baibulo ndi ochokera kwa Mulungu. Choncho tingawakhulupirire pa zifukwa izi:

  •   Mulungu ndi wodalirika. Baibulo limanena kuti Mulungu “sanganame.” (Tito 1:2) Komanso Mulungu yekha ndi amene anganeneretu za m’tsogolo. (Yesaya 46:10) M’Baibulo muli zitsanzo zambiri zosonyeza kuti zimene Mulungu amaneneratu zinachitikadi. Kuti mudziwe zambiri pa nkhaniyi, onerani vidiyo yakuti Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona?

  •   Mulungu ali ndi mphamvu zothetsera mavuto athu. Baibulo limanena kuti Mulungu ali ndi mphamvu zochitira ‘chilichonse chimene akufuna kuchita.’ (Salimo 135:5, 6) M’mawu ena tinganene kuti palibe chimene chingalepheretse Mulungu kuti akwaniritse malonjezo ake. Kuwonjezera pamenepa, Mulungu amafunitsitsa kutithandiza chifukwa choti amatikonda.​—Yohane 3:16.

 Koma mungadzifunse kuti, ‘Ngati Mulungu amafuna kutithandiza komanso ali ndi mphamvu zotithandizira, kodi n’chifukwa chiyani timakumanabe ndi mavuto ambiri?’ Kuti mupeze yankho la funsoli, onerani vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?

 Kodi malonjezowa adzakwaniritsidwa bwanji?

 Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumu wake, womwe ndi boma lakumwamba, kuti akwaniritse malonjezo ake. Iye anasankha Yesu Khristu kuti akhale Wolamulira wa Ufumuwo ndipo wamupatsa ulamuliro wosamalira dzikoli ndi anthu okhala padzikoli. Yesu ali padzikoli, anachiritsa odwala, kudyetsa anjala, kulamulira nyengo komanso anaukitsa akufa. (Maliko 4:39; 6:41-44; Luka 4:40; Yohane 11:43, 44) Pochita zimenezi, anasonyeza zimene adzachite monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.

 Kuti mudziwe zimene Ufumu wa Mulungu udzachite pokuthandizani, onerani vidiyo yakuti Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

 Kodi malonjezowa adzakwaniritsidwa liti?

 Adzakwaniritsidwa posachedwapa. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Baibulo linaneneratu zinthu zimene zizidzachitika Ufumu wa Mulungu utatsala pang’ono kuyamba kulamulira dzikoli. (Luka 21:10, 11) Zinthu zimene zikuchitika padzikoli masiku ano zikufanana ndi zimene Baibulo linaneneratu.

 Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti “Kodi Ufumu wa Mulungu Udzayamba Liti Kulamulira Dzikoli?

 Kodi malonjezo a m’Baibulo angakuthandizeni bwanji panopa?

 Munthu wina amene analemba nawo Baibulo anayerekezera chiyembekezo chathu chochokera kwa Mulungu ndi “nangula wa miyoyo yathu.” (Aheberi 6:19) Mofanana ndi mmene nangula amathandizira sitima kuti isatengeke ndi mphepo, malonjezo a m’Baibulo angatithandize kuti tipirire mavuto athu. Malonjezowa angatithandize kuti mtima wathu ukhale m’malo, tiziganiza bwino komanso kuti tikhale athanzi.​—1 Atesalonika 5:8.