Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 103

Abusa Ndi Mphatso

Abusa Ndi Mphatso

(Aefeso 4:8)

  1. 1. Yehova watipatsa mphatso,

    Abusa mu mpingo.

    Mwachitsanzo chawo chabwino

    Amatiphunzitsa.

    (KOLASI)

    M’lungu watipatsa akulu

    Omwe timadalira.

    Amadera nkhawa tonsefe

    Ndiye tiziwakonda.

  2. 2. Abusawa ndi achikondi,

    Amaleza mtima.

    Tikapunthwa amathandiza

    Kutitu tichire.

    (KOLASI)

    M’lungu watipatsa akulu

    Omwe timadalira.

    Amadera nkhawa tonsefe

    Ndiye tiziwakonda.

  3. 3. Amatipatsa malangizo,

    Tisasocheretu.

    Tizisangalatsa Mulungu

    Pomutumikira.

    (KOLASI)

    M’lungu watipatsa akulu

    Omwe timadalira.

    Amadera nkhawa tonsefe

    Ndiye tiziwakonda.