NYIMBO 110
“Chimwemwe Chimene Yehova Amapereka”
-
1. Zizindikiro zasonyeza kuti
Ufumu wayandikira.
Chipulumutso chayandikiradi.
Tukulani mitu yanu.
(KOLASI)
Chimwemwe chochoka kwa Yehova
Ndi malo achitetezo.
Imbani mofuula ndi chimwemwe
Chifukwa cha chiyembekezo.
Chimwemwe chochoka kwa Yehova
Ndi malo achitetezo.
Tilambire M’lungu modzipereka.
Tim’tumikire mwachimwemwe.
-
2. Inu nonse okondadi Yehova
Muzimukhulupirira.
Imirirani ndipo fuulani.
Imbani mosangalala.
(KOLASI)
Chimwemwe chochoka kwa Yehova
Ndi malo achitetezo.
Imbani mofuula ndi chimwemwe
Chifukwa cha chiyembekezo.
Chimwemwe chochoka kwa Yehova
Ndi malo achitetezo.
Tilambire M’lungu modzipereka.
Tim’tumikire mwachimwemwe.
(Onaninso 1 Mbiri 16:27; Sal. 112:4; Luka 21:28; Yoh. 8:32.)