Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 133

Lambirani Yehova Mudakali Achinyamata

Lambirani Yehova Mudakali Achinyamata

(Mlaliki 12:1)

  1. 1. Anyamata ndi atsikanafe

    Ndife ofunika kwa Mulungu.

    Tikamam’tumikira mwakhama

    Azitidalitsa nthawi zonse.

  2. 2. Timasonyeza chikondi chathu

    Tikamalemekeza makolo.

    Anthu ndi M’lungu amatikonda

    Ndipo timayandikira M’lungu.

  3. 3. Tizikumbukira M’lungu wathu.

    Tikonde choonadi kwambiri.

    Tikakhulupirika kwa iye

    Tizisangalatsa mtima wake.