Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 2

‘Dzina Lanu Ndi Yehova’

‘Dzina Lanu Ndi Yehova’

(Salimo 83:18)

  1. 1. Mulungu woona,

    Mlengi wa zinthu zonse.

    Mulungu wamuyaya,

    Ndinudi Yehova.

    Timasangalala

    Kukhala anthu anu.

    Tilengeze za inu

    Ku mitundu yonse.

    (KOLASI)

    Yehova, Yehova,

    M’lungu ndinu nokha.

    Kumwambako ndi padziko

    Palibenso wina.

    Ndinudi wamphamvuyonse,

    Tidziwitse onse.

    Yehova, Yehova,

    M’lungu wathu ndinu nokha.

  2. 2. Tingathe kukhala

    Chimene mukufuna.

    Mumatithandizatu

    Ndinudi Yehova.

    Mwatipatsa dzina

    Takhala Mboni zanu.

    Ndifedi anthu anu.

    Timakukondani.

    (KOLASI)

    Yehova, Yehova,

    M’lungu ndinu nokha.

    Kumwambako ndi padziko

    Palibenso wina.

    Ndinudi wamphamvuyonse,

    Tidziwitse onse.

    Yehova, Yehova,

    M’lungu wathu ndinu nokha.