Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Madalitso Ophunzira Chinenero China

Madalitso Ophunzira Chinenero China

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Mwina m’maganizira,

    Za chilankhulo china.

    Mwinanso m’mapemphera,

    ‘Yehova M’lungu nditani?’

    Choncho tilankhulepo

    Kutitu m’sankhe bwino.

    Mukasankha kuwoloka,

    Inu m’dzasangalala.

    (KOLASI)

    Sankhani kuwoloka

    Ndipo m’sadere nkhawa.

    Pajatu m’kawoloka,

    Mudzadalitsidwa, o.

    Wolokerani.

    Wolokerani ku Makedoniya!

  2. 2. Ntchitoyi yolalikira,

    Imatikhudza mtima.

    Mudzadabwa kuona

    Anthu akumvetsera.

    Mudzayandikira M’lungu

    Moyo wanu wonse.

    Chifukwa ’dzakuthandizani

    Kuphunzira nthawi zonse.

    (KOLASI)

    Sankhani kuwoloka

    Ndipo m’sadere nkhawa.

    Pajatu m’kawoloka,

    O, m’dzapeza chuma.

    Mwina mukusinkhasinkha

    Zoti muwoloke, o.

    (KOLASI)

    Sankhani kuwoloka

    Mudzadalitsidwa, o.

    Wolokerani.

    Wolokerani.

    Chotero wolokerani ku Makedoniya!