Pitani ku nkhani yake

Kuona Malo ku Beteli

Tikukuitanani kuti mudzaone maofesi athu a nthambi omwenso amadziwika kuti Beteli. Ku maofesi athu ena kulinso malo achionetsero omwe mukhoza kuona nokha popanda wokutsogolerani.

Kuyambiranso Kuona Malo: M'mayiko ambiri, anthu adzayambiranso kuona malo m'maofesi athu a nthambi kuyambira pa 1 June, 2023. Kuti mudziwe zambiri, lankhulani ndi abale a ku nthambi yomwe mukufuna kukaonayo. Komabe, musapite kukaona malo ngati mwapezeka ndi COVID-19 kapena ngati muli ndi zizindikiro za chimfine kapenanso ngati posachedwapa munakumana ndi munthu amene wapezeka ndi COVID-19.

Slovakia

Pekna cesta 17

831 52 BRATISLAVA 34

SLOVAK REPUBLIC

+421 2-49107611

Kuona Malo

Lolemba mpaka Lachisanu

8:00 a.m. mpaka 10:30 a.m. ndi 1:00 p.m. mpaka 3:30 p.m.

Nthawi yonse: Ola limodzi ndi hafu

Zimene Timachita

Timayang’anira ntchito imene Mboni za Yehova zoposa 26,500 zikugwira ku Czech Republic ndi Slovakia. Timamasulira mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo m’Chislovaki ndiponso m’Chinenero Chamanja cha ku Slovakia. Timatumiza mabuku m’mipingo ya ku Austria, Czech Republic, Slovakia ndi Slovenia.

Koperani pepala losonyeza ofesi yathu.