Pitani ku nkhani yake

Anakwanitsa Kuzimitsa Moto

Anakwanitsa Kuzimitsa Moto

Tsiku lina m’mawa, Sandra akumwa tiyi kwa apongozi ake anangoona moto ukuyaka m’kanyumba kosungiramo zinthu komwe kali pafupi ndi nyumba yaikulu. Iye anakuwa kuti: “Moto! Moto kuno!” Sandra ndi mwamuna wake Thomas anayamba kuzimitsa motowo mwamsanga. Sandra anatenga chozimitsira moto ndipo Thomas anathamanga kuti akaone kanyumba kamayaka motoko. Kenako Sandra anapatsira Thomas chozimitsira motocho ndipo anauzimitsa. Iye anati: “Tikanapanda kuuzimitsa mwachangu, kanyumba konse kakanayaka.”

Kodi n’chiyani chinathandiza Thomas ndi Sandra kuti asachite mantha n’kuzimitsa motowo mwachangu? Iwowa limodzi ndi anzawo ena 1,000, amatumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Selters m’dziko la Germany ndipo anaphunzitsidwa zimene angachite pakabuka moto.

Malo omwe pali ofesi ya nthambi ku Selters ndi aakulu mahekitala 30. Malowa sikuti ali ndi maofesi komanso nyumba zogona zokha, koma alinso ndi malo ochapira zovala, malo osindikizira mabuku komanso malo ogwirira ntchito zosiyanasiyana, ndipo m’malo onsewa muli zinthu zomwe sizingachedwe kugwira moto. Choncho, dipatimenti yothandiza anthu kupewa ngozi (Safety and Environment Department) yomwe ili pa nthambiyi, inakhazikitsa pulogalamu yophunzitsa anthu mmene angapewere ngozi ya moto. Choyamba gulu lina lomwe limathandiza pakachitika ngozi zamwadzidzidzi (Emergency Response Team) limayeserera mmene lingazimitsire moto pamodzi ndi dipatimenti yozimitsa moto ya m’derali. Kenako, nthawi ndi nthawi anthu onse amene amatumikira pa nthambiyi amachita zinthu zotsatirazi:

  • Kuyeserera mmene angathawire pakabuka moto.

  • Kuphunzira mmene angapewere zinthu zoyambitsa moto.

  • Kuphunzira mmene angazimitsire moto ukangoyamba kumene.

Zimenezi zimathandiza anthu omwe amatumikira pamalowa kuti aphunzire zinthu zofunikira kuchita pakabuka moto.

Kuyeserera Njira Yabwino Yozimitsira Moto

Pa nthawi yoyeserera, anthu amaphunzira mmene angazimitsire moto popanda kuchita ngozi. A Christin omwe anaphunzirapo mmene angazimitsire moto kupulayimale anayamikira zimene anaphunzira pa ofesi ya nthambi ndipo anati: “Ndinatenga chozimitsira moto, kuchitsegula kenako ndinayamba kuzimitsa moto moyang’anitsa chozimitsiracho kumbali yomwe sikukuchokera mphepo. Ndikanachiyang’anitsa komwe kukuchokera mphepo, malawi a moto akanandiwotcha kunkhope. Ndipo ndinakwanitsa kuzimitsa motowo ndekha. Ndinaphunziranso mmene ndingazimitsire moto limodzi ndi gulu la anthu 4 kapena 5.”

A Daniel omwe amaphunzitsa anthu mmene angapewere ngozi za moto pa ofesi ya nthambi, ananena kuti kuyeserera kumathandiza kuti anthu “asamaope kwambiri kuzimitsa moto.” Iwo ananenanso kuti: “Moto ukayamba nthawi zambiri anthu amasowa chochita. Pa nthawiyi amachita mantha kwambiri ndipo amadzifunsa kuti, ‘Ndiye titani pamenepa? Chozimitsira motochi tichigwiritsa ntchito bwanji?’ Koma akadziwa zoyenera kuchita, sangavutike kuzimitsa moto womwe wangoyamba kumene kuti usakule n’kufika powononga zinthu zambiri.” A Daniel anafotokozanso kuti pa nthawi imene anthuwa akuphunzira, “onse amaphunzira mmene angagwirire mosamala chozimitsira moto kuti athe kuzimitsa bwinobwino moto wadzidzidzi. Amathanso kuchita zinthu molimba mtima kuti azitha kuchitapo kanthu mwamsanga moto ukabuka.”

Maphunziro Ozimitsa Moto ndi Othandiza

Anthu ambiri anayamikira maphunzirowa. A Christin, omwe tawatchula koyamba aja anati: “Kanali koyamba kuti ndigwiritse ntchito chozimitsira moto. Ndikuona kuti aliyense ayenera kuphunzira zimene ife taphunzirazi.” A Nadja nawonso anayamikira kwambiri maphunzirowa. Iwo amagwira ntchito ku bwalo la ndege koma masiku ena amadzatumikira pa ofesi ya nthambi ndipo anati: “Ndakhala ndikungophunzira za mmene tingazimitsire moto kuntchito kwathu kwa zaka 10. Koma ku nthambi kuno tikaphunzitsidwa timayesereranso mmene tingazimitsire moto ndipo zimenezi zandithandiza kuti ndisamachite mantha. Panopa ndikudziwa zoyenera kuchita moto utati wabuka.”

Sandra amaona kuti maphunziro ozimitsa moto omwe amaphunzira ku ofesi ya nthambi ndi amene anamuthandiza kuti azimitse msanga moto kwa apongozi ake. Iye anati: “Panopa sindimaopa kugwiritsa ntchito chozimitsira moto. Kunena zoona maphunziro amene timakhala nawo chaka ndi chaka andithandiza kwambiri.”

Kuyeserera Kuzimitsa Moto Limodzi ndi Ozimitsa Moto a Boma a M’derali

Dipatimenti yozimitsa moto ya m’dera la Selters imapita pafupipafupi ku ofesi ya nthambi kukayeserera kuzimitsa moto. Mkulu wa dipatimentiyi a Theo Neckermann anafotokoza chifukwa chimene amachitira zimenezi ndipo anati: “Dipatimenti yathu ndi imene imafunika kuzimitsa moto m’dera lonse la Selters lomwe lili chakumidzi. Nthawi zambiri timazimitsa moto m’nyumba za anthu. Koma ku ofesi ya nthambi kuno n’kosiyana ndi malo ena onse chifukwa malo ake ndi aakulu, kuli nyumba zikuluzikulu ndiponso kumachitika ntchito zosiyanasiyana. Ndiye tikufunika kukhala aluso kwambiri kuti tithe kuzimitsa moto pamalo ano. Choncho, timasangalala kwambiri kuti timakhala ndi mwayi wodzayeserera kunoko.”

Anthu oposa 100 omwe amathandiza pakachitika ngozi zamwadzidzidzi (Emergency Response Team), amayeserera mmene angapulumutsire anthu komanso mmene angathawire pakabuka moto limodzi ndi a m’dipatimenti yozimitsa moto ya m’derali. A Neckermann anati: “Timasirira gulu lanu limene limathandiza pakachitika ngozi zamwadzidzidzi. Popanda kuthandizidwa ndi gululi, ntchito yoyeserera kupulumutsa anthu pakabuka moto ndi mmene angathawire si bwenzi ikuyenda bwino.”

Akusonyeza kuopsa kozimitsa moto wa mafuta ndi madzi

Tsiku lina madzulo mu February 2014, dipatimenti yozimitsa moto ya m’derali komanso othandiza pakachitika ngozi zamwadzidzidzi a pa Beteli anasonyeza luso lawo. Mbali ina ya imodzi mwa nyumba yomwe ili ndi zipinda zogona pa nthambiyi inadzadza utsi. A Daniel omwe tawatchula kale aja anati: “Utsiwo unali wochuluka kwambiri moti sitinkatha kuona manja athu tikawayandikizitsa kunkhope zathu. Nthawi yomweyo tinadziwitsa dipatimenti yozimitsa moto ya m’derali ndipo anthu anayamba kutuluka m’zipinda zonse 88 za nyumbayi. Pamene ozimitsa motowo ankafika, tonse tinali titatuluka kale m’nyumbayi.” A Neckermann anati: “Sindimaganizira zoti mungakwanitse kutuluka m’nyumba yaikulu chonchi mofulumira kwambiri makamaka mu mzinda wa Frankfurt uno. Ndaona kuti anthu inu munaphunzitsidwa bwino ndiponso gulu lanu lothandiza pakachitika ngozi zamwadzidzidzi limadziwadi ntchito yake.” Anthu ozimitsa moto anazindikira chomwe ndinayambitsa utsiwo n’kuchichotsa. Palibe munthu aliyense amene anavulala kapenanso zinthu zomwe zinawonongeka kwambiri.

Anthu onse omwe amatumikira pa ofesi ya nthambi ku Selters akukhulupirira kuti pa ofesiyi sipangadzabuke moto wodetsa nkhawa. Komabe ngati utabuka, iwo ndi okonzeka kuuzimitsa chifukwa anaphunzira mmene angazimitsire moto.