Pitani ku nkhani yake

Tsiku Lapadera Lokaona Malo ku Steinfels

Tsiku Lapadera Lokaona Malo ku Steinfels

Padziko lonse, a Mboni za Yehova ali ndi maofesi osindikizira mabuku okwana 15. Imodzi mwa maofesiwa ndi ya Central Europe yomwe ili m’tawuni ya Steinfels m’dziko la Germany. M’Chijeremani, dzina lakuti Steinfels limatanthauza “Mwala.”

Pa May 23 mpaka 25, 2014, ofesi ya Mboni za Yehovayi inaitana anthu okhala pafupi, abizinezi ndiponso akuluakulu ena a boma a m’derali kuti adzaone malowa. Mwambo wapadera wodzaona malowa unali ndi mutu wakuti: “Takwanitsa Zaka 30 Tili ku Selters Kuno.” Anasankha mutuwu chifukwa a Mboni za Yehova anatsegulira malo osindikizira mabuku m’derali pa April 21, 1984.

Anthu oposa 3,000 anabwera kudzaona malowa. Ndipo meya wa mzindawu, yemwe wakhala paudindowu kwa zaka 30 anati: “Nthawi zonse ndimasangalala kwambiri ndikabwera kudzaona maofesi a Mboni za Yehova. Ndimachita chidwi kwambiri ndi mmene ntchito yomanga ofesiyi kuno ku Steinfels, yomwe inayambika mu 1979 mpaka 1984, inayendera mwachangu.”

Zimene Anthu Anaona

Pamalo ena oonetserapo zinthu panalembedwa kuti: “Anthu a Yehova ku Central Europe.” Alendowa anaona zinthu zimene a Mboni za Yehova a ku Central Europe akhala akuchita kwa zaka pafupifupi 120. Mpaka pano malowa adakalipobe pa ofesi ya Mboniyi.

Pamalo enanso ankaonetsapo Mabaibulo amene sapezeka kawirikawiri komanso ndi ofunika kwambiri. Mwachitsanzo, panali Baibulo lathunthu la m’Chijeremani lomwe linatuluka koyamba mu 1534 ndiponso Baibulo lokhala ndi zilankhulo 12 lomwe linamasuliridwa ndi Elias Hutter ndipo linatuluka koyamba mu 1599. Komanso panali zinthu zosiyanasiyana monga matchati ndiponso mavidiyo osonyeza kuti mfundo za m’Baibulo ndi zothandiza kwambiri masiku ano.

Anthuwa anayenda ulendo wa magawo awiri woona malo osiyanasiyana. Malowa ankasonyeza zochitika za pa ofesiyi komanso ntchito zimene anthu oposa 1,000 amagwira tsiku lililonse. Mutu wa gawo loyamba pa ulendowu unali wakuti, “Mmene Timakhalira,” ndipo alendowa anaona zipinda zogona za anthu a pa ofesiyi. Anthu onsewa anapita kuchipinda chodyera cha pa ofesiyi kukadya chakudya chamasana ndipo pambuyo pake ankayendayenda pamalowa. Mlendo wina anati: “Kunena zoona, malowa ndi okongola kwambiri.”

Gawo lachiwiri la ulendowu linali ndi mutu wakuti, “Ntchito Zosiyanasiyana.” Pagawoli anaona Dipatimenti Yosindikiza Mabuku, Yoikira Zikuto ndiponso Yotumiza Mabuku. Anthuwo anaona mmene amasindikizira mabuku, kuikira zikuto ndiponso kuwatumiza kumayiko oposa 50. Munthu wina ananena kuti: “Sindinkadziwa kuti mpingo wa Mboni za Yehova ndi gulu la anthu omwe ali padziko lonse. Mabuku awo amafika kulikonse padzikoli. Kunena zoona izi n’zodabwitsa chifukwa ntchitoyi ikugwiridwa ndi anthu ongodzipereka.”

Alendo akuphunzira mmene angagwiritsire ntchito webusaiti ya jw.org

Mbali inanso yochititsa chidwi inali yokhudza webusaiti yovomerezeka ya Mboni za Yehova ya jw.org. Gulu la anthuwo lomwe panali ana ndiponso akuluakulu anaonera mavidiyo osiyanasiyana ndipo anayankhidwa mafunso awo osiyanasiyana.

Anthu ambiri anachita chidwi ndipo anali osangalala ataona mmene ntchito ya Mboni za Yehova padziko lonse ikuyendera. Bambo wina anati: “Ndinali ndi maganizo olakwika okhudza a Mboni za Yehova koma tsopano ndifunika kuganiziranso bwino.” Mayi winanso ananena kuti: “Zimene taona lero zathetseratu tsankho limene tinali nalo.”

^ ndime 17 Ziwerengero za mu 2014

^ ndime 21 Ziwerengero za mu 2014

^ ndime 24 Ziwerengero za mu 2014