Pitani ku nkhani yake

“Akazi Angathe Kugwira Nawo Ntchito ya Zomangamanga”

“Akazi Angathe Kugwira Nawo Ntchito ya Zomangamanga”

Bungwe lina la ntchito zomangamanga ku Britain linathokoza a Mboni za Yehova chifukwa chophunzitsa akazi kuti azitha kuyendetsa zimagalimoto ndi mashini akuluakulu panthawi yomanga ofesi yawo yanthambi yatsopano yomwe ili kufupi ndi Chelmsford, ku Essex. Bungwe la Considerate Constructors Scheme * (CCS) linanena kuti a Mboni aposa mabungwe ena onse pa nkhani yophunzitsa akazi ntchito zomangamanga ndipo anati njira imeneyi ndi “yatsopano.” N’chifukwa chiyani ananena kuti a Mboni aposa mabungwe ena onse?

M’dziko la Britain, pa anthu 100 alionse ogwira ntchito zomangamanga, ndi azimayi 13 okha amene amagwira nawo ntchitoyi. Kampani ina ya ku Britain itapanga kafukufuku inapeza kuti azimayi ambiri sakonda kugwira ntchito zomangamanga. Komabe pa anthu omwe amagwira ntchito yomanga ku Chelmsford, pa anthu 100 alionse, 40 ndi azimayi. Chiwerengerochi chinakweranso kufika pa azimayi oposa 60 pa anthu 100 alionse.

Akazi akugwira ntchito limodzi ndi amuna ku Chelmsford

Kodi n’chiyani chimathandiza azimayi a Mboniwa kuti azikwanitsa kugwira ntchitoyi? Iwo amaphunzitsidwa bwino ndiponso amathandizidwa. Mfundo ziwirizi zilinso pa mndandanda wa malamulo a bungwe la Considerate Constructors Scheme. Malamulo awo amalimbikitsa makampani a zomangamanga kuti aziona anthu omwe akugwira ntchito pakampanipo kukhala ofunika. Iwo ayenera kuchita zimenezi poonetsetsa kuti pa “malo awo a ntchito aliyense akulemekezedwa, sakuchitiridwa nkhanza, akulimbikitsidwa ndi kuthandizidwa,” ndipo asamaiwalenso “kuphunzitsa anthu awo ntchito.”

Kuphunzitsa Akazi Kugwiritsa Ntchito Zimagalimoto ndi Mashini Akuluakulu

Jade ndi mmodzi mwa akazi omwe anaphunzitsidwa kuyendetsa mathirekitara ndi mashini ena. Iye anati: “N’zosangalatsa! Sindinkadziwa kuti ndingathe kuchita zimenezi. Nthawi zina ntchito yomwe tikufunika kugwira imakhala yovuta koma ndimaphunzitsidwa pafupipafupi ndipo ndimaphunzira zinthu zatsopano.” Nayenso Lucy pano wayamba kuyendetsa zimagalimoto ndi mashini akuluakulu. Ndipo anati: “Ndimakumbukira kuti nditangobwera kumene pamalo ano, ndinalibe luso lina lililonse lomwe ndikanatha kuligwiritsa ntchito. Koma ndinayamba kuphunzitsidwa kungoyambira tsiku lomwe ndinafika. Ndakhala ndikugwira ntchito ndi magulu osiyanasiyana 5 ndipo ndaphunzitsidwa zinthu zambiri m’magulu amenewa.”

Akuphunzitsidwa mmene angamayendetsere thirakitala yonyamulira zinthu

Akazi amene amagwira ntchito ndi maguluwa amakhala ndi maluso ambiri. Amene amayang’anira gulu lina dzina lake Eric ananena kuti: “Akazi amasamala kwambiri zinthu kuposa mmene amuna amachitira, ndipo savutika kuzindikira kuti mashini enaake ali ndi vuto ndipo amakanena za vutolo.”

Kuthandiza Akazi Pantchito ya Zomangamanga

Carl yemwe amatsogolera magulu osiyanasiyana ogwiritsa ntchito mashini akuluakulu anati: “Ndachita chidwi kwambiri ndi mmene azimayi aphunzirira kuyendetsa magalimoto akuluakulu. Ndipo nthawi zina ndimasankha azimayi kuti ayendetse zimagalimotozi m’malo mwa azibambo oti akhala akuziyendetsa kwa zaka zambiri.”

Akugwiritsa ntchito mashini olumikizira mapaipi a pulasitiki

Amene akutsogolera magulu akamayesetsa kuthandiza anthu amene akugwira nawo ntchito, zimathandiza kwambiri anthuwo kuti asamadziderere. Izi n’zimene zinachitikira Therese. Iye wakhala akugwiritsa ntchito mashini akuluakulu kwa zaka zambiri ndipo amadziwa kuti munthu amene akugwiritsa ntchito mashiniwa, ayeneranso kukhala wosamala kwambiri kuti apewe ngozi. Therese ananena kuti: “Ndikadziwa kuti amene amatitsogolera akundithandiza m’pamene ndimachita zambiri kuposa mmene ndikanachitira pandekha chifukwa ndimadziwa kuti munthu wina akundidalira. Komanso ndimagwira ntchito mwakhama kwambiri ndikadziwa kuti anthu amaona kuti ntchito yanga ndi yofunika komanso ngati amayamikira zomwe ndikuchita.”

Nayenso Abigail, amayendetsa magalimoto ndi mashiniwa ndipo anati: “Azibambo amene tikugwira nawo ntchito pano samandiona ngati wosafunika. Pakafunika kundithandiza amandithandiza m’malo mongopitiriza iwowo ntchitoyo. Amayesetsa kundithandiza mpaka ndimakwanitsa kugwira ntchitoyo.”

Akazi Amakhala Osamala Kwambiri

Akazi amene amagwira ntchito ku Chelmsford anaphunzitsidwanso kuti azitha kuyeza malo omwe tikufuna kumangapo, kuyesetsa kusamalira zinthu zapamalopo, kukonza mashini owonongeka, ndiponso kumanga malo okonzerapo mashini akuluakulu. Robert amene wakhala akugwira ntchito zosiyanasiyana ndi azimayi ananena kuti azimayi “amakhala osamala, odzipereka pogwira ntchito ndiponso amayesetsa kutsatira malangizo a mmene angagwirire ntchito.” Tom yemwe amagwira ntchito yoyeza malo anati: “Akazi amene ndimagwira nawo ntchito amakhala osamala kwambiri komanso zomwe ayeza zimakhala zolondola. Amaonetsetsa kuti asaphonyetse.”

Ndipotu n’zosadabwitsa kuti a Fergus omwe amayang’anira gulu loyeza malo ananena mosangalala kuti: “Kunena zoona akazi angathe kugwira nawo ntchito ya zomangamanga.”

^ ndime 2 Bungwe la Considerate Constructors Scheme ndi lodziimira palokha ndipo limagwira ntchito yothandiza pa ntchito zomangamanga m’dziko la Britain kuti zizikhala zamaonekedwe apamwamba.