Pitani ku nkhani yake

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

“Zochita Zanga Zoipa Komanso Kukonda Ndalama Zinandibweretsera Mavuto Ambiri”

“Zochita Zanga Zoipa Komanso Kukonda Ndalama Zinandibweretsera Mavuto Ambiri”
  • Chaka Chobadwa: 1974

  • Dziko: Albania

  • Poyamba: Anali wakuba, wozembetsa mankhwala osokoneza bongo komanso mkaidi

KALE LANGA

 Ndinabadwira m’banja losauka ku Tiranë, likulu la dziko la Albania. Bambo anga ankachita zinthu moona mtima ndipo ankagwira ntchito maola ambiri kuti azitipezera zofunika pa moyo. Komabe, nthawi zonse sitinkakhala ndi ndalama zokwanira kugula zinthu zofunikira. Ndili mwana, zinkandiwawa kwambiri kuti tinali osauka. Nthawi zambiri ndinkayenda opanda nsapato ndiponso chakudya chinkakhala choperewera.

 Ndinayamba kuba ndili wamng’ono kwambiri. Pa nthawiyo ndinkaganiza kuti ndikungothandizira kupeza zinthu zofunika pa banja lathu. Patapita nthawi apolisi anadzandigwira. Ndiyeno mu 1988 ndili ndi zaka 14, bambo anga ananditumiza kusukulu ya ana omwe anapalamula milandu. Kusukuluku ndinakhalako zaka ziwiri ndipo ndinaphunzira ntchito yowotchelera. Nditachokako ndinkafuna nditamachita zinthu moona mtima koma sindinkapeza ntchito. Pa nthawiyi anthu ambiri ku Albania sankapeza ntchito chifukwa cha mavuto azandale. Zimenezi zinandikhumudwitsa kwambiri moti ndinayambiranso kucheza ndi anzanga akale aja n’kuyambiranso kuba. Kenako ine ndi anzangawo tinamangidwa n’kugamulidwa kuti tikakhale kundende zaka zitatu.

 Nditatuluka m’ndende ndinapitiriza kupalamula milandu. Chuma cha dziko la Albania sichimayenda bwino moti zinthu zinali zitasokonekera kwambiri. Koma ineyo ndinkapeza ndalama zambiri chifukwa ndinkachita zinthu zambiri zachinyengo. Nthawi ina ine ndi anzanga titakaba moopseza ndi mfuti, anzanga awiri anamangidwa koma ine ndinathawira dziko lina poopa kukakhala kundende kwa nthawi yaitali. Pa nthawiyi n’kuti nditakwatirana ndi Julinda ndipo tinali ndi mwana wamwamuna.

 Tinathawira ku England ndipo ndinkafunitsitsa kumachita zinthu zabwino kuti ine, mkazi wanga ndi mwana wathu tiyambe kukhala moyo watsopano. Koma zinkandivutabe kusintha makhalidwe oipa. Pasanapite nthawi ndinapalamula mlandu wina. Pa nthawiyi ndinagwidwa ndikuzembetsa mankhwala osokoneza bongo komanso kupezeka ndi ndalama zambiri.

 Kodi Julinda ankamva bwanji chifukwa chakuti ndinkazembetsa mankhwala osokoneza bongo? Bwanji ndimulole ayankhe yekha: “Popeza kuti ndinakulira ku Albania, ndinkalakalaka nditakhala wolemera. Ndinkafunitsitsa kuyesera njira zosiyanasiyana zomwe zingathandize kuti moyo wanga usintheko. Ndinkaganiza kuti ndalama zithandiza kuti moyo wathu usinthe moti ndinagwirizana ndi zoti Artan azinama, kuba komanso kuzembetsa mankhwala osokoneza bongo, bola ngati akupanga ndalama.”

“Ndinagwirizana ndi zoti Artan azinama, kuba komanso kuzembetsa mankhwala osokoneza bongo.”—Julinda

 Kenako moyo wathu unasintha mwadzidzidzi mu 2002. Apatu zomwe tinkayembekezera kuti tikhala moyo wamwanaalirenji zija zinathera pomwepo. Ndinagwidwa ndi mankhwala osokoneza bongo ambiri ndipo ndinamangidwanso.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA

 Baibulo linayamba kusintha moyo wanga ndisanayambe n’komwe kuliphunzira. Chakumayambiriro kwa chaka cha 2000, Julinda anakumana ndi a Mboni za Yehova ndipo anayamba kuphunzira naye Baibulo. Ineyo sindinkafuna kuphunzira Baibulo chifukwa ndinkaona kuti ndi zobowa. Koma Julinda ankakonda kwambiri kuphunzira. Iye anafotokoza kuti: “Ndinakulira m’banja lokonda kupemphera ndipo Baibulo ndinkalikonda komanso kulilemekeza kwambiri. Ndinkafunitsitsa kudziwa zimene limaphunzitsa ndipo ndinasangalala kwambiri kuyamba kuphunzira ndi a Mboni. Zinthu zambiri zomwe ndinkaphunzira zinkandifika pamtima. Zimene ndinaphunzira zinandithandiza kusintha moyo wanga. Koma pa nkhani ya ndalama pokha ndinkaonabe kuti zingatithandize kukhala ndi moyo wosangalala. Ndiyeno Artan atamangidwa, ndinasinthiratu maganizo anga. Mwadzidzidzi ndinazindikira kuti zimene Baibulo limanena zokhudza ndalama n’zoona. Ifeyo ndiye tinayesetsa kusakasaka ndalama koma sizinatithandizepo kukhala osangalalala. Apatu ndinazindikira kuti ndinkafunika kutsatira mfundo za Mulungu ndi mtima wanga wonse.”

 Mu 2004, ndinatulutsidwa m’ndende koma posakhalitsa ndinayambiranso kuzembetsa mankhwala osokoneza bongo. Komabe, Julinda anali atasintha maganizo ndipo zimene ananena zinandichititsa kuti ndiganize mwanzeru. Iye anati: “Sindikufunanso ndalama zanu. Ndikufuna mubwererenso mwakale muja monga mwamuna wanga komanso bambo wa ana anga.” Ngakhale kuti mawu amenewa anandidzidzimutsa koma ankanena zoona. Banja langa linandisowa kwa zaka zambiri. Ndinaganiziranso mavuto amene ndinakumana nawo chifukwa chomangokhalira kufunafuna ndalama m’njira zachinyengo. Choncho ndinaganiza zosintha moyo wanga komanso kusiya kucheza ndi anzanga aja.

 Ndinasintha kwambiri nditapita kumisonkhano ya Mboni za Yehova limodzi ndi mkazi wanga komanso ana athu. Ndinachita chidwi kwambiri nditaona anthu achikondi chenicheni komanso ansangala. Patapita nthawi ndinayamba kuphunzira Baibulo.

Poyamba ndinkaganiza kuti ndalama zambiri zingatithandize kukhala osangalala

 Ndinaphunzira kuchokera m’Baibulo kuti “Kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse, ndipo pokulitsa chikondi chimenechi, ena . . . adzibweretsera zopweteka zambiri pathupi lawo.” (1 Timoteyo 6:9, 10) Ndinamvetsa kuti mfundo yapalembali ndi yoona. Ndinamva chisoni kwambiri ndi zimene ndinalakwitsa m’mbuyomu chifukwa zinabweretsa mavuto pa moyo wanga komanso m’banja langa. (Agalatiya 6:7) Ndinayamba kusintha umunthu wanga nditadziwa kuti Yehova ndi Mwana wake Yesu Khristu amatikonda kwambiri. M’malo momaganizira kwambiri zokhudza ineyo, ndinayamba kuganizira kwambiri anthu ena ndipo ndinayambanso kupeza nthawi yomacheza ndi banja langa.

PHINDU LIMENE NDAPEZA

 Ndapindula kwambiri chifukwa chotsatira mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.” (Aheberi 13:5) Panopa ndili ndi mtendere wam’maganizo komanso chikumbumtima choyera. Zimenezi zandithandiza kuti ndizikhala ndi chimwemwe chimene ndinali ndisanakhalepo nacho ndi kale lonse. Banja langa ndi lolimba ndipo timakondana kwambiri.

 Poyamba ndinkaganiza kuti ndalama zambiri zingatithandize kukhala osangalala. Koma panopa ndikuchita kuoneratu mmene kupalamula milandu komanso kukonda ndalama kunandibweretsera mavuto ambiri. Ngakhale kuti tilibe ndalama zambiri koma ndimamva kuti tinapeza chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu, chomwe ndi kukhala pa ubwenzi ndi Yehova Mulungu. Timasangalala kwambiri tikamamulambira limodzi monga banja.

Ndi banja langa pamsonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova