Pitani ku nkhani yake

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

“Misewu Ndi Imene Inali Nyumba Yanga”

“Misewu Ndi Imene Inali Nyumba Yanga”
  • Chaka Chobadwa: 1955

  • Dziko: Spain

  • Poyamba: Ankagwiritsa Ntchito Mankhwala Osokoneza Bongo, Kumwa Mowa Mwauchidakwa Komanso Ankachita Zachiwawa

KALE LANGA

 Anthu ena zimawatengera nthawi yayitali kuti aphunzirepo kanthu pa zoipa zimene zawachitikira pa moyo wawo. Ndi mmene ineyo ndinalili. Ndinabadwira komanso kukulira ku Barcelona, womwe ndi mzinda wachiwiri pamizinda ikuluikulu kwambiri m’dziko la Spain. Banja lathu linkakhala m’dera lotchedwa Somorrostro, lomwe limapanga mbali yayikulu ya madera omwe ali m’mphepete mwa nyanja. Dera la Somorrostro linkatchuka kwambiri ndi za uchifwamba komanso mankhwala osokoneza bongo.

 Makolo anga anali ndi ana 9, ndipo ineyo ndine woyamba kubadwa. Chifukwa chakuti tinali osauka kwambiri, bambo anga anandiuza kuti ndizikagwira ntchito yotolera mpira pa malo ena osewerera tenisi. Pa nthawiyo n’kuti ndili ndi zaka 10 ndipo ndinkagwira ntchito maola okwana 10 tsiku lililonse. Chifukwa cha zimenezi, sindinkapita ku sukulu ngati mmene ana a msinkhu wanga ankachitira. Nditakwanitsa zaka 14, ndinayamba kugwira ntchito pa fakitale ina yopanga zitsulo.

Mu 1975, ndinayamba kugwira ntchito ndi gulu la asilikali a ku Spain omwe ankakhala ku North Africa ndipo ndinkavala yunifolomu ya gululi

 Mu 1975, ndinaitanidwa kuti ndikayambe ntchito yausilikali yomwe inali yokakamiza ku Spain. Popeza kuti pa moyo wanga ndinkafunitsitsa kupita ku malo osiyanasiyana, ndinadzipereka kuti ndizikagwira ntchito ndi gulu la asilikali a ku Spain omwe ankakhala mu mzinda wotchedwa Melilla ku North Africa. Mum’zindawu munkakhala anthu a ku Spain okhaokha. Pa nthawi imeneyi, ndinayamba kugwiritsa ntchito kwambiri mankhwala osokoneza bongo komanso kumwa mowa mwauchidakwa.

 Nditasiya kugwira ntchito ndi gulu la asilikali lija, ndinabwerera ku Barcelona ndipo ndinayambitsa kagulu ka zauchifwamba. Tinkaba chilichonse chimene tachipeza. Ndiyeno tinkagulitsa zinthu zomwe tabazo kuti tipeze ndalama zogulira mankhwala osokoneza bongo. Kenako ndinayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo oopsa kwambiri komanso ena oonjezera mphamvu m’thupi. Ndinayambanso khalidwe la chiwerewere, mowa, ndi kutchova juga. Makhalidwe amenewa anandipangitsa kuti ndikhale munthu wachiwawa kwambiri. Nthawi zonse ndinkayenda ndi mpeni, nkhwangwa, kapena chikwanje, ndipo sindinkaopa kuzigwiritsa ntchito ndikaona kuti pakufunika kutero.

 Tsiku lina, kagulu kanga ka zauchifwamba ndi ineyo tinaba galimoto ndipo apolisi anayamba kutithamangitsa. Zomwe zinachitikazo zinali ngati filimu. Tinayendetsa galimotoyo mtunda wamakilomita 30 ndipo kenako apolisi anayamba kutiwombera. Kenako tinachita ngozi ndi galimotoyo ndipo tonse tinathawa kuchoka pamalowo. Bambo anga atadziwa zimenezi, anandithamangitsa pakhomo.

 Kwa zaka 5 zotsatira, misewu ndi imene inali nyumba yanga. Ndinkagona pamakomo a nyumba, m’magalimoto, m’mabenchi, komanso m’manda. Nthawi ina ndinakhala m’phanga kwa nthawi yaitali ndithu. Moyo wanga unalibe tanthauzo lililonse, ndipo ndinalibe nazo ntchito zoti ndikhala ndi moyo kapena ndifa. Ndikukumbukira kuti nthawi ina ndinadzicheka mikono chifukwa cha mankhwala osokoneza bongo. Zipsera zake ndidakali nazo mpaka pano.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA

 Ndili ndi zaka 28, mayi anga anabwera kudzandifufuza ndipo anandiuza kuti ndibwerere kunyumba. Ndinavomera kubwerera kunyumba ndipo ndinalonjeza mayi anga kuti ndisintha makhalidwe anga oipa, koma zinanditengera nthawi kuti ndikwaniritse lonjezo limeneli.

 Tsiku lina masana, a Mboni za Yehova awiri anabwera kunyumba kwathu. Pamene ndinkawamvetsera, bambo anga anakuwa kuchokera m’nyumbamo kuti ndiwatsekere a Mboniwo panja. Koma chifukwa choti sindinkakonda kuuzidwa zochita, ndimangowanyalanyaza bambowo. Anandipatsa mabuku ang’onoang’ono atatu, ndipo ndinawalandira mosangalala. Ndinawafunsa kumene amasonkhana, ndipo patatha masiku ochepa ndinapita ku Nyumba ya Ufumu.

 Chinthu choyamba chomwe ndinaona chinali choti munthu wina aliyense anavala bwino. Koma ineyo ndinali ndi tsitsi lalitali, ndevu zosasamalidwa, komanso zovala zong’ambikang’ambika. Zinkachita kuonekeratu kuti sindinali woyenera kulowa, choncho ndinakhala kunja kwa Nyumba ya Ufumuyo. Koma ndinadabwa kwambiri nditaona mmodzi mwa anthu amene ndinali nawo m’gulu la zauchifwamba lija, dzina lake Juan, atavala suti. Kenako ndinazindikira kuti iye anakhala wa Mboni za Yehova chaka chapitacho. Kupezeka kwa Juan pamalowo kunandipangitsa kuti ndilimbe mtima kulowa m’Nyumba ya Ufumuyo ndi kuchita nawo misonkhano. Apa m’pamene zinthu zinayamba kusintha pamoyo wanga.

 Kenako ndinavomera kuti ndiziphunzira Baibulo ndipo mwamsanga ndinazindikira kuti ngati ndikufuna kuti Mulungu azisangalala nane, ndikufunika kusiya kukhala munthu waukali komanso makhalidwe anga oipa. Koma sizinali zophweka kuti ndisinthe. Ndinaphunzira kuti, kuti ndikondweretse Yehova Mulungu, ndinayenera ‘kusandulika mwa kusintha maganizo anga.’ (Aroma 12:2) Chifundo cha Mulungu chinandikhudza mtima kwambiri. Ndinazindikira kuti ngakhale kuti pali zinthu zomwe ndinkalakwitsa, Mulungu ankandipatsa mwayi woti ndisinthe moyo wanga. Zimene ndinaphunzira zokhudza Yehova, zinakhazikika kwambiri mumtima mwanga. Kenako ndinazindikira kuti pali Mlengi amene amasamala za ine.—1 Petulo 5:6, 7.

 Zimenezi zinandipangitsa kuti ndiyambe kusintha. Mwachitsanzo, nthawi ina pamene ndinkaphunzira Baibulo, tinakambirana nkhani yokhudza fodya. Ndiyeno ndinadziuza kuti, ‘Ngati Yehova Mulungu akufuna kuti ndikhale woyera m’mbali iliyonse ya moyo wanga, ndiye kuti ndikuyenera kutaya ndudu za fodyazi.’ (2 Akorinto 7:1) Kenako ndinataya nduduzo m’bini.

 Ndinkafunikanso kusiya kugulitsa komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Zimenezi zinanditengera nthawi yayitali komanso khama. Kuti ndikwanitse kuchita zimenezi, ndinazindikira kuti ndinkafunika kusiya kucheza ndi anzanga akale. Zochita zawo sizinkandithandiza kuti ndipitirize kukonda Mulungu. Komabe, pamene nthawi inkadutsa, ndinayamba kudalira kwambiri Mulungu komanso thandizo la anzanga atsopano amene ndinali nawo mu mpingo. Chikondi komanso chidwi chimene ankandisonyeza zinali zinthu zomwe ndinali ndisanazionepo m’moyo wanga. Patatha miyezi ingapo, ndinasiya kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndipo ‘ndinavala umunthu watsopano,’ womwe unandithandiza kuti Mulungu azisangalala nane. (Aefeso 4:24) Mu August 1985, ndinabatizidwa monga wa Mboni za Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA

 Baibulo landithandiza kukhala ndi moyo wabwino kwambiri. Landithandiza kusiya makhalidwe amene ankawononga moyo wanga komanso kundichotsera ulemu. Ndipo anzanga oposa 30 omwe ndinkagwirizana nawo kale, anafa akadali achinyamata chifukwa cha edzi komanso matenda obwera chifukwa cha mankhwala osokoneza bongo. Ndikuyamikira kwambiri kuti chifukwa chogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo, ndinapewa kukumana ndi zinthu zoopsa zomwe anzangawa anakumana nazo.

 Panopa sindinyamulanso mipeni ndi nkhwangwa zomwe ndikayenda nazo pa nthawi imene ndinkachita zachiwawa. Sindinkalotako n’komwe kuti tsiku lina ndizidzanyamula Baibulo m’malo mwa mipeni ndi nkhwangwa. Panopa ineyo ndi mkazi wanga tikutumikira monga atumiki a nthawi zonse a Mboni za Yehova.

 Makolo anga sanakhale a Mboni za Yehova, koma anayamikira kwambiri poona mmene kuphunzira Baibulo kwandithandizira. Ndipo bambo anga ankanena zabwino zokhudza a Mboni anzawo akamanena zoipa. Bambo anga ankachita kuoneratu kuti zimene ndinayamba kukhulupirira zinapangitsa kuti ndisinthe kwambiri n’kuyamba kuchita zinthu zabwino. Kawirikawiri mayi anga ankanena kuti zikanakhala bwino ndikanaphunzira Baibulo kalekale. Nthawi zambiri sindinkagwirizana nawo pa zinthu zambiri.

 Zimene ndakumana nazo pamoyo zandiphunzitsa kuti ndi kupanda nzeru kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso kuchita makhalidwe ena oipa kuti munthu azisangalala. Panopa ndimapeza chisangalalo chenicheni chifukwa chophunzitsa anthu ena mfundo za m’Mawu a Mulungu zomwe zimapulumutsa moyo.