Pitani ku nkhani yake

Puneet Aggarwal, Delroy Williamson, Ashok Patel (pamwamba, kuyambira kumanzere kupita kumanja); Mark Sleger, Jouni Palmu, Hiroshi Aoki (pansi, kuyambira kumanzere kupita kumanja)

10 JULY, 2020
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Mabaibulo 6 Atulutsidwa Patangotha Mlungu Umodzi Mabaibulo Enanso 6 Atatulutsidwa

Mabaibulo 6 Atulutsidwa Patangotha Mlungu Umodzi Mabaibulo Enanso 6 Atatulutsidwa

Patangotha mlungu umodzi Mabaibulo okwanira 6 atatulutsidwa, a Mboni za Yehova alengezanso za kutuluka kwa Mabaibulo enanso 6. Pa 4 July, 2020, Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika linatulutsidwa mu Chibisilama komanso Chioromo. Tsiku lotsatira pa 5 July, Baibulo la Dziko Latsopano linatulutsidwa mu Chilativiya ndi Chimarathi komanso Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu linatulutsidwa mu Chibengali ndi Chikareni (S’gaw). Mabaibulowa ndi apazipangizo zamakono ndipo anatulutsidwa pankhani zochita kujambuliratu. Ofalitsa anaonera pulogalamu yapaderayi kudzera pa intaneti ndipo anasangalala kwambiri ndi mphatso zochokera kwa Yehova zimenezi.

Chibisilama

Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso linatulutsidwa m’Chibisilama ndi M’bale Mark Sleger, yemwe ali m’Komiti ya Nthambi ya ku Fiji. Ofalitsa a ku Vanuatu anamvetsera pulogalamuyi yomwe inachitika mu Chibisilama ndipo inamasuliridwanso m’chinenero chamanja cha Chibisilama.

Ntchito yokonzanso Baibuloli inatenga zaka zitatu ndipo magulu awiri a omasulira ndi omwe anagwira ntchitoyi. Womasulira wina anati: “Abale asangalala kwambiri ndi Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso chifukwa ndi losavuta kuwerenga komanso mawu amene agwiritsidwa ntchito ndi amakono, omwe anthu amagwiritsa ntchito tsiku ndi tsiku. Baibuloli litithandiza kuti tizimvetsa bwino mfundo za choonadi.”

Tikukhulupirira kuti Baibulo limeneli lithandiza ofalitsa oposa 700 omwe amalankhula Chibisilama kuti azipindula akamaphunzira paokha komanso akamalalikira.

Chioromo

M’bale Delroy Williamson, yemwe ali m’Komiti ya Nthambi ku Ethiopia, ndi amene anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano mu Chioromo. Abale ndi alongo okwana 12,548 analumikiza n’kumvetsera kapena kuonera pulogalamuyi. Nambala imeneyi ikuphatikizaponso ofalitsa okwana 2,000 omwe amalankhula Chioromo.

Chifukwa cha mavuto ena, Bungwe Lolamulira linavomereza kuti pulogalamu yomwe anajambuliratu ionetsedwe kudzera pa TV. Ofalitsa anapatsidwanso mwayi woti akhoza kulumikiza n’kumvetsera pulogalamuyi kudzera pafoni.

Omasulira okwana 5 anagwira ntchito yomasulira Baibuloli kwa zaka 5. Baibulo limeneli lithandiza kwambiri abale ndi alongo omwe amalalikira m’gawo lalikulu kwambiri la anthu olankhula Chioromo.

Chilativiya

Patadutsa zaka 12 omasulira akugwira ntchito mwakhama, Baibulo la Dziko Latsopano latulutsidwa mu Chilativiya. Mipingo yonse ya Chilativiya komanso Chirasha yomwe ili ku Latvia inauzidwa kuti ikhoza kuonera pulogalamuyi.

M’bale Jouni Palmu, yemwe ali m’Komiti ya Nthambi ya ku Finland ndi amene anakamba nkhani yotulutsa Baibuloli. Iye anati: “Ndife osangalala kutulutsa Baibulo lomveka bwino komanso losavuta kuwerenga lomwe lithandize anthu omwe amatha kuwerenga Chilativiya. Tikukhulupirira kuti Baibuloli lichititsa kuti anthu azisangalala akamaphunzira Mawu a Mulungu komanso kuganizira mozama zimene awerenga.”

Ponena za zinthu zothandiza pofufuza zomwe zili m’Baibulo latsopanoli, womasulira wina anati: “Baibulo lomwe latulukali lili ngati foni yamakono. Lili ndi chilichonse chomwe munthu angafunikire ndipo lingathandize kuti munthu azipindula kwambiri akamaphunzira payekha komanso kuti aziganizira mozama zimene akuwerenga.”

Chimarathi

Baibulo la Dziko Latsopano linatulutsidwa m’Chimarathi papulogalamu ina yomwe mipingo yonse yomwe imagwiritsa ntchito chinenerochi inamvetsera ku India. M’bale Puneet Aggarwal, yemwe ali m’Komiti ya Nthambi ku India ndi amene analengeza za kutulutsidwa kwa Baibuloli.

Omasulira okwana 6 anagwira ntchito yomasulira Baibuloli kwa zaka zitatu. Mmodzi wa omasulirawo anati: “Baibulo limeneli lithandiza makolo ndi anthu omwe amaphunzitsa anthu Baibulo kuti aziphunzitsa choonadi cha m’Baibulo mogwira mtima.”

Womasulira winanso anati: “N’zosangalatsa kwambiri kudziwa kuti Baibulo limeneli labwezeretsa dzina la Mulungu lakuti Yehova m’malo onse omwe linkapezeka m’mipukutu yoyambirira. Owerenga azitha kupeza dzina la Yehova pafupifupi tsamba lililonse. Zimenezi zichititsa kuti dzina la Yehova lipatsidwe ulemu woyenerera.”

Anthu oposa 83 miliyoni amayankhula Chimalathi m’chigawo chapakati cha dziko la India.

Chibengali

Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba a Chigiriki linatulutsidwa ndi M’bale Ashok Patel yemwe ali m’Komiti ya Nthambi ku India. Ofalitsa oposa 1,200 analumikiza n’kumvetsera pulogalamuyi ku India komanso ku Bangladesh.

Anthu oposa 265 miliyoni amalankhula Chibengali, chomwe ndi chinenero cha nambala 7 pa zinenero zomwe zimalankhulidwa ndi anthu ochuluka kwambiri padziko lonse. Pofuna kutulutsa Baibulo loti anthu ambiri asamavutike kulimva, omasulira ochokera mbali zosiyanasiyana za dziko la India komanso Bangladesh anagwira ntchito yomasulira Baibuloli kwa zaka zitatu.

Munkhani yomwe anakamba, M’bale Patel anati: “Chibengali ndi chimodzi mwa zinenero zoyambirira kukhala ndi Baibulo ku India kuno. Baibulo la Malemba a Chigiriki linatulutsidwa mu 1801. Chosangalatsa kwambiri ndi choti Baibulo limeneli linali ndi dzina la Mulungu lakuti Yehova. Komabe, Mabaibulo ambiri omwe atuluka pakatipa anachotsa dzina limeneli n’kuikamo dzina la udindo lakuti ‘Ambuye.’ Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba a Chigiriki lithandiza kwambiri chifukwa ndi lolondola komanso lomveka bwino.”

Mmodzi wa anthu amene anamasulira nawo Baibuloli anati: “Baibulo limeneli ndi umboni wakuti Yehova Mulungu amakonda anthu a mitundu yonse ndiponso amafuna kuti aphunzire zokhudza iye ndi mwana wake, Yesu Khristu.”

Chikareni (S’gaw)

M’bale Hiroshi Aoki, yemwe ali m’Komiti ya Nthambi ya ku Myanmar, ndi amene anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba a Chigiriki mu Chikareni (S’gaw). Anthu 510 ochokera m’mipingo yokwana 6 komanso timagulu 4 analumikizidwa papulogalamuyi.

Ntchito yomasulira Baibulo mu Chikareni (S’gaw) inatenga chaka chimodzi chokha. Mmodzi wa omasulira Baibuloli anati: “Abale ndi alongo komanso anthu omwe timawalalikira asangalala kwambiri kuwerenga Baibulo mu Chikareni (S’gaw) chifukwa labwezeretsa dzina la Yehova komanso lagwiritsa ntchito mawu amakono. Baibuloli ndi lomveka bwino komanso lolondola. Tikuthokoza Yehova chifukwa cha mphatso ya m’chinenero chomwe timachimva bwino imene itithandiza kumuyandikira.”

Womasulira winanso anati: “Baibulo la Dziko Latsopano lagwiritsa ntchito mawu omwe anthu amagwiritsa ntchito tsiku ndi tsiku, choncho lingathandize owerenga kumvetsa mmene anthu otchulidwa m’Baibulo ankamvera. Lingawathandizenso kumayerekezera zimene zinkawachitikira anthuwo komanso kutsanzira chikhulupiriro chawo.”

Tikusangalala kwambiri limodzi ndi abale komanso alongo athu omwe alandira Mabaibulo amenewa. Sitikukayikira kuti Mabaibulowa awathandiza kuyandikira Yehova komanso kuti asamavutike akamathandiza anthu ena kudziwa choonadi.—Yohane 17:17.