DECEMBER 2, 2020
NKHANI ZA PADZIKO LONSE
Mphepo Yamkuntho Yotchedwa Iota Yasakaza ku Colombia Komanso ku Central America ndi ku Mexico
Malo
Central America, Colombia ndi Mexico
Ngozi yake
Pa 15 ndi 16 November 2020, mphepo yamkuntho yotchedwa Iota yomwe inali yamphamvu kwambiri inawononga m’madera akumpoto kwa Colombia, makamaka m’zilumba za San Andrés ndi Providencia ku Nyanja Yaikulu ya Caribbean
Mphepoyi inachititsa kuti kugwe chimvula champhamvu komanso nthaka inagumuka
Pa 16 November 2020, mphepo yamkuntho ya Iota inawomba ku Nicaragua kenako inafikanso m’madera ena a ku Central America. Mphepoyi inachititsa kuti zinthu zambiri ziwonongeke chifukwa chakumayambiriro kwa mweziwu, m’maderawa munawombanso mphepo ina yamkuntho yotchedwa Eta
Mmene ngoziyi yakhudzira abale ndi alongo athu
Central America
Costa Rica
Ofalitsa 22 anafunika kuchoka m’nyumba zawo
Guatemala
Ofalitsa 93 anafunika kuchoka m’nyumba zawo
Honduras
Ofalitsa 1,531 anafunika kuchoka m’nyumba zawo
Ofalitsa awiri anavulala pang’ono
Nicaragua
Ofalitsa 75 anafunika kuchoka m’nyumba zawo
Panama
Ofalitsa 16 anafunika kuchoka m’nyumba zawo
Colombia
Wofalitsa mmodzi wa ku Providencia anathyoka mkono
Wofalitsa mmodzi wa ku San Andrés anavulala pang’ono
Mexico
Ofalitsa 1,248 anachoka m’nyumba zawo m’madera a Tabasco ndi Veracruz
Katundu yemwe wawonongeka
Central America
Costa Rica
Nyumba 9 zinawonongeka
Guatemala
Nyumba 18 zinawonongeka
Nyumba za Ufumu 7 zinawonongeka pang’ono
Nyumba za Ufumu ziwiri zinawonongeka kwambiri
Honduras
Nyumba za Ufumu 7 zinawonongeka pang’ono
Nyumba 227 zinawonongeka
Nicaragua
Nyumba 106 zinawonongeka
Nyumba za Ufumu zitatu zinawonongeka pang’ono
Panama
Nyumba 5 zinawonongeka
Nyumba za Ufumu ziwiri zinawonongeka kwambiri
Colombia
Malipoti oyambirira akusonyeza kuti nyumba za abale zambiri zinawonongeka kwambiri ku Providencia komanso Nyumba ya Ufumu imodzi inagweratu. Panopa zikumavuta kulumikizana ndi abale ndi alongo omwe amakhala pazilumbazi chifukwa choti mawaya a magetsi ndi a telefoni anaduka
Nyumba 20 komanso Nyumba ya Ufumu imodzi ku San Andrés zinawonongeka pang’ono
Mexico
Nyumba 184 zinawonongeka
Ntchito yothandiza anthu
Komiti ya Nthambi ku Colombia yakhazikitsa Komiti Yothandiza pa Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi kuti igwire ntchito yothandiza ofalitsa. Komitiyi ikugwira ntchito limodzi ndi woyang’anira dera m’chigawochi popereka zinthu zofunika komanso kulimbikitsa abale ndi alongo ndi mfundo za m’Baibulo
Ofesi ya Nthambi ya Central America inakhazikitsa makomiti 4 othandiza pa ngozi zogwa mwadzidzidzi kuti athandize abale ndi alongo omwe anakhudzidwa ndi mphepo ya Eta ndiponso ya lota ku Central America ndi ku Mexico. Oyang’anira madera akulimbikitsa komanso kupereka zinthu zofunika ku mabanja okhudzidwa. Komanso, mipingo ya kumeneko yapereka maphukusi oposa 400 a chakudya kuti chithandize abale ndi alongo a ku Honduras ndi ku Nicaragua. Abale ndi alongo ena omwe anachoka m’nyumba zawo akukhala m’nyumba za a Mboni amene ali m’madera omwe sanakhudzidwe ndi mphepozi
Abale ndi alongo omwe akugwira nawo ntchito yothandiza anthu okhudzidwa akuyesetsa kutsatira malangizo opewera mliri wa COVID-19 n’cholinga choti akhale otetezeka pogwira ntchitoyi
Ngakhale kuti sizingatheke kuti abale ndi alongo athuwa apeweretu kukumana ndi mavuto osiyanasiyana m’dzikoli kuphatikizapo omwe amabwera chifukwa cha ngozi zam’chilengedwe, iwo sakukayikira kuti Yehova Mulungu wathu awathandiza ndipo akhala malo awo achitetezo.—Salimo 142:5.