Pitani ku nkhani yake

19 OCTOBER, 2016
ERITREA

Kwa Nthawi Yoyamba Mayiko Ambiri Asonyeza Kuti Sakugwirizana ndi Nkhanza Zimene Dziko la Eritrea Likuchitira a Mboni za Yehova

Kwa Nthawi Yoyamba Mayiko Ambiri Asonyeza Kuti Sakugwirizana ndi Nkhanza Zimene Dziko la Eritrea Likuchitira a Mboni za Yehova

Dziko la Eritrea likuzunza a Mboni za Yehova kuposa mmene zilili m’mayiko ena onse padziko lapansi. Kungoyambira pomwe dziko la Eritrea linalandira ufulu wodzilamulira mu 1993, a Mboni akhala akuponyedwa m’ndende, kuzunzidwa komanso kuonedwa ngati osafunika m’dzikolo. A Mboniwa amazunzidwa chifukwa chokana kulowerera nkhani za ndale komanso kulowa usilikali.

Panopa a Mboni za Yehova okwana 54 ali m’ndende ku Eritrea. Pa zaka 22 zapitazi, ndi mlandu wa munthu mmodzi yekha womwe unaweruzidwapo ndipo ena onsewo anamangidwa pazifukwa zosamveka komanso nkhani zawo sizinafike kukhoti. Atatu mwa anthuwa, anamangidwa mu 1994 chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira.

Mayiko Ambiri Akupitiriza Kudzudzula Zimene Boma la Eritrea Likuchita

Kuchokera nthawi imene a Mboni anayamba kuzunzidwa, mabungwe omenyera anthu ufulu komanso mabungwe omwe amagwira ntchito limodzi ndi boma, akhala akudzudzula nkhanza zimene boma la Eritrea likuchitira a Mboni za Yehova. Chaposachedwa, bungwe la United Nations linakhazikitsa gulu loti lifufuze mmene boma la Eritrea likuchitira pa nkhani za ufulu wa anthu. Gululi linapeza kuti boma la Eritrea limachitira nkhanza a Mboni komwe ndi kuphwanya ufulu wa anthu. Lipoti loyamba lomwe gululi linapereka ku Nthambi ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu mu 2015, linali ndi mbali ina yapadera yofotokoza za nkhanza zomwe boma la Eritrea likuchitira a Mboni.

Pa 21 June 2016, gulu lija linaperekanso lipoti lake lina ku Nthambi ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu. Gululi linapempha boma la Eritrea kuti liyambe “kulemekeza ufulu wachipembedzo kapena wa zinthu zomwe munthu amakhulupirira.” Linapemphanso kuti bomalo lisiye kumanga anthu popanda chifukwa, mwachitsanzo kuwamanga chifukwa cha zikhulupiriro za chipembedzo chawo ngati mmene likuchitira ndi a Mboni za Yehova. Gululi linanenanso kuti amasule mwamsanga anthu omwe linawamanga mosagwirizana ndi malamulo komanso popanda zifukwa.

Mogwirizana ndi zimene linapeza, gululi linamaliza ndi kuuza boma la Eritrea kuti “kumanga munthu pa zifukwa za chipembedzo kapena mtundu wake,” n’kosemphana ndi malamulo omwe mayiko anakhazikitsa ndipo kuchita zimenezi ndi “mlandu wophwanya ufulu wa anthu.” Mayiko ambiri akuona kuti boma la Eritrea likulakwa kwambiri kuphwanyira a Mboni za Yehova ufulu wawo. Gulu lofufuza lija likuyembekezeka kudzapereka zonse zomwe linapeza pa Msonkhano Waukulu wa bungwe la United Nations womwe udzachitike pa 27 October 2016.

Kodi Dziko la Eritrea Lidzasiya Kuchitira Nkhanza a Mboni?

A Mboni za Yehova padziko lonse lapansi akudera nkhawa a Mboni anzawo a ku Eritrea. Akupempha kuchokera pansi pa mtima kuti boma la Eritrea lisiye kuzunza Akhristu osalakwa komanso kuti awalole kusangalala ndi ufulu wawo.