Pitani ku nkhani yake

AUGUST 25, 2023
MALAWI

Baibulo la Dziko Latsopano Lokonzedwanso Latulutsidwa mu Chichewa

Baibulo la Dziko Latsopano Lokonzedwanso Latulutsidwa mu Chichewa

Pa 18 August 2023, M’bale Kenneth Cook, Jr., wa m’Bungwe Lolamulira anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika mu Chichewa. Baibuloli linatulutsidwa pa tsiku loyamba la Msonkhano Wachigawo wa 2023 wakuti, “Khalani Oleza Mtima” womwe unachitikira pa Malo a Msonkhano a Lilongwe ku Malawi. Anthu omwe anapezeka pamsonkhanowu analandira Mabaibulo osindikizidwa. Komanso anali ndi mwayi wopanga dawunilodi Baibulo la pazipangizo zamakono polumikiza ku JW Box.

Nkhani ya kutulutsidwa kwa Baibuloli inalumikizidwanso kusitediyamu ya m’chigawo chapakati, m’chigawo chakum’mwera komanso m’malo angapo a misonkhano a m’madera a kumidzi ndiponso pafupifupi ku Nyumba za Ufumu zonse za ku Malawi, kudzera pa Tchanelo cha JW cha pa Setilaiti. Kuwonjezera apo, nkhaniyi inalumikizidwanso ku Nyumba za Ufumu zina za ku Mozambique komwe anthu ake amalankhula Chichewa. Anthu 77,112 omwe anasonkhana kumasitediyamu awiriwa komanso kumalo a misonkhano a m’madera a kumidzi, kuphatikizapo anthu enanso masauzande omwe anasonkhana mu Nyumba za Ufumu, anamvetsera nkhani ya kutulutsidwa kwa Baibuloli.

Chichewa ndi chilankhulo chomwe anthu ambiri amalankhula ku Malawi ndipo chimalankhulidwa ndi anthu a m’dzikoli oposa 10 miliyoni. Anthu a m’mayiko ena monga Mozambique, South Africa, Zambia ndi Zimbabwe amalankhulanso chilankhulochi. Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba a Chigiriki linatulutsidwa mu Chichewa mu 2006, ndipo Baibulo lathunthu linatulutsidwa mu 2010. Abale ndi alongo ndi osangalala kwambiri kuti tsopano ali ndi Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lokonzedwanso mu Chichewa.

Pofotokozapo za Baibuloli, wofalitsa wina ananena kuti: “Anthu ambiri olankhula Chichewa omwe timawalalikira, ali ndi Mabaibulo omwe Chichewa chake n’chachikale. Tikawapempha kuti awerenge lemba linalake m’Baibulo lawo, nthawi zambiri amavutika kumvetsa zomwe awerenga. Pomwe Baibulo la Dziko Latsopano ndi losavuta kumvetsa. Ndikungoona kuchedwa kuti ndikayambe kuligwiritsa ntchito mu utumiki.”

Tikukhulupirira kuti Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lokonzedwansoli, lithandiza abale ndi alongo athu komanso anthu ena achidwi olankhula Chichewa, kuti ‘azikonda kwambiri chilamulo cha Yehova.’​—Salmo 1:2.