Pitani ku nkhani yake

Maofesi omasulira mabuku ndi nyumba zogonamo zatsopano zayamba kugwira ntchito ku Mexico. Kumanzere: Ofesi ya Chitsotsilu. Kumanja pamwamba: Ofesi ya Chizapoteki (cha ku Isthmus). Kumanja mmunsi: Ofesi ya Chiotomi (cha ku Mezquital Valley)

31 AUGUST, 2022
MEXICO

Tsopano ku Central America Kuli Maofesi Omasulira Mabuku Okwana 25

Tsopano ku Central America Kuli Maofesi Omasulira Mabuku Okwana 25

Maofesi omasulira mabuku (RTO) atsopano okwana 5, anayamba kugwira ntchito ku Mexico kuyambira mwezi wa January mpaka July 2022. Tsopano, ndiye kuti m’gawo la nthambi ya Central America muli maofesi omasulira mabuku okwana 25. Maofesiwa athandiza kuti anthu ogwira ntchito yomasulira mabuku mu Chitarasikani, Chitsotsilu, Chizapoteki (cha ku Isthmus), Chiotomi (cha ku Mezquital Valley) ndi Chicholi, azikakhala m’madera amene anthu ambiri amalankhula zilankhulozi. M’miyezi ikubwerayi, maofesi ena omasulira mabuku okwana 8 akuyembekezeka kutsegulidwa m’gawo la nthambi ya Central America. Panopo abale ali mkati mokonza mapulani omanga maofesi enanso okwana 34.

Pamakhala ubwino waukulu ngati ogwira ntchito yomasulira, akugwirira ntchito yawo m’dera limene anthu ambiri amalankhula chilankhulo chomwe akumasuliracho. Mlongo Marcela Hernández amene amamasulira mabuku m’Chitsotsilu, amenenso anatumikirapo pa ofesi ya nthambi kwa zaka zingapo ananena kuti: “Ndili ku nthambi, ndinayamba kuona kuti ziganizo zomwe ndikulankhula zikumakhala zosamveka bwinobwino. Koma panopo, ndikamamva abale akumpingo akulankhula komanso kulalikira, zimandithandiza kuti ndizimasulira zinthu zomveka bwino.”

Maofesi omasulirawa omwe akumangidwa mwamakono, akuchititsa chidwi anthu a m’deralo chifukwa akumaoneka okongola komanso aukhondo. Ndipo sizachilendo kuona anthu ataima n’kumayang’anitsitsa maofesiwa ngakhale kujambula zithunzi kumene. Mayi wina amene ali ndi shopu yaing’ono m’mbali mwa msewu wochokera ku ofesi yathu ina yomasulira mabuku, anachita chidwi kwambiri atamva za ntchito yomwe imagwiridwa pamalowa ndipo nayenso anayamba kusesa msewu wapafupi ndi shopuyo komanso kusamalira bwino shopu yake. Mayiyo ananena kuti: “Ndimakhala m’mbali mwa msewu wopita kunyumba ya Mulungu.”

N’zoonekeratu kuti Yehova wadalitsa khama lomwe lakhalapo pomanga maofesiwa. Tikumuthokoza kwambiri chifukwa cha mmene ntchito yomasulira mabuku ikuyendera.—Salimo 127:1.