Pitani ku nkhani yake

AUGUST 8, 2019
NETHERLANDS

Zokhudza Msonkhano Wamayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Utrecht, Netherlands

Zokhudza Msonkhano Wamayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Utrecht, Netherlands
  • Masiku: 2 mpaka 4 August, 2019

  • Malo: Jaarbeurs Hallencomplex, Utrecht, Netherlands

  • Zinenero: Chiarabu, Chidatchi, Chinenero Chamanja cha ku Netherlands, Chingelezi, Chipapiamento, Chipolishi, Chipwitikizi, Chisipanishi, Chitwi

  • Chiwerengero cha Osonkhana: 42,335

  • Chiwerengero cha Obatizidwa: 212

  • Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 6,000

  • Nthambi Zoitanidwa: Australasia, Belgium, Brazil, Canada, Colombia, Indonesia, Korea, Portugal, Romania, South Africa, Suriname, ndi United States

  • Zina Zomwe Zinachitika: M’bale wina amagwira ntchito ku kampani ina yoyeretsa malo ndipo kampaniyo inapeza ntchito yoyeretsa malo a Jaarbeurs Hallencomplex. M’baleyo analandira foni kuchokera kwa abwana ake ndipo anamuuza kuti: “Tsopano tili ndi gulu la anthu omwe akuchita zonse zomwe tinagwirizana ndipo akuzichita pa nthawi yake. Akuyeretsa malowa ndipo apanga dongosolo lawo loyeretsera kuti pasapezeke pena paliponse posayeretsedwa. Sitikukayika kuti malowa awasiya ali abwino kwambiri kuposa mmene analili pamene tinkawapatsa kuti ayambe kuwagwiritsa ntchito. N’zochititsa chidwi kwabasi! Zimenezi sindinazionepo. Ayeretsa ngakhale mbali ina ya lesitilanti yomwe panopa sikugwiritsidwa ntchito. Nthawi zonse kuzimbudzi kukumakhala anthu awiri omwe akumathandiza anthu, ndipo ngati penapake pali vuto, nthawi yomweyo anthu amabwera kudzakonza. Sindinaonepo zimenezi zikuchitika.”

 

Abale ndi alongo a ku Netherlands akulandira alendo ochokera kumayiko ena

Atumiki a pa Beteli akulandira alendo omwe abwera kudzaona nthambi ya Netherlands

Mlongo wochokera kudziko lina akugwira ntchito yoitanira anthu kumsonkhano limodzi ndi mlongo wa ku Netherlands

Abale ndi alongo akumvetsera msonkhano mu holo yaikulu ya Jaarbeurs Hallencomplex. Abale ndi alongo ena anaonera msonkhanowu m’maholo enanso 5 a pamalopa

Ena mwa abale ndi alongo 212 atsopano akubatizidwa

Abale ndi alongo akumvetsera nkhani ndiponso akulemba notsi

Alendo ochokera kumayiko ena akupatsana mphatso

M’bale Geoffrey Jackson wa m’Bungwe Lolamulira, akukamba nkhani yomaliza pa tsiku Lamlungu

Amishonale ndiponso atumiki ena anthawi zonse akubayibitsa anthu pamapeto pa msonkhano